Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Amakhululukira Munthu wa “Mtima Wosweka ndi Wolapa”

Amakhululukira Munthu wa “Mtima Wosweka ndi Wolapa”

Yandikirani Mulungu

Amakhululukira Munthu wa “Mtima Wosweka ndi Wolapa”

2 SAMUELI 12:1-14

TONSEFE timachimwa nthawi zambiri ndipo ngakhale titam’pempha kwambiri Mulungu kuti atikhululukire, tingamadzifunsebe kuti, ‘Kodi Mulungu amamvadi mapemphero anga ochokera pansi pa mtima om’pempha kuti andikhululukire? Kodi andikhululukiradi?’ Baibulo limaphunzitsa mfundo yolimbikitsa yakuti: Ngakhale kuti Yehova sasekerera munthu akamachita zoipa, iye ndi wokonzeka kukhululukira munthu wochimwa amene walapa mochokera pansi pa mtima. Mfundo imeneyi tingaimvetse bwino tikaganizira nkhani ya Mfumu Davide ya ku Isiraeli, yomwe ili m’chaputala 12 cha buku la 2 Samueli.

Yesani kuona nkhani yotsatirayi m’maganizo anu: Davide wachita machimo aakulu kwambiri. Iye wachita chigololo ndi Bateseba ndipo atalephera kubisa tchimolo akuchititsa kuti mwamuna wa Batesebayo aphedwe. Kenako, Davide sakuuza aliyense za machimo akewa kwa miyezi ingapo, kukhala ngati sanachite choipa chilichonse. Komabe, Yehova waona machimo onse amene Davide wachita. Koma akuonanso kuti Davide ali ndi mtima wabwino moti angathe kulapa. (Miyambo 17:3) Ndiyeno Kodi Yehova achita chiyani pamenepa?

Yehova akutuma mneneri Natani kuti apite kwa Davide. (Vesi 1) Motsogoleredwa ndi mzimu woyera, Natani akulankhula ndi mfumuyo mwaluso. Iye akudziwa kuti ayenera kusamala kalankhulidwe kake. Kodi iye angatani kuti am’thandize Davide kuzindikira kuti machimo ake ndi aakulu ndiponso kuti asiye kudzinyenga?

Pofuna kuti Davide asadzilungamitse, Natani akumuuza nkhani yoti imukhudze mtima kwambiri monga munthu woti anagwirapo ntchito yoweta nkhosa. Nkhani yake ndi ya anthu awiri, wina wosauka ndipo winayo wolemera. Wolemerayo anali ndi “zoweta zazing’ono ndi zazikulu zambiri ndithu,” pamene wosaukayo anali ndi “kamwana kakakazi ka nkhosa” kamodzi kokha. Tsiku lina munthu wolemera uja analandira mlendo ndipo anafuna kum’konzera chakudya. M’malo mopha imodzi mwa nkhosa zake, iye anakatenga nkhosa ya munthu wosauka ija. Poganiza kuti nkhaniyi inachitikadi, Davide akupsa mtima kwambiri n’kunena mokalipa kuti: “Munthu amene anachita ichi, ayenera kumupha.” N’chifukwa chiyani iye akugamula choncho? Davide akufotokoza kuti: “Chifukwa anachita ichi osakhala nacho chifundo.” *​—Vesi 2-6.

Fanizo la Natani lakwaniritsa cholinga chake. Ndipo kwenikweni Davide wadziweruza yekha. Tsopano Natani akumuuza mosapita m’mbali kuti: “Munthuyo ndi inu nomwe.” (Vesi 7) Popeza Natani akulankhula m’malo mwa Mulungu, zikuonekeratu kuti zimene Davide wachita zakwiyitsa kwambiri Yehova. Pophwanya malamulo a Mulungu, Davide wasonyeza kuti sakulemekeza Mulungu amene anapereka malamulowo. Ndiye Mulungu akuti: “Unandipeputsa ine.” (Vesi 10) Davide akukhudzidwa mtima kwambiri ndi mawu amphamvu omudzudzulawo ndipo akuvomereza tchimo lake ponena kuti: “Ndinachimwira Yehova.” Natani akumulimbitsa mtima Davide pomuuza kuti Yehova wamukhululukira, koma akumuuzanso kuti akumana ndi mavuto chifukwa cha zimene anachita.​—Vesi 13 ndi 14.

Tchimo la Davide litaonekera poyera, iye analemba mawu amene ali mu Salmo 51. Mu Salmo limeneli, Davide anafotokoza zonse zimene zinali mumtima mwake, ndipo zimasonyeza kuti anali atalapadi mochokera pansi pa mtima. Davide anapeputsa Yehova pophwanya malamulo ake. Koma atalapa anasangalala kwambiri poona kuti Mulungu wamukhululukira ndipo poyamikira anamuuza Yehova kuti: “Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.” (Salmo 51:17) Kwa munthu wochimwa amene akufuna kuti Yehova amuchitire chifundo, amenewa ndi mawu okhazika mtima pansi kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Kalelo anthu ankakonda kupha nkhosa pofuna kusonyeza mlendo kuti amulandira ndi manja awiri. Koma kuba nkhosa ya wina unali mlandu womwe chilango chake chinali kubweza nkhosa zinayi. (Eksodo 22:1) Davide anaona kuti munthu wolemerayo sanasonyeze chifundo potenga nkhosa ya munthu wosaukayo. Pochita zimenezi iye analanda wosaukayo nkhosa imene ikanathandiza banja lake kupeza mkaka ndi ubweya, mwinanso akanaisunga kuti idzabereke nkhosa zina.