Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Bata ndi Mtendere Weniweni Zidzakhalako Liti?

Kodi Bata ndi Mtendere Weniweni Zidzakhalako Liti?

Nkhani ya Onse Yapadera

Kodi Bata ndi Mtendere Weniweni Zidzakhalako Liti?

Kwa zaka zambiri, anthu akhala akufuna kuti padzikoli pakhale bata ndi mtendere koma alephera. Chifukwa chiyani? Baibulo limatiuza zifukwa ziwiri zazikulu zimene zachititsa kuti anthu alephere kubweretsa bata ndi mtendere padzikoli. Koma m’Baibulo mulinso mfundo yolimbikitsa iyi: Mulungu walonjeza kuti adzabweretsa padziko lapansili bata ndi mtendere weniweni umene sudzatha.

Nanga kodi bata ndi mtendere umenewu zidzabwera bwanji? Ndipo zidzabwera liti? Kodi inuyo muyenera kuchita chiyani kuti mudzalandire madalitso amenewa? Mafunso amenewa adzayankhidwa munkhani ya onse yakuti “Kodi Bata ndi Mtendere Weniweni Zidzakhalako Liti?” Nkhani yochokera m’Baibulo imeneyi idzakambidwa padziko lonse m’mayiko oposa 230. M’mayiko ambiri, nkhaniyi idzakambidwa pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova, Lamlungu pa 18 April, 2010. Funsani Mboni za Yehova za m’dera lanu kuti zikudziwitseni malo ndiponso nthawi imene nkhaniyi idzakambidwe kwanuko. Tidzakulandirani ndi manja awiri.