Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu

Rabeka Anali Wofunitsitsa Kukondweretsa Yehova

Rabeka Anali Wofunitsitsa Kukondweretsa Yehova

RABEKA ndi dzina lotchuka masiku ano. Kodi ukudziwa wina aliyense amene ali ndi dzina limeneli?​— * Rabeka anali munthu wofunika kwambiri m’buku lotchuka padziko lonse, lomwe ndi Baibulo. Kodi ukudziwa chilichonse chokhudza iyeyu?​— Tiyenera kuphunzira za Rabeka chifukwa chitsanzo chake chingatithandize kutumikira Mulungu woona, Yehova.

Rabeka ndi mkazi wachiwiri amene Baibulo limatchula kuti ankalambira Yehova movomerezeka. Kodi ukudziwa mkazi woyamba kutchulidwa m’Baibulo kuti ankalambira Yehova movomerezeka?— Anali Sara, mkazi wa Abulahamu. Atakalamba, Sara anabereka mwana wamwamuna mmodzi yekha, dzina lake Isake. Tsopano tiye tione mmene Rabeka anasonyezera kuti anali wofunitsitsa kukondweretsa Yehova ndiponso zimene zinachitika kuti akumane ndi Isake.

Panali patadutsa zaka 60 kuchokera pamene Mulungu anauza Abulahamu ndi Sara kuti achoke kwawo ku Harana n’kupita m’dziko la Kanani. Abulahamu ndi Sara atakalamba kwambiri, Mulungu anawalonjeza kuti adzakhala ndi mwana wamwamuna ndipo adzamutche dzina loti Isake. N’zosakayikitsa kuti makolo a Isake ankamukonda kwambiri mwana wawoyu. Patapita nthawi, Sara anamwalira ali ndi zaka 127. Apa n’kuti Isake atakula ndithu motero anali ndi chisoni kwambiri chifukwa cha imfa ya mayi ake. Abulahamu sankafuna kuti Isake adzakwatire mkazi wa ku Kanani chifukwa anthu amenewa sankalambira Yehova. Choncho, iye anatuma wantchito wake kuti apite kwa abale ake a Abulahamu amene ankakhala ku Harana kuti akamufunire Isake mkazi. N’kutheka kuti wantchitoyu anali Eliezere. Iye anayenda ulendo wa makilomita 800 kuti akafike kumeneko.​—Genesis 12:4, 5; 15:2; 17:17, 19; 23:1.

Pa ulendowu Eliezere anapita limodzi ndi antchito anzake ena ndipo anatenga ngamila 10 zimene zinanyamula katundu ndi mphatso zokapereka kwa mkazi amene angakapezeyo. Patapita masiku angapo iwo anafika ku Harana. Kenako anaima pachitsime chifukwa Eliezere ankadziwa kuti dzuwa likapendeka anthu ankabwera kudzamwetsa ziweto zawo komanso kudzatunga madzi akunyumba kwawo. Ndiyeno Eliezere anapemphera kuti apempha madzi akumwa kwa akazi amene abwere kuchitsimeko ndipo iye asankhira Isake mkazi amene angayankhe kuti: ‘Imwani, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zanu.’

Zimenezi zinachitikadi ndendende. Kuchitsimeko kunafika mtsikana wina “wokongola kwambiri,” dzina lake Rabeka. Eliezere atam’pempha madzi akumwa, iye anayankha kuti: ‘Ndidzatungiranso ngamila zanu.’ Pamene iye ‘ankathamangira kuchitsimeko mobwerezabwereza kukatunga madzi,’ Eliezere ankangomuyang’anitsitsa modabwa. Tangoganiza chintchito chimene Rabeka anali nacho kuti ngamila zonse 10 ziphe ludzu. Iye anafunika kuzitungira madzi okwanira zigubu zikuluzikulu pafupifupi 50.

Kenako Eliezere anam’patsa Rabeka mphatso zokongola kwambiri, ndipo Rabeka anamuuza kuti iye ndi mwana wa Betuele. Ameneyu anali m’bale wake wa Abulahamu. Rabeka anapempha Eliezere ndi anzakewo kuti apite kwa makolo ake kuti akapeze malo ogona. Kenako iye anathamanga kuti atsogole ndi kukauza makolo ake za alendo amene Abulahamu anawatuma kuchokera ku Kanani.

Mlongo wake wa Rabeka, dzina lake Labani, atangoona mphatso zamtengo wapatali zimene Eliezere anapatsa mchemwali wake, anawauza alendowo kuti alowe m’nyumba. Koma Eliezere ananena kuti: ‘Sindidya ndisananene chimene ndadzera.’ Choncho anafotokoza zimene Abulahamu anamutuma. Betuele, limodzi ndi mkazi wake, komanso Labani anasangalala kwambiri ndipo anavomereza zoti Rabeka akakwatiwe ndi Isake.

Atatha kudya, Eliezere limodzi ndi amene anali nawo anagona. Kutacha, Eliezere ananena kuti: “Mundilole ine ndimke kwa mbuyanga.” Koma mayi ndiponso mlongo wake wa Rabeka anawapempha kuti akhalebe kwa masiku osachepera 10. Rabeka atafunsidwa ngati angakonde kupita mwamsanga, iye anayankha kuti: “Ndidzanka.” Apa iye anasonyeza kuti anali wofunitsitsa kupita kwa Isake. Nthawi yomweyo ananyamuka limodzi ndi Eliezere. Atafika ku Kanani, iye anakhala mkazi wa Isake.​—Genesis 24:1-58, 67.

Rabeka ankadziwa kuti mwina sadzaonananso ndi banja lake ndiponso anzake. Ndiye kodi ukuganiza kuti zinali zophweka kuti iye asiyane nawo ndi kupita kudera lakutali?​— Ayi, zinali zovuta. Motero Rabeka anadalitsidwa chifukwa chokhala wofunitsitsa kuchita zinthu zokondweretsa Yehova. Patapita nthawi, Mpulumutsi wathu Yesu Khristu anadzabadwa kwa zidzukulu za Rabeka. Ifenso tingadalitsidwe ngati tikhala wofunitsitsa kuchita zimene zingakondweretse Yehova monga mmene Rabeka anachitira.​—Aroma 9:7-10.

^ ndime 3 Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana wanu, pamene pali mzere pakusonyeza kuti muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.