Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi chipata cha mudzi, kapena kuti mzinda, chimene chimatchulidwa kawirikawiri m’Baibulo chinali chiyani?

Kale mizinda yambiri inkakhala ndi mipanda ikuluikulu. Mkati mwamipandayi munali malo omwe anthu ankakumana kuti achite misonkhano yosiyanasiyana, malonda komanso kuti akambirane nkhani zosiyanasiyana. Kumalo amenewa ankalengezerako zochitika zosiyanasiyana ndipo nthawi zina aneneri ankalengezerako uthenga wawo. (Yeremiya 17:19, 20) Buku lina linanena kuti “pafupifupi zochitika zonse zokhudza anthu a mumzinda zinkachitikira kuchipata kapena malo ena oyandikana ndi chipatacho.”​—The Land and the Book.

Mwachitsanzo, Abulahamu anagula munda ku Efroni kuti ukhale manda ndipo anachita zimenezi “pamaso pa ana a Heti, pa onse amene analowa pachipata cha mudzi wake.” (Genesis 23:7-18) Komanso pamene Boazi anafuna kuchita mwambo wotenga Rute pamodzi ndi cholowa chake, potsatira lamulo lokhudza ukwati wapachilamu, anapempha akuluakulu 10 a ku Betelehemu kuti apite kuchipata cha mzinda komwe iye anakonza zoti kukachitikire mwambowo. (Rute 4:1, 2) Ndiponso kuchipata cha mzinda ndi kumene akulu a mzindawo ankaweruzirako milandu.​—Deuteronomo 21:19.

Kodi ku Ofiri kumene Baibulo limanena kuti kunkachokera golide wabwino kwambiri kunali kuti?

Buku la Yobu ndi limene limatchula koyamba za ‘golide wa ku Ofiri’ kuti anali ‘woyengedwa bwino.’ (Yobu 28:15, 16) Patatha zaka 600 kuchokera m’nthawi ya Yobu, Mfumu Davide anasonkhanitsa ‘golide wa ku Ofiri’ kuti amangire kachisi wa Yehova ku Yerusalemu. Nayenso mwana wake Solomo anaitanitsa golide kuchokera ku Ofiri.​—1 Mbiri 29:3, 4; 1 Mafumu 9:28.

Malinga ndi zimene Malemba amanena, Solomo anali ndi zombo zambiri zopangidwa ku Ezioni Geberi, dera la m’mphepete mwa Nyanja Yofiira. Zombozi zinkabweretsa golide wochekera ku Ofiri. (1 Mafumu 9:26) Akatswiri odziwa za malo akale amati dera la Ezioni Geberi lili m’mphepete mwa nyanja ya Aqaba, malo amene masiku ano amatchedwanso Elat. Zombo zochokera m’derali zinkatha kufika ku Nyanja Yofiira kapenanso kumadera akutali ochitira malonda monga ku Africa kapena ku India. Mwina limodzi mwa madera amenewa ndi kumene kunali malo otchedwa Ofiri. Koma ena amakhulupirira kuti dera la Ofiri linali ku Arabia komwe akatswiri apezako migodi ya golide yakale kwambiri ndipo chaposachedwapa anthu akhala akukumbako golide.

Ngakhale kuti ena amaganiza kuti nkhani yoti Solomo anali ndi migodi ya golide ku Ofiri ndi yopeka, katswiri wina wofufuza zinthu zakale za ku Iguputo, dzina lake Kenneth A. Kitchen, analemba kuti: “Ofiri anali malo enieni. Phale lakale lolembedwa m’Chiheberi, lomwe mwina ndi la m’ma 700 B.C.E., lili ndi mawu achidule olembedwa bwino akuti: ‘Golide wa ku Ofiri wokwana masekeli 30 [340 g] apite ku Betihoroni.’ Apa n’zoonekeratu kuti Ofiri anali malo enieni amene kunkachokera golide, monga mmene amaneneranso kuti ‘golide wa ku ‛Amau,’ kapena ‘golide wa ku Punti,’ kapenanso ‘golide wa ku Kusi,’ amene amatchulidwa m’zolemba za ku Iguputo. Zolemba zimenezi zikusonyeza kuti golideyo ankatchulidwa ndi dzina la malo amene anachokera kapena mmene anamuyengera.”

[Chithunzi patsamba 15]

Abulahamu Ali Pachipata cha Mzinda Kuti Agule Malo

[Chithunzi patsamba 15]

Phale Lolembedwa M’chiheberi Lotchula Malo Otchedwa Ofiri

[Mawu a Chithunzi]

Collection of Israel Antiquities Authority, Photo © The Israel Museum, Jerusalem