Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anthu Onse Abwino Amapita Kumwamba?

Kodi Anthu Onse Abwino Amapita Kumwamba?

Kodi Anthu Onse Abwino Amapita Kumwamba?

YESU atatha kudya komaliza limodzi ndi atumwi ake madzulo a tsiku loti mawa lake aphedwa, analonjeza atumwiwo kuti adzapita kumwamba. Iye anati: “M’nyumba ya Atate wanga alimo malo ambiri okhalamo. Akanapanda kukhalamo, ndikanakuuzani, chifukwa ndikupita kukakukonzerani malo.” (Yohane 14:2) Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anawalonjeza malo kumwamba? Kodi iwo azikachita chiyani kumwambako?

Yesu ankaganiza za ntchito yapadera imene ankafuna kuti ophunzira ake akachite kumwamba. Madzulo a tsiku lomweli, iye anati: “Inu ndinu amene mwakhalabe ndi ine m’mayesero anga. Choncho ndikuchita nanu chipangano, mmene Atate wanga wachitira chipangano cha ufumu ndi ine.” (Luka 22:28, 29) Mulungu analonjeza Yesu kuti adzakhala Mfumu imene idzabweretse chinthu chimene anthu onse amafunikira kwambiri, chomwe ndi boma labwino. Yesu adzapulumutsa anthu osautsika ndipo adzaphwanya amene amawachitira zachinyengo. Mpando wachifumu wa Yesu udzakhala kumwamba, komabe iye adzalamulira anthu onse “kufikira malekezero a dziko lapansi.”​—Salmo 72:4, 8; Danieli 7:13, 14.

Komabe, Yesu sadzalamulira yekha. N’chifukwa chake analonjeza atumwi ake aja kuti adzawapatsa malo kumwamba. Atumwiwa anali anthu oyamba kusankhidwa kuti ‘adzalamulire dziko lapansi monga mafumu.’​—Chivumbulutso 5:10.

Kodi ndi anthu angati amene akufunika kupita kumwamba? Mofanana ndi boma lina lililonse, olamulira mu Ufumu wa Mulungu wakumwamba ndi ochepa poyerekezera ndi anthu onse amene azidzalamuliridwa ndi boma limeneli. Yesu anauza amene azidzalamulira naye kuti: “Musaope, kagulu ka nkhosa inu, chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani ufumu.” (Luka 12:32) “Kagulu ka nkhosa” kameneka ndi anthu 144,000. (Chivumbulutso 14:1) Chiwerengero chimenechi ndi chaching’ono poyerekezera ndi anthu mamiliyoni amene adzasangalale ndi moyo wosatha padziko lapansi monga nzika zokhulupirika za Ufumu wa Mulungu.​—Chivumbulutso 21:4.

Choncho, sikuti anthu onse abwino amapita kumwamba. Mfumu Davide anali munthu wabwino, koma mtumwi Petulo anati: “Davide sanakwere kumwamba.” (Machitidwe 2:34) Nayenso Yohane Mbatizi anali munthu wabwino. Komabe Yesu anasonyeza kuti Yohane sadzapita kumwamba kukakhala mfumu. Yesu anati: “Mwa onse obadwa mwa akazi, sanabadwepo wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma munthu amene ali wocheperapo mu ufumu wa kumwamba ndi wamkulu kuposa iyeyu.”​—Mateyo 11:11.

Kodi Mudzalandira Mphoto ya Anthu Abwino?

Kodi munthu ayenera kuchita chiyani kuti adzalandire mphoto yokhala ndi moyo wosatha padziko lapansi? Yesu ananena kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Lembali likusonyeza kuti, chifukwa chakuti Mulungu amakonda dziko, wapereka kwa anthu onse mwayi wokhala ndi moyo wosatha. Koma okhawo amene ali ‘okhulupirira’ ndi amene adzalandire mphoto imeneyi.

Munthu ayenera kukhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene akuzidziwa molondola. (Yohane 17:3) Inuyo mungasonyeze kuti ndinu munthu wabwino ngati muphunzira zambiri zokhudza cholinga cha Yehova kwa anthu. Chitanipo kanthu pa zimene mukuphunzira kuti musonyeze chikhulupiriro. Ndipo dziwani kuti muli ndi mwayi wodzalandira moyo wosatha.

[Bokosi patsamba 7]

Kodi Baibulo Limati Chiyani?

Funso:

Kodi anthu abwino akafa chimawachitikira n’chiyani?

Yankho:

“Akufa sadziwa kanthu bi.”​MLALIKI 9:5.

Funso:

Kodi anthu abwino amayembekezera kuti mtsogolo mudzachitika zotani?

Yankho:

“Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu ake [a Yesu] ndipo adzatuluka.”​YOHANE 5:28, 29.

Funso:

Kodi anthu abwino ochuluka azidzakhala kuti?

Yankho:

“Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​SALMO 37:29.