Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kuwonjezera pa zimene Baibulo limanena, kodi palinso umboni wina wotsimikizira kuti Yesu analipodi?

Anthu angapo olemba mabuku osati a m’Baibulo anatchula Yesu m’mabuku awo. Anthuwa anakhalapo m’nthawi yoyandikana ndi nthawi imene Yesu anakhala padziko lapansi pano. Mmodzi mwa anthu amenewa anali Cornelius Tacitus. Iye analemba mbiri ya Aroma panthawi imene ankalamulidwa ndi mafumu. Ponena za moto umene unawononga Roma mu 64 C.E., Tacitus ananena kuti panali mphekesera zoti Mfumu Nero ndi amene anabutsa motowo. Iye ananenanso kuti Nero ananamizira kagulu kena ka anthu otchedwa Akhristu kuti ndi amene anayambitsa motowo. Tacitus analemba kuti: “Khristu, munthu yemwe kagulu ka anthu otchedwa Akhristu kanatengera dzina lawo, anaphedwa ndi Pontiyo Pilato mu ulamuliro Tiberiyo.”​—Annals, XV, 44.

Nayenso Flavius Josephus, yemwe anali Myuda wolemba mbiri yakale, anatchula Yesu m’mabuku ake. Pofotokoza zimene zinachitika pakati pa nthawi imene Fesito, kazembe wachiroma wa ku Yudeya anamwalira cha m’ma 62 C.E., ndi nthawi imene Albinus anayamba kulamulira, Josephus ananena kuti Mkulu wa Ansembe Anasi “anachititsa msonkhano wa Bungwe Lalikulu la Ayuda ndipo anabweretsa Yakobe, m’bale wake wa Yesu yemwe ankatchedwanso Khristu, limodzi ndi anthu ena.”​—Jewish Antiquities, XX, 200 (ix, 1).

N’chifukwa chiyani Yesu ankatchedwa Khristu?

Mabuku a Uthenga Wabwino amati mngelo Gabiriele anaonekera kwa Mariya n’kumuuza kuti adzakhala ndi pakati ndipo adzabereka mwana wa mwamuna, dzina lake Yesu. (Luka 1:31) Dzina lakuti Yesu linali lodziwika ndithu kwa Ayuda a m’nthawi imeneyo. Wolemba mbiri wina wachiyuda dzina lake Josephus, anatchula anthu 12 amene anali ndi dzina limeneli, koma amene sanatchulidwe m’Baibulo. Yesu yemwe anali mwana wa Mariya ankatchedwa kuti “Mnazarete,” ndipo zimenezi zinkathandiza kuti anthu azidziwa kuti Yesu wake anali wa ku Nazarete. (Maliko 10:47) Iye ankadziwikanso ndi dzina loti “Khristu,” kapena Yesu Khristu. (Mateyo 16:16) Kodi dzina loti Khristu limatanthauza chiyani?

Mawu a Chichewa akuti “Khristu” anachokera kumawu a Chigiriki akuti Khri·stosʹ, ndipo ndi mawu ofanana ndi a Chiheberi akuti Ma·shiʹach (Mesiya). Mawu awiri onsewa amatanthauza “Wodzozedwa.” Anthu enanso amene anakhalapo Yesu asanabwere padziko lapansi ankatchedwa ndi dzina limeneli. Mwachitsanzo, Mose, Aroni ndiponso Mfumu Davide amadziwika kuti anali odzozedwa, kutanthauza kuti anali osankhidwa ndi Mulungu kuti akhale m’maudindo omwe anali nawo. (Levitiko 4:3; 8:12; 2 Samueli 22:51; Aheberi 11:24-26) Koma Yesu, yemwe anali Mesiya wolonjezedwa, anali woimira Yehova wamkulu koposa ena onsewa. Motero, m’pomveka kuti ankatchedwa “Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”​—Mateyo 16:16; Danieli 9:25.

[Chithunzi patsamba 15]

Chithunzi Chojambulidwa pa Manja, Chosonyeza Flavius Josephus