Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafuta a Basamu wa ku Gileadi Ndi Ochiritsa

Mafuta a Basamu wa ku Gileadi Ndi Ochiritsa

Mafuta a Basamu wa ku Gileadi Ndi Ochiritsa

NKHANI ina yodziwika bwino m’Baibulo ya m’buku la Genesis imanena kuti Yosefe anagulitsidwa ndi abale ake kwa anthu amalonda. Anthu amenewa anali Aisimaeli ndipo anali pa ulendo wopita ku Iguputo. Pa ulendowu amalondawa ankachokera ku Gileadi ndipo ananyamula mafuta a basamu ndi zinthu zina pangamila zawo. (Genesis 37:25) Nkhani yachidule imeneyi imasonyeza kuti mafuta a basamu wa ku Gileadi anali amtengo wapatali kwambiri kwa anthu akale a ku Palesitina ndi madera ena oyandikana nawo chifukwa mafutawa ankagwiritsidwanso ntchito ngati mankhwala.

Komabe, cha m’ma 500 B.C.E., mneneri Yeremiya anafunsa modandaula kuti: “Kodi mulibe mvunguti [basamu] m’Gileadi?” (Yeremiya 8:22) N’chifukwa chiyani Yeremiya anafunsa funso limeneli? Kodi mafuta a basamu anali otani? Kodi masiku ano pali mafuta a basamu amene angachiritse?

Mafuta a Basamu Otchulidwa M’Baibulo

Mafuta a basamu anali onunkhira, opangidwa kuchokera ku utomoni wa zomera zosiyanasiyana. Kale ku Palesitina ndi madera ena oyandikana nawo, mafuta a basamu nthawi zambiri ankagwiritsidwa ntchito ngati zofukizira ndiponso zonunkhiritsa. Mafutawa anali chimodzi mwa zinthu zimene Aisiraeli, atangotuluka kumene ku Iguputo, ankagwiritsa ntchito popanga mafuta opatulika odzozera anthu komanso popanga zofukiza zonunkhira za kuchihema. (Eksodo 25:6; 35:8) Mafuta a basamu anali chimodzi mwa mphatso zapadera zimene mfumukazi ya ku Seba inapereka kwa Mfumu Solomo. (1 Mafumu 10:2, 10) Ndipo kuti Esitere akaoneke wokongola kwambiri kwa Mfumu Ahasiwero ya ku Perisiya, anam’paka mafuta ‘onunkhira bwino [basamu]’ kwa “miyezi isanu ndi umodzi.”​—Estere 1:1; 2:12.

Mafuta a basamu ankachokera m’madera osiyanasiyana oyandikana ndi ku Palesitina, koma tikanena za mafuta a basamu a ku Gileadi, amenewa anali ochokera ku Dziko Lolonjezedwa. Gileadi linali dera la kum’mawa kwa mtsinje wa Yorodano. Yakobo ankaona kuti mafuta a basamu anali “zinthu zamtengo wapatali za dziko” lake ndipo anatumiza mafutawa ngati mphatso ku Iguputo. (Genesis 43:11, NW) Mneneri Ezekieli anatchula mafuta a basamu pa zinthu zimene Ayuda ndi Aisiraeli ankagulitsa ku Turo. (Ezekieli 27:17) Mafuta a basamu anali odziwika bwino chifukwa ankagwiritsidwanso ntchito ngati mankhwala. Mabuku akale kawirikawiri amatchula kuti mafuta a basamu anali ochiritsa, makamaka mabala.

Mtundu Wodwala wa Isiraeli Unafunika Mankhwala a Basamu

Ndiyeno n’chifukwa chiyani Yeremiya anafunsa kuti, ‘Kodi mulibe basamu m’Gileadi’? Kuti timvetse chifukwa chake anafunsa funso limeneli, tiyenera kuona bwinobwino mmene zinthu zinalili ndi mtundu wa Isiraeli panthawi imeneyi. Yeremiya asanafunse funso limeneli, mneneri Yesaya anafotokoza mmene moyo wauzimu wa Isiraeli unawonongekera. Iye anati: “Kuchokera pansi pa phazi kufikira kumutu m’menemo mulibe changwiro; koma mabala, ndi mikwingwirima, ndi zilonda; sizinapole, ngakhale kumangidwa.” (Yesaya 1:6) M’malo mozindikira mmene moyo wawo wauzimu unalili ndiponso kuti anayenera kusintha, mtunduwu unapitirizabe kuchita zoipa. Mpake kuti Yeremiya anadandaula kuti: “Akana mawu a Yehova ali nayo nzeru yotani?” Ngati iwo akanabwerera kwa Yehova, akanawachiritsa. Funso la Yeremiya lakuti, ‘Kodi mulibe basamu m’Gileadi?’ linali lothandiza munthu kuganiza.​—Yeremiya 8:9.

