Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi mtumwi Paulo anadutsa msewu uti paulendo wake woyamba wa ku Roma?

Lemba la Machitidwe 28:13-16 limanena kuti ngalawa imene Paulo anakwera popita ku Italiya inafika mumzinda wa Potiyolo (womwe masiku ano umatchedwa Pozzuoli), womwe uli padoko la Naples. Kenako iye anapita ku Roma podutsa mumsewu waukulu wa mumzindawo wotchedwa Appia.

Dzina la msewu umenewu, lakuti Appia, linachokera kwa mkulu wina wa boma la Roma wotchedwa Appius Claudius Caecus, yemwe anayamba kumanga msewuwu m’chaka cha 312 B.C.E. Msewu umenewu, womwe ndi wotambalala mamita 5 mpaka 6 ndipo unamangidwa ndi miyala ikuluikulu yolimba kwambiri, ndi wautali makilomita 583 kuchokera ku Roma kupita kudera la kumwera chakummawa kwa dzikoli. Msewuwu umalumikiza dziko la Roma ndi doko la Brundisiuma (lomwe masiku ano limatchedwa Brindisi). Padokoli m’pamene anthu amadutsa popita kudera la kum’mawa. Anthu apaulendo ankapumira ulendo wawo m’malo osiyanasiyana omwe anali otalikirana makilomita pafupifupi 24 kuti agule zinthu zina ndi zina, agone, asinthe mahatchi kapena asinthe ngolo.

Paulo anayenda mumsewu wa Appia popita ku Roma ndipo unali ulendo wa makilomita 212. Zikuoneka kuti paulendowu, iye anayenda wapansi. Msewu umenewu unadutsa m’dera la zithaphwi la Pontine, ndipo munthu wina wolemba mabuku wa ku Roma anadandaula kuti derali linali lonunkha ndiponso la udzudzu kwambiri. Chakumpoto kwa dera la zithaphwili, kunali Msika wa Apiyo, womwe unali pamtunda wa makilomita 65 kuchokera ku Roma ndiponso Nyumba Zitatu za Alendo zomwe zinali pamtunda wa makilomita 50 kuchokera mumzindawo. Pamalo awiri amenewa, omwe anthu apaulendo ankapumira ulendo wawo, Akhristu a ku Roma anabwera kudzachingamira Paulo. Atawaona, iye “anayamika Mulungu, nalimba mtima.”​—Machitidwe 28:15.

Kodi cholembapo chathabwa chotchulidwa pa Luka 1:63 chinali chiyani?

Uthenga Wabwino wa Luka umanena kuti anzake a Zekariya anam’funsa kuti anene dzina limene am’patse mwana wake yemwe anali atangobadwa kumene. Zekariya “anapempha cholembapo chathabwa ndipo analemba kuti: ‘Dzina lake ndi Yohane.’” (Luka 1:63) Zolembapo zoterezi zinali zopangidwa ndi timatabwa tomwe ankatilumikiza pamodzi kenako n’kupaka phula la njuchi pamwamba pake kuti pakhale posalala. Kenako, munthu ankatha kulembapo pogwiritsa ntchito kathabwa kosongoka. Komanso anthu ankatha kufufuta zomwe alembazo kuti alembepo zina.

Buku lina linati: “Zojambula za ku Pompeii, ziboliboli zochokera m’madera osiyanasiyana m’dziko la Roma ndiponso zinthu zina zimene zinafukulidwa m’madera osiyanasiyana ku Egypt mpaka ku Hadrian’s Wall [kumpoto kwa dziko la Britain], zimasonyeza kuti anthu ankagwiritsa ntchito kwambiri zolembapo za matabwa zimenezi.” (Reading and Writing in the Time of Jesus) Anthu monga ochita malonda, ogwira ntchito za boma ndipo mwinanso Akhristu a m’nthawi ya atumwi, ankagwiritsa ntchito zolembapo zoterezi.

[Chithunzi patsamba 11]

Msewu wa Appia

[Chithunzi patsamba 11]

Thabwa Lolembapo la Mwana wa Sukulu la m’ma 100 C.E.

[Mawu a Chithunzi]

By permission of the British Library