Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Maganizo a Mulungu Pankhani ya Kumwa Mowa

Maganizo a Mulungu Pankhani ya Kumwa Mowa

Maganizo a Mulungu Pankhani ya Kumwa Mowa

MLENGI wathu, yemwe amatifunira zabwino, saletsa kumwa mowa pang’ono. N’chifukwa chake anapatsa anthu “vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake, ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.” (Salmo 104:15) Nthawi ina Yesu Khristu anathandiza kuti anthu asangalale paphwando la ukwati posandutsa madzi kukhala “vinyo wabwino.”​—Yohane 2:3-10.

N’zosachita kufunsa kuti Mlengi wathu amadziwa mmene mowa umakhudzire thanzi ndiponso ubongo wathu. Kudzera m’Baibulo, Atate wathu wakumwamba ‘amatiphunzitsa kuti tipindule,’ ndipo amatichenjeza mosapita m’mbali kuti tisamamwe mowa mwauchidakwa. (Yesaya 48:17) Taonani machenjezo awa:

“Musamaledzere naye vinyo, mmene muli makhalidwe oipa.” (Aefeso 5:18) ‘Zidakwa sizidzalowa mu ufumu wa Mulungu.’ (1 Akorinto 6:9-11) Mawu a Mulungu amaletsa ‘kumamwa mowa mwauchidakwa, maphwando aphokoso, ndi zina zotero.’​—Agalatiya 5:19-21.

Tsopano tiyeni tione ena mwa mavuto amene amabwera chifukwa chomwa mowa mwauchidakwa.

Kuopsa Komwa Mowa Mwauchidakwa

Ngakhale kuti mowa umathandiza m’thupi la munthu, uli ndi zinthu zina zimene zingawononge maganizo komanso thanzi. Kumwa mowa kwambiri kungabweretse mavuto otsatirawa:

Kungasokoneze maganizo a munthu moti “angamalephere kuganiza bwino.” (Miyambo 23:33, TEV) Allen, chidakwa chomwe tachitchula kumayambiriro kwa nkhani yoyamba ija, ananena kuti: “Uchidakwa ndi matenda okhudza thupi, maganizo ndiponso khalidwe la munthu. Munthu ukamamwa mwauchidakwa suganizira mavuto amene anthu ena akukumana nawo chifukwa cha khalidwe lako.”

Kungachititse kuti munthu asamadziletse. Baibulo limatichenjeza kuti: “Vinyo ndi chimera zichotsa nzeru.” (Hoseya 4:11, Malembo Oyera) N’chifukwa chiyani zili choncho? N’chifukwa chakuti munthu akamwa mowa, zinthu zoipa amayamba kuziona ngati zabwino. Kumwa mowa mwauchidakwa kungachititse kuti munthu azilephera kuchita zinthu zabwino. Mowa ungasokoneze khalidwe lathu labwino ndipo zimenezi zingawononge moyo wathu wauzimu.

Mwachitsanzo, John atakangana ndi mkazi wake, anatuluka m’nyumba atakwiya n’kupita komwa mowa. Atamwa mabotolo angapo kuti mtima ukhale pansi, mkazi wina anafika pamene iye anali. Atamwanso mabotolo ena angapo, John anatengana ndi mkaziyo kukachita chiwerewere. Kenako John anadandaula kwambiri kuti anachita chinthu chimene sakanachita n’komwe akanakhala kuti sanaledzere.

Kungachititsenso kuti munthu azilankhula ndiponso kuchita zinthu motayirira. Baibulo limafunsa kuti: “Ndani amakhala m’mavuto nthawi zonse? Ndani amakonda kukangana komanso kumenyana?” Kenako limayankha kuti: “Ndi amene amachezera kumwa mowa n’kumanena kuti, ‘Ndingomwako botolo limodzi lokha.’” (Miyambo 23:29, 30, Contemporary English Version) Kumwa mowa mwauchidakwa kungachititse munthu ‘kufanana ndi munthu wogona pakati panyanja, komanso munthu wogona tulo pamwamba pa mzati wa bwato.’ (Miyambo 23:34, Malembo Oyera) Munthu amene waledzera kwambiri angadzuke “atasupukasupuka, koma osakumbukira kuti chinachitika n’chiyani.”​—Miyambo 23:35, CEV.

Kungachititse kuti munthu adwale kwambiri. Baibulo limati: ‘Pa chitsiriziro chake mowa umaluma ngati njoka, nujompha ngati mamba.’ (Miyambo 23:32) Madokotala amavomereza kuti mawu amenewa ndi oona. Kumwa mowa kwambiri n’koopsa chifukwa kungachititse kuti munthu adwale matenda osiyanasiyana monga khansa, kutupa kwa chiwindi, kutupa kwa kapamba, matenda a shuga ndiponso kungachititse kuti mayi adzabereke mwana wozerezeka. Kumwa mowa kwambiri kungachititsenso matenda ofa ziwalo kapena amtima. Ndipo kumwa kwambiri mowa, ngakhale kamodzi kokha, kungachititse kuti munthu akomoke kapena kufa kumene. Komabe, pali chifukwa chachikulu chimene chimapangitsa kumwa mowa mwauchidakwa kukhala koopsa. Chifukwa chimenechi sichikukhudzana ndi matenda amene amayamba chifukwa chomwa mowa mwauchidakwa.

Vuto lalikulu la kumwa mowa mwauchidakwa. Ngakhale munthu atakhala kuti sanaledzere, ngati atamwa kwambiri angawononge ubwenzi wake ndi Mulungu. Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti: “Tsoka kwa iwo amene adzuka m’mamawa kuti atsate zakumwa zaukali; amene achezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsa!” Kenako linafotokoza kuti munthu akamamwa mowa mosadziletsa amawononga ubwenzi wake ndi Yehova. Limati: “Iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang’ana pa machitidwe a manja ake.”​—Yesaya 5:11, 12.

Mawu a Mulungu amatichenjeza kuti: ‘Tisakhale mwa akumwaimwa vinyo.’ (Miyambo 23:20) Baibulo limalangiza amayi achikulire kuti asakhale “akapolo a vinyo wambiri.” (Tito 2:3) N’chifukwa chiyani limachenjeza choncho? N’chifukwa choti pang’ono ndi pang’ono ndiponso mosadziwa, munthu amayamba kumwa mowa mwauchidakwa pafupipafupi. Pamapeto pake munthuyo angayambe kumadzifunsa kuti, “Ndidzadzuka liti? . . . Ndifuna kumwabe.” (Miyambo 23:35, Malembo Oyera) Munthu womwa mowa kwambiri amafika mpaka pomamwa m’mawa pofuna kupha matsire.

Baibulo limachenjeza kuti anthu omwa vinyo mopitirira muyezo, ochita maphwando a phokoso ndiponso omwa mwa mpikisano “adzayankha mlandu kwa uja wokonzeka kuweruza amoyo ndi akufa.” (1 Petulo 4:3, 5) Ponena za nthawi yathu ino, Yesu anachenjeza kuti: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa.”​—Luka 21:34, 35.

Komabe, kodi anthu omwe amamwa mowa mwauchidakwa angatani kuti apewe ‘kulemedwa ndi kumwa kwambiri’?

[Zithunzi pamasamba 4, 5]

Kumwa mowa mwauchidakwa kungayambitse mavuto ambiri