Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Akufa Angathandize Amoyo?

Kodi Akufa Angathandize Amoyo?

Kodi Akufa Angathandize Amoyo?

MNYAMATA wina wa ku West Africa, dzina lake Tamba, * atatsala pang’ono kulemba mayeso, mayi ake anamuuza kuti apemphe mizimu ya makolo kuti imuthandize kupambana mayesowo. Mumzinda wa Palermo, ku Sicily, muli manda enaake amene anawamanga m’njira yoti mitembo izionekera. Mitemboyo anaikonza kuti isawonongeke ndipo alendo amabwera kudzaona pokhulupirira kuti ingawathandize. Anthu ambiri ku Africa amayesetsa kuchita zinthu zosangalatsa mizimu ya makolo n’cholinga choti iziwathandiza. Ena amapereka nsembe kwa mizimuyo kuti iwabweretsere mvula ndiponso kuti iwachiritse matenda.

Padziko lonse anthu akupitirizabe kukhulupirira kuti mizimu ya anthu akufa ingawathandize. Kodi inuyo maganizo anu ndi otani pankhaniyi? Mwina mumakhulupirira kuti mizimu ya anthu akufa imathandiza anthu amoyo kapena mumakhala limodzi ndi anthu amene amakhulupirira zimenezi. Kunena zoona, aliyense amafuna ataonananso ndi achibale kapena anzake amene anamwalira. Ndipo asing’anga amizimu amauza anthu kuti amathandiza kulankhulana ndi anthu akufa. Mwachitsanzo, magazini ya Time inalemba zimene sing’anga wina ananena kuti mizimu “imakhala yokonzeka kuthandiza anthu ngati ataipempha.” Koma kodi zimenezi ndi zoona? Kodi anthu akufa angathandizedi amoyo? Taonani zimene Baibulo limaphunzitsa pankhaniyi.

Kodi Akufa Amakhala ndi Moyo Kwinakwake?

Baibulo limanena momveka bwino mmene akufa alili. Taonani zimene lemba la Mlaliki 9:5 limanena: “Amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi.” Kodi anthu akufa amaganiza? Vesi 6 limayankha kuti: “Chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano; ndipo nthawi yamuyaya sagawa konse kanthu kali konse kachitidwa pansi pano.” Onaninso kuti vesi 10 la chaputalachi limati, “mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.” N’zochititsa chidwi kuti Malemba Achigiriki Achikhristu amanenanso kuti Yesu Khristu atamwalira, anaikidwa m’manda.​—Machitidwe 2:31.

Nthawi imene Yesu anali padziko lapansi, anathandiza anthu ambiri koma iye ankadziwa kuti adzafa. Koma kodi iye ankayembekezera kuti akadzamwalira adzapitirizabe kuthandiza anthu? Ayi. Yesu anayerekezera imfa yake ndi usiku womwe n’zosatheka kugwira ntchito. (Yohane 9:4) Yesu ankadziwa bwino kuti munthu akafa ‘sakhalanso ndi moyo.’​—Yesaya 26:14.

Pofuna kumveketsa bwino mfundo imeneyi, Yesu anayerekezera imfa ndi chinthu china. Lazaro atamwalira, Yesu anayerekezera imfa ndi tulo. (Yohane 11:11-13) Zimenezitu n’zomveka chifukwa sitiyembekezera kuti munthu amene ali mtulo atithandize chifukwa samadziwa chilichonse.

Kodi Pali Chinachake Chimene Chimakhalabe ndi Moyo Munthu Akafa?

Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu anaika mwa anthu ndi nyama mphamvu yamoyo, kapena kuti mzimu, yomwe imagwira ntchito mothandizidwa ndi kupuma. Mphamvu imeneyi ndi yomwe imachititsa kuti thupi likhale ndi moyo. Komabe, nyama ndiponso munthu akasiya kupuma, mphamvu yamoyo imene Mulungu anaiika ija siigwiranso ntchito ndipo amafa. Zikatere, nyama kapena munthuyo sadziwa chilichonse.​—Genesis 3:19; Mlaliki 3:19-21; 9:5.

Komabe, mwina mungadzifunse kuti, ‘Nanga bwanji anthu ambiri amanena kuti anaonapo kapena kulankhulana ndi anthu akufa?’ Nkhani zimenezi n’zofala kwambiri padziko lonse. Nkhanizi zimachititsa anthu amene achibale kapena anzawo anamwalira kukhulupirira kuti ali ndi moyo kwinakwake ndipo zimapangitsa anthu ambiri kupita kwa asing’anga amene amati amalankhula ndi akufa.

