Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tasiya Kuopa Tchimo?

Kodi Tasiya Kuopa Tchimo?

Kodi Tasiya Kuopa Tchimo?

M’MBUYOMU, anthu akapita kutchalitchi, nthawi zambiri ankamva atsogoleri akulalikira za kuipa kochita zimene amati ndi “machimo 7 owopsa kwambiri.” Machimo amenewa ndi chilakolako cha kugonana, dyera, kukonda kwambiri chuma, ulesi, mkwiyo, kusirira ndiponso kunyada. Nthawi zambiri wolalikirayo ankatchula kuipa kochita machimo amenewa ndipo ankalimbikitsa anthu kuti atembenuke ndiponso alape. Munthu wina wolemba mabuku analemba kuti: “Koma masiku ano, atsogoleri ambiri azipembedzo amapewa kulalikira uthenga umene sungasangalatse omvera awo. Iwo amakonda kulalikira uthenga womwe akudziwa kuti ungasangalatse omvera awo.”

Nawonso anthu ena olemba nkhani m’manyuzipepala aona kuti ndi mmenedi atsogoleri azipembedzo akuchitira. Taonani zina mwa zimene analemba:

▪ “Atsogoleri sakulalikiranso zoti anthu asiye machimo, alape ndiponso apulumutsidwe. M’malomwake, amangolalikira zowakomera anthuwo powauza zimene angachite kuti azidzisangalatsa ndiponso asamadzikayikire.”​—Star Beacon, Ashtabula, Ohio.

▪ “Zikuoneka kuti palibe amene amadandaulanso akachita tchimo.”​—Newsweek.

▪ “Masiku ano sitiganiziranso zimene Mulungu amafuna kuti tichite, koma timangoganizira zimene Mulunguyo angatichitire.”​—Chicago Sun-Times.

Masiku ano, anthu osiyana zikhalidwe, zipembedzo ndiponso zipani amakhala dera limodzi ndipo zimenezi zimachititsa kuti asamadzudzulane akamachita zinthu zolakwika. Iwo amaona kuti kudzudzula anthu ena n’kupanda ulemu komanso limenelo ndilo tchimo lalikulu. N’chifukwa chake anthu ambiri amayendera mfundo yakuti: ‘Zimene umakhulupirira kuti n’zabwino kwa iweyo, usakakamize anthu ena kuti atsatire zimenezo. Masiku ano, anthu amayendera mfundo zosiyanasiyana. Palibe munthu amene anganene kuti iye yekha ndi amene akudziwa zolondola pa nkhani ya makhalidwe. Mfundo zomwe anthu ena amayendera n’zofunika kwambiri kwa iwo ngati mmene inuyo mumaonera mfundo zanu.’

Maganizo amenewa achititsa kuti anthu asinthe mawu ena ndi ena ndipo anthu sakonda kugwiritsa ntchito mawu akuti “tchimo” munthu wina akalakwa. M’malomwake anthu ambiri amangowatchula mwamasewera. Mwachitsanzo, ngati mwamuna ndi mkazi osakwatirana akukhalira limodzi, anthu amangoti “limenelo ndi banja.” Ngati ena akuchita “zachiwerewere,” anthu amangoti “akusangalala ndi moyo.” Ndipo ngati akazi okhaokha kapena amuna okhaokha akugonana, anthu amangoti “ndi ufulu wawo.”

Apa n’zoonekeratu kuti anthu asintha maganizo awo pazinthu zimene amaona kuti “n’zoyenera” ndi zimene amaona kuti ndi “tchimo.” N’chifukwa chiyani anthu asintha chonchi? N’chifukwa chiyani anthu asiya kuopa kuchita tchimo? Kodi zili ndi ntchito ngati inuyo maganizo anu asintha pa nkhaniyi kapena ayi?