Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mudzakhala Wokhulupirika”

“Mudzakhala Wokhulupirika”

Yandikirani Mulungu

“Mudzakhala Wokhulupirika”

2 SAMUELI 22:26, NW

PALI zinthu zochepa chabe zimene zimapweteka kwambiri kuposa mmene zimapwetekera munthu amene timamukhulupirira akatikhumudwitsa. Koma m’dziko lopanda chilungamo lino, sizachilendo kukhumudwitsidwa. (2 Timoteyo 3:1-5) Kodi pali aliyense amene tingamudalire kuti sangatikhumudwitse? Tiyeni tione zimene mfumu Davide ya Aisiraeli inanena pa nkhaniyi.

Davide anachitiridwa zinthu mopanda chilungamo osati masewera. Iye anakakamizika kumakhala moyo wothawathawa chifukwa chozunzidwa ndi Sauli, amene anali mfumu yoyamba ya Aisiraeli komanso munthu wansanje. Ngakhalenso Mikala, yemwe anali mkazi wa Davide, anali wosakhulupirika kwa iye mpaka anayamba ‘kum’peputsa mumtima mwake.’ (2 Samueli 6:16) Komanso Ahitofeli, phungu wodalirika wa Davide, anamupandukira. Kodi anayambitsa chiwembu chimenechi ndani? Mungadabwe kudziwa kuti amene anayambitsa zimenezi ndi Abisalomu, mwana weniweni wa Davide. Popeza anthu amene ankawadalira anamukhumudwitsa, kodi Davide anasiya kukhulupirira munthu aliyense? Kodi anaganiza kuti palibe amene angakhale wokhulupirika kwa iye nthawi zonse?

Timapeza mayankho a mafunso amenewa pa zimene Davide ananena pa 2 Samueli 22:26 (NW). Davide, yemwe anali munthu wa chikhulupiriro cholimba, anaimba nyimbo yandakatulo kwa Yehova Mulungu, kuti: “Kwa munthu wokhulupirika, inunso mudzakhala wokhulupirika.” Davide ankakhulupirira kuti ngakhale anthu atamukhumudwitsa bwanji, Yehova amakhalabe wokhulupirika kwa iye.

Tiyeni tiganizire mofatsa mawu a Davide amenewa. Mawu achiheberi omasuliridwa kuti “mudzakhala wokhulupirika” angatanthauzenso “kuchita zinthu mokoma mtima.” Choncho, munthu wokhulupirikadi amachita zinthu chifukwa cha chikondi ndipo Yehova amakonda anthu amene ali okhulupirika kwa iye. *

Chinanso n’chakuti munthu wokhulupirika samangomva mumtima mwake kuti ndi wokhulupirika koma amachita zinthu zosonyeza kuti ndi wokhulupirika. Yehova amachita zinthu mokhulupirika ndipo Davide anaona yekha kuti mfundo imeneyi ndi yoona. Panthawi imene iye anakumana ndi mavuto aakulu, Yehova anamuthandiza pomuteteza mokhulupirika ndi kumutsogolera. Davide anazindikira kuti Yehova ndi amene anamuteteza ‘pomupulumutsa m’dzanja la adani ake onse.’​—2 Samueli 22:1.

Kodi tikuphunzirapo chiyani pa mawu a Davide amenewa? Tikuphunzira kuti Yehova sasintha. (Yakobe 1:17) Iye amachita zinthu motsatira mfundo zake ndipo amakwaniritsa malonjezo ake mokhulupirika. Mu Salmo lina limene Davide analemba, iye anati: “Yehova . . . sataya okondedwa [okhulupirika ake].”​—Salmo 37:28.

Yehova amasangalala ngati ndife okhulupirika ndiponso tikamamumvera mokhulupirika. Iye amatilimbikitsanso kuti tizichita zinthu mokhulupirika ndi anzathu potengera chitsanzo chake. (Aefeso 4:24; 5:1) Tikamachita zinthu mokhulupirika chonchi, sitingakayikire kuti Yehova adzakhala nafe nthawi zonse. Ngakhale anthu anzathu atatikhumudwitsa, tingadalire Yehova kuti adzatithandiza mokhulupirika kuti tipirire mayesero aliwonse amene tingakumane nawo. Kodi inuyo mukufuna kuyandikira Yehova yemwe ndi “wolungama” kapena kuti wokhulupirika?​—Chivumbulutso 16:5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Lemba la 2 Samueli 22:26 limafanana ndi Salmo 18:25. Baibulo lina linamasulira Salmo limeneli motere: “Inuyo mumamukonda kwambiri munthu wokhulupirika.”​—The Psalms for Today.