“Ndingomwako Botolo Limodzi Lokha”
“Ndingomwako Botolo Limodzi Lokha”
ALLEN anayamba kumwa mowa mwauchidakwa ali ndi zaka 11 zokha. * Iye ndi anzake ankakonda kusewera m’nkhalango, poyerekezera anthu amene ankawaona m’mafilimu. Zimene ankachita anthu a m’mafilimuwo zinali zongoyerekezera, koma mowa umene Allen ndi anzake ankamwa unali weniweni.
Tony anayamba kumwa mowa kwambiri ali ndi zaka 40. Poyamba iye ankamwa botolo limodzi kapena awiri usiku uliwonse, koma kenako anafika pomamwa mabotolo asanu kapena 6. Kenako anafika poti sankadziwa n’komwe kuchuluka kwa mabotolo amene wamwa patsiku.
Allen anapempha ena kuti amuthandize kuthana ndi vuto lake lomwa mowa mwauchidakwa. Koma Tony anakana kutsatira zimene achibale komanso anzake ankamuuza pomuthandiza kuti asinthe khalidwe lake. Tikunena pano, Allen adakali moyo ndipo amafotokozera anthu zimene zinkamuchitikira. Koma Tony anamwalira zaka zingapo zapitazo pangozi ya pamsewu yomwe inachitika chifukwa choti analedzera.
Ngakhale kuti munthu angaledzere ali yekha, mavuto amene amabwera chifukwa cha kuledzerako amakhudza kwambiri anthu ena. Kawirikawiri anthu oledzera amatukwana, amachitira ena nkhanza, amamenya anthu ena mwinanso kuwapha kumene. Nthawi zambiri anthu oledzera ndi amene amachititsa ngozi zapamsewu, amavulala kuntchito komanso nthawi zina amadwala matenda osiyanasiyana. Kumwa mowa mwauchidakwa kumawonongetsa ndalama zambirimbiri chaka chilichonse kuwonjera pa mavuto amene munthuyo, achibale ake ndiponso ana ake amakumana nawo.
Bungwe lina loona za umoyo linanena kuti “sikuti aliyense amene amamwa mowa tsiku lililonse ndiye kuti ndi chidakwa. Komanso si zidakwa zonse zimene zimamwa mowa tsiku lililonse.” (U.S. National Institutes of Health) Anthu ambiri omwe sizidakwa sazindikira kuti ayamba kumwa mowa kwambiri. Ena samwa mowa kawirikawiri koma akati amwe, amamwa mabotolo oposa asanu nthawi imodzi.
Ngati mwasankha kumwa mowa, kodi muyenera kumwa wochuluka bwanji? Kodi mungadziwe bwanji kuti pamene mwafika simukufunikanso kuganiza kuti, “ndingomwako botolo limodzi lokha”? (Miyambo 23:29, 30, Contemporary English Version) Munkhani zotsatirazi tiona mfundo zothandiza pankhani imeneyi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 Tasintha mayina ena.