‘Yehova Amayang’ana Mumtima’
Yandikirani Mulungu
‘Yehova Amayang’ana Mumtima’
MAONEKEDWE apusitsa. Mmene munthu amaonekera kunja si mmene angakhaliredi mkati, kapena kuti mumtima mwake. Anthufe timakonda kumuganizira munthu zinazake pongotengera maonekedwe ake. Koma n’zosangalatsa kuti Yehova Mulungu sayang’ana maonekedwe okha. Tingamvetse bwino mfundo imeneyi poganizira nkhani imene ili pa 1 Samueli 16:1-12.
Tayerekezerani kuti mukuona izi zikuchitika: Yehova akufuna kudzoza mfumu yatsopano ya mtundu wa Isiraeli. Ndiye akuuza mneneri Samueli kuti: “Ndidzakutumiza kwa Jese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.” (Vesi 1) Yehova sakumuuza dzina la munthu amene wasankhayo koma wangonena kuti ndi mmodzi wa ana aamuna a Jese. Popita ku Betelehemuko, n’kutheka kuti Samueli akudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikam’dziwa bwanji mwana amene Yehova wasankhayo?’
Pofika ku Betelehemu, Samueli akukonza zoti Jese ndi ana ake abwere kumwambo wopereka nsembe. Atangofika Eliyabu, mwana woyamba wa Jese, Samueli akukopeka ndi maonekedwe ake, moti akuona kuti ufumu ungamukhale kwambiri. Kenako akunena kuti: “Zoonadi, wodzozedwa wa Yehova ali pamaso pake.”—Vesi 6.
Koma Yehova sakuona choncho. Iye akuuza Samueli kuti: “Usayang’ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza ine ndinam’kana iye.” (Vesi 7) Yehova sakukopeka ndi kutalika kapenanso kukongola kwa Eliyabu. Maso a Yehova samangoona maonekedwe a kunja okha, koma amaonanso kukongola kwenikweni kwa munthu kumene kumakhala mumtima.
Yehova akuuza Samueli kuti: “Pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.” (Vesi 7) Inde, chimene Yehova amayang’ana mwa munthu ndi mtima wake chifukwa ndiwo chimake cha zonse zimene amaganiza ndiponso kuchita. Popeza ‘Yehova amayesa mitima,’ akukana kudzoza Eliyabu komanso ana ena 6 a Jese amene wawabweretsa kwa Samueli.—Miyambo 17:3.
Patsala mwana mmodzi wotsiriza wa Jese amene anali ‘koweta nkhosa,’ ndipo dzina lake ndi Davide. (Vesi 11) Motero Jese akutuma munthu kuti akaitane Davide kutchire kumene ali ndipo posakhalitsa akufika naye kwa Samueli. Kenako Yehova akuuza Samueli kuti: “Nyamuka um’dzoze, pakuti ndi ameneyu.” (Vesi 12) N’zoona kuti Davide ndi mnyamata “wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma.” Koma kukongola kwa mumtima mwake ndi kumene kwachititsa kuti akhale wovomerezekadi kwa Mulungu.—1 Samueli 13:14.
Anthu ambiri masiku ano amaona kuti kukongola kwa thupi n’kofunika kwambiri, choncho n’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova Mulungu samatengeka ndi maonekedwe a munthu. Kwa iye zilibe kanthu kuti ndinu wamfupi kapena wamtali, kaya ena amakuonani kuti ndinu wokongola kwambiri kapena ayi. Chimene Yehova amaona kuti n’chofunika kwambiri ndi mtima wanu. Tikukhulupirira kuti kudziwa zimenezi kungakulimbikitseni kukhala ndi makhalidwe abwino amene angachititse kuti mukhale wokongola m’maso mwa Mulungu.