Masiku ano, m’dzikoli muli mavuto ambiri ofanana ndi “mabala, ndi mikwingwirima, ndi zilonda.” Anthu akuvutika ndi umphawi, kupanda chilungamo, kudzikonda, ndiponso kupanda chifundo. Zonsezi zikuchitika chifukwa anthu sakukondanso Mulungu ndiponso anthu anzawo. (Mateyo 24:12; 2 Timoteyo 3:1-5) Anthu ambiri amasalidwa chifukwa cha mtundu wawo, kumene anachokera ndiponso zaka zawo. Kuwonjezera pamenepa, anthu akuvutikanso ndi njala, matenda, nkhondo ndi imfa. Mofanana ndi Yeremiya, anthu ambiri okhulupirika amadzifunsanso ngati mulibe ‘basamu m’Gileadi’ woti apake anthu amene akuvutika ndi mabala auzimu.

Uthenga Wabwino Umachiritsa

M’nthawi ya Yesu, anthu odzichepetsa ankafunsanso funso lomweli ndipo anapeza yankho. Chakumayambiriro kwa chaka cha 30 C.E., Yesu anapita kusunagoge wa ku Nazarete ndipo anawerenga mumpukutu wa Yesaya kuti: “Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mawu abwino kwa ofatsa; iye wanditumiza ndikamange osweka mtima.” (Yesaya 61:1) Kenako Yesu anafotokoza kuti mawu amenewa akunena za iyeyo kuti ndi Mesiya amene ali ndi ntchito yolengeza uthenga wotonthoza anthu.​—Luka 4:16-21.

Nthawi yonse imene Yesu ankachita utumiki, ankalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu mwakhama. (Mateyo 4:17) Pa Ulaliki wa Paphiri, analonjeza anthu ovutika kuti moyo wawo sudzakhala choncho mpaka kalekale. Iye anati: “Osangalala ndinu, amene mukulira tsopano, chifukwa mudzaseka.” (Luka 6:21) Tinganene kuti Yesu ‘anamanga osweka mtima’ mwa kulalikira uthenga wopatsa chiyembekezo wakuti Ufumu wa Mulungu wayandikira.

Mpaka pano, “uthenga wabwino wa ufumu” umatonthoza anthu. (Mateyo 6:10; 9:35) Mwachitsanzo, taganizirani za Roger ndi mkazi wake Liliane. Mu January 1961, anamva koyamba uthenga wabwino wokhudza moyo wosatha umene Mulungu walonjeza, ndipo zimenezi zinawalimbikitsa ngati mmene amachiritsira mafuta a basamu. Liliane anati: “Ndinasangalala moti ndinavina kukhitchini chifukwa cha zimene ndinkaphunzira.” Ndipo Roger, amene panthawiyi anali atafa ziwalo zina kwa zaka 10, anawonjezera kuti: “Ndinasangalala kwambiri ndipo ndinayamba kusangalala ndi moyo chifukwa zimene ndinaphunzira zinandipatsa chiyembekezo. Ndinaphunzira kuti anthu akufa adzauka ndipo sikudzakhalanso zopweteka komanso matenda aliwonse.”​—Chivumbulutso 21:4.

Mu 1970 mwana wawo wamwamuna wazaka 11 anamwalira. Iwo anali ndi chisoni koma sanataye mtima. Anaona kuti Yehova ‘amachiritsa osweka mtima, namanga mabala awo.’ (Salmo 147:3) Chiyembekezo chawo chinawatonthoza. Kwa zaka 50 tsopano, uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu umene ukubwerawo wawathandiza kukhala ndi mtendere wa m’maganizo ndiponso kukhala mosangalala.

Posachedwapa Anthu Onse Adzachira

Nanga kodi masiku ano pali ‘basamu m’Gileadi’? Inde, masiku ano pali mafuta a basamu auzimu. Uthenga wabwino wa Ufumu umatonthoza anthu ndi kuwapatsa chiyembekezo. Zimenezi zili ngati kuchiritsa mitima yosweka. Kodi inunso mukufuna kuchiritsidwa? Zimene muyenera kuchita ndi kulandira uthenga wotonthoza wa m’Mawu a Mulungu kuti uzikutsogolerani pa moyo wanu. Anthu ambiri achita kale zimenezi.

Kuchiritsa kwa mafuta a basamu kumachitira chithunzi mfundo yakuti anthu onse adzachiritsidwa. Nthawi ikuyandikira kwambiri imene Yehova Mulungu ‘adzachiritsa amitundu’ ndipo adzawapatsa moyo wosatha. Panthawi imeneyo, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” Inde, mpaka pano ‘basamu alimobe m’Gileadi.’​—Chivumbulutso 22:2; Yesaya 33:24.

[Chithunzi patsamba 23]

Uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ukupitirizabe kuchepetsa ululu wa anthu osweka mtima masiku ano