Kodi nkhanizi zimakhala zoona? Ngati n’zoona, kodi zikugwirizana ndi zimene Baibulo limanena pankhani ya anthu akufa? Khristu Yesu ananena kuti Mawu a Mulungu ndi choonadi. (Yohane 17:17) Ndipo choonadi sichitsutsana. Komanso, m’Baibulo muli malangizo omveka bwino okhudza mmene tiyenera kuonera zimene anthu ena amanena kuti akufa angathandize anthu amoyo. Baibulo limatiuza za munthu winawake amene anapempha munthu wakufa kuti amuthandize. Kuwerenga nkhani imeneyi mofatsa kutithandiza kudziwa zoona zenizeni.

Mfumu Sauli Anapempha Kuti Akufa Amuthandize

Nthawi ina kumpoto kwa dziko la Isiraeli kunali nkhondo pakati pa asilikali oopsa a Afilisiti ndi Mfumu Sauli ndi asilikali ake. Sauli ataona gulu la asilikali la Afilisiti “anaopa, ndi mtima wake unanjenjemera kwakukulu.” Panthawi yovuta ya ulamuliro wake imeneyi, Sauli anali atasiya kulambira Mulungu woona. Ndipo chifukwa cha zimenezi, Yehova anasiya kuyankha mapemphero ake. Zitatero, kodi Sauli anatani pofuna kuti athandizidwe popeza kuti Samueli, yemwe anali mneneri wa Mulungu, anali atamwalira?​—1 Samueli 28:3, 5, 6.

Sauli anapita kukawombeza kwa sing’anga wa ku Endori. Iye anapempha sing’angayo kuti ‘amuukitsire Samueli.’ Sing’angayo anabweretsa mzukwa wooneka ngati Samueli. Mzukwawo unauza Sauli kuti Afilisiti adzagonjetsa Aisiraeli ndiponso kuti Sauli ndi ana ake adzafa kunkhondo. (1 Samueli 28:7-19) Koma kodi mzukwawo unalidi Samueli?

Taganizirani izi: Baibulo limanena kuti munthu akamwalira ‘amabwerera kumka ku nthaka yake,’ ndiponso “zotsimikiza mtima zake zitayika.” (Salmo 146:4) Sauli ndiponso Samueli ankadziwa kuti Mulungu amadana ndi okhulupirira mizimu. N’chifukwa chake Sauli asanayambe kukhulupirira mizimu, anagwira ntchito yaikulu yothana ndi kulambira mizimu.​—Levitiko 19:31.

Taganizirani bwinobwino nkhaniyi. Zikanakhala kuti Samueli anali moyo kwinakwake ngati mzimu, kodi akanalolera kuswa lamulo la Mulungu pogwirizana ndi sing’anga n’cholinga choti alankhule ndi Sauli? Yehova anali atakana kulankhula ndi Sauli. Ndiyeno kodi sing’anga angakakamize Mulungu, amene ndi Wamphamvuyonse kuti alankhule ndi Sauli kudzera mwa Samueli? Ayi. Apatu n’zachidziwikire kuti mzukwawo sunali Samueli, yemwe anali mtumiki wokhulupirika wa Mulungu. Koma chinali chiwanda chimene chinanamizira kuti chinali Samueli amene anamwalira kale.

Ziwanda ndi angelo amene anagalukira Mulungu kalekale munthu atangolengedwa kumene. (Genesis 6:1-4; Yuda 6) Ziwanda zimenezi zimadziwa zimene munthu ankachita pamoyo wake, mmene ankalankhulira ndiponso mmene ankaonekera. Cholinga chawo n’kulimbikitsa mfundo yotsutsana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. N’chifukwa chake Baibulo limatichenjeza kuti sitiyenera kulankhula ndi mizimu. (Deuteronomo 18:10-12) Masiku ano mizimu yoipa ikupitirizabe kusocheretsa anthu.

Tsopano tadziwa chifukwa chake anthu ena amati “aona” kapena “amva” mawu a abale awo omwe anamwalira. Ngakhale kuti mizimu imeneyi nthawi zina ingaoneke ngati yabwino, cholinga chawo ndi kupusitsa anthu basi. * (Aefeso 6:12) Komanso taganizira mfundo iyi: Yehova Mulungu amatikonda kwambiri. Zikanakhala kuti akufa amakhala ndi moyo kwinakwake ndipo angathandize achibale kapena anzawo, kodi Mlengi wathu yemwe ndi wachikondi akanatiletsa kuti tisamalankhule nawo? Ndiponso kodi Yehova akananena kuti ‘amanyansidwa’ ndi zimenezi? Ayi sakanachita zimenezo. (1 Petulo 5:7) Ndiyeno kodi pali winawake amene angatithandize?

