Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yesu Anapereka Moyo Wake M’malo mwa Anthu Ambiri

Yesu Anapereka Moyo Wake M’malo mwa Anthu Ambiri

Yesu Anapereka Moyo Wake M’malo mwa Anthu Ambiri

Yesu Khristu anauza otsatira ake kuti iye sanabwere padziko lapansi “kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mateyo 20:28) Iye anapereka moyo wake ndi mtima wonse kuti athandize anthu.

Kodi zinatheka bwanji Yesu kupereka dipo mwa imfa yake? Nanga n’chifukwa chiyani iye anafunika kuchita zimenezi? Kodi Yesu anapereka moyo wake m’malo mwa ndani makamaka? Ndipo kodi imfa yakeyo ingakuthandizeni bwanji?

Mboni za Yehova zikukuitanani kuti mukasonkhane nawo ndi kufufuzira limodzi mayankho a m’Baibulo a mafunso amenewa. Chaka chino, mwambo wokumbukira imfa ya Yesu udzachitika Lachiwiri, pa 30 March, dzuwa litalowa. Pamwambo umenewu padzakambidwa nkhani imene idzayankha mafunso amene ali pamwambawa.

Mutha kudzapita ku Nyumba ya Ufumu iliyonse imene mwayandikana nayo. Funsani Mboni za Yehova za kwanuko kuti mudziwe nthawi komanso malo enieni amene mwambowu udzachitikire.