Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Tingachite Kuti Titsatire Khristu

Zimene Tingachite Kuti Titsatire Khristu

Zimene Tikuphunzira kwa Yesu

Zimene Tingachite Kuti Titsatire Khristu

Munthu akasonyeza kuti akukhulupirira Yesu, iye ankakonda kumuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.” (Mateyo 9:9; 19:21) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale wotsatira wa Yesu, kapena kuti tikhale Mkhristu? Taonani mafunso atatu otsatirawa, omwe ndi ofunika kwambiri, ndiponso onani mayankho ake:

Kodi muyenera kukhala bwanji ndi anthu ena?

▪ Wotsatira wa Yesu ayenera kumvera malangizo ake okhudza mmene ayenera kukhalira ndi anthu ena. Mwachitsanzo, Yesu ananena kuti: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.” Kodi muyenera kuchitanji munthu wina akakulakwirani? Yesu anati: “Thetsa nkhani mofulumira ndi wokuimba mlandu.” Iye anauzanso otsatira ake kuti: “Ngati simumakhululukira anthu zolakwa zawo, Atate wanu sadzakukhululukirani zolakwa zanu.”​—Mateyo 5:25; 6:15; 7:12.

Yesu anapereka malangizo otsatirawa kwa anthu apabanja: “Inu munamva kuti anati, ‘Usachite chigololo.’ Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.” Mkhristu weniweni amaona kuti zimene Yesu anaphunzitsa n’zofunika kwambiri pamoyo wake ndipo amaziganizira nthawi zonse.​—Mateyo 5:27, 28.

Akhristu oona amalolera kukumana ndi mavuto pofuna kuthandiza ena. Iwo amachita zimenezi potsanzira Yesu yemwe ankalolera kuvutikira ena. Mwachitsanzo, panthawi ina Yesu ndi ophunzira ake anatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira moti analibe ngakhale nthawi yoti adye chakudya. Motero Yesu anatengana ndi ophunzira akewo pabwato kuti apite kwinakwake kwaokha kukapuma. Koma anthu atamva zimenezi, anathamanga n’kukafikako Yesu ndi ophunzirawo asanafike. Baibulo limati: “Potsika, anaona khamu lalikulu la anthu, koma anawamvera chifundo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda m’busa. Ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Maliko 6:30-34) Mungathe kutsatira Yesu pochita zimene Mulungu akufuna kuti muzichita, ngakhale patakhala zovuta zina.

N’chifukwa chiyani muyenera kuuza ena uthenga wabwino?

▪ Yesu anauza otsatira ake kuti azilalikira uthenga wabwino. Iye anauza atumwi ake kuti: “Pitani ndi kulalikira kuti, ‘Ufumu wa kumwamba wayandikira.’” (Mateyo 10:7) Masiku ano, otsatira a Yesu ali ndi uthenga wofunika kwambiri chifukwa Yesu anapemphera kuti: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona.”​—Yohane 17:3.

Yesu analosera za ntchito imene otsatira ake ambirimbiri adzagwire. Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse.” (Mateyo 24:14) Ngati munadziwa za Ufumu wa Mulungu ndipo mumakhulupirira zimene Baibulo limaphunzitsa, n’zosakayikitsa kuti mungasangalale kuuza ena zimene mukudziwazo. Monga poyambira, otsatira a Yesu ambiri amalalikira za Ufumu wa Mulungu kwa achibale awo.​—Yohane 1:40, 41.

N’chifukwa chiyani muyenera kubatizidwa?

▪ Panthawi imene Yesu ankabatizidwa mumtsinje wa Yorodano, zikuoneka kuti anapemphera kuti: ‘Ndabwera kudzachita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.’ (Aheberi 10:7) Ngati mukufuna kuchita chifuniro cha Mulungu, nanunso muyenera kubatizidwa. Yesu anapereka lamulo lakuti: “Mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse. Muziwabatiza.”​—Mateyo 28:19.

Kodi munthu wobatizidwa amakhala ndi udindo komanso mwayi wotani? Otsatira a Yesu omwe ndi obatizidwa amatumikira Mulungu ndi moyo wawo wonse. Yesu anatchula mawu a m’chilamulo cha Mulungu, akuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse.” (Mateyo 22:37) Iye anatinso: “Ngati munthu akufuna kunditsatira adzikane yekha.” (Mateyo 16:24) Ubatizo umaimira zimene munthu wasankha zoti adzikane yekha n’kudzipereka kwa Mulungu. Anthu amene ali paubwenzi wapadera umenewu ndi Mulungu angathe kum’pempha kuti awathandize kukhala ndi chikumbumtima choyera.​—1 Petulo 3:21.

Kuti mudziwe zambiri, onani mutu 18 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.