Mulungu ndi Amene Angathandizedi Anthu Amoyo Komanso Akufa

Zimene takambiranazi zikutithandiza kumvetsa mfundo yakuti akufa sangathandize anthu amoyo. Ndiponso zimene munthu angachite pofuna kuti athandizidwe ndi anthu akufa n’zongotayitsa nthawi ndipo n’zoopsa kwambiri. Zili choncho chifukwa kuchita zimenezi n’kuphwanya malamulo a Mulungu ndipo zingachititse kuti ziwanda zizitilamulira.

Baibulo limatiuza kuti Mlengi wathu, Yehova, ndi amene angatithandizedi. Iye angatipulumutse ngakhale ku imfa imene. (Salmo 33:19, 20) Ngakhale masiku ano, Yehova ndi wokonzeka kutithandiza. Iye amatipatsa chiyembekezo chenicheni ndipo zimenezi n’zosiyana ndi zimene asing’anga amizimu amalonjeza anthu.

Tamba, amene tamutchula kumayambiriro uja, anazindikira kuti pali kusiyana pakati pa malonjezo abodza amene asing’anga amapereka ndi mfundo za choonadi zimene Yehova amatipatsa. Asing’anga ananena kuti ngati sapereka nsembe kwa mizimu yamakolo ndiye kuti alephera mayeso. Panthawiyi Tamba anali akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo anali atadziwa mmene akufa alili komanso kuopsa kwa mizimu yoipa imene imanamizira kuti ndi anthu akufa. Ngakhale kuti mayi ake ankamukakamiza kuti asing’anga amizimu amuthandize, iye anakana ndipo anawauza kuti, “Ngati ndingalephere mayesowa, chaka chamawa ndidzalimbikira kuti ndidzakhonze.”

Ndiyeno kodi mayeso anayenda bwanji? Anamuyendera bwino kwambiri chifukwa anakhoza kuposa anzake onse. Mayi ake anadabwa kwambiri ndi zimenezi ndipo anasiya kukhulupirira asing’anga amizimu komanso anasiya kumulimbikitsa kuchita zinthu zokhulupirira mizimu. Tamba anaphunzira kuti Yehova amafuna kuti tizipewa ‘kufunsira kwa akufa.’ (Yesaya 8:19) Iye ataphunzira Baibulo, anayamba kukhulupirira kuti akamakonda kwambiri malamulo a Mulungu, zinthu zizimuyendera bwino.​—Salmo 1:1-3.

Nanga bwanji anthu amene anamwalira? Kodi pali chiyembekezo choti tsiku lina tidzawaonanso? Inde, chifukwa kuwonjezera pa kuthandiza anthu amoyofe, Yehova walonjeza kuti adzathandiza anthu amene ali m’manda. Mneneri Yesaya atafotokoza kuti anthu akufa sangatithandize, ananena mawu otsatirawa omwe ali m’chaputala 26, vesi 19 kuti: “Akufa anu adzakhala ndi moyo. . . . Ukani muyimbe, inu amene mukhala m’fumbi.” Ulosiwu umapitiriza kuti “dziko lapansi lidzatulutsa” anthu amene anafa.

Tangoganizirani mmene zinthu zidzakhalire. Anthu osawerengeka omwe ali m’manda adzauka. Ndipotu Baibulo limanena kuti Yehova ‘amakhumba’ kuukitsa anthu amene anamwalira. (Yobu 14:14, 15) Koma kodi malonjezo amenewa adzakwaniritsidwadi? Inde, chifukwa Yesu Khristu ankakhulupirira kuti akufa adzauka ndipo anachita kunena kuti Yehova amaona kuti kwa iyeyo, akufa ali moyo.​—Luka 20:37, 38.

Kodi nanunso mumafuna kukhala ndi chiyembekezo chimenechi? * Pitirizani kuphunzira choonadi chimene chimapezeka m’Baibulo. Mukamaphunzira, mudzakhulupirira kuti Yehova angakuthandizeni komanso angathandize akufa. Ndipotu malonjezo ake “ndi odalirika ndi oona.”​—Chivumbulutso 21:4, 5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Tasintha dzinali.

^ ndime 18 Ngati mukufuna kudziwa zambiri pankhani imeneyi, onani kabuku kakuti Mizimu ya Akufa​—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? Kabukuka n’kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 26 Kuti mudziwe zambiri pa zimene Baibulo limalonjeza kuti akufa adzauka, onani mutu 7 wa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 19]

Aliyense amafuna ataonananso ndi achibale kapena anzake amene anamwalira

[Chithunzi patsamba 20]

Kodi mneneri Samueli anaukadi kwa akufa kuti alankhulane ndi Mfumu Sauli?