Mayankho a Mafunso Anayi Okhudza Kutha kwa Dziko
Mayankho a Mafunso Anayi Okhudza Kutha kwa Dziko
YESU KHRISTU ananeneratu kuti m’tsogolo ‘mapeto adzafika.’ Ponena za nthawi imeneyo, iye anati: “Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha dziko kufikira lerolino, ndipo sichidzachitikanso.”—Mateyo 24:14, 21.
Zimene Yesu ananena komanso nkhani zina za m’Baibulo zokhudza mapeto zimachititsa anthu kufunsa mafunso osiyanasiyana ofunika kuyankhidwa. Mungachite bwino kutsegula Baibulo lanu ndi kuwerenga zimene limayankha pa mafunso amenewo.
1 Kodi Chidzatha N’chiyani?
Baibulo siliphunzitsa kuti dziko lenilenili lidzawonongedwa. Wamasalmo analemba kuti: “[Mulungu] anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka ku nthawi yonse.” (Salmo 104:5) Komanso Baibulo siliphunzitsa kuti zamoyo zonse padziko lapansi zidzawonongedwa ndi moto. (Yesaya 45:18) Zimene Yesu ananena zikusonyeza kuti pali anthu ena amene adzapulumuke. (Mateyo 24:21, 22) Ndiyeno kodi Baibulo limanena kuti chimene chidzathe n’chiyani?
Maboma a anthu adzatha chifukwa alephera kuthetsa mavuto. Mulungu anauzira mneneri Danieli kulemba kuti: “Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.
Nkhondo komanso kuwononga dziko zidzatha. Lemba la Salmo 46:9 limanena zimene Mulungu adzachite, kuti: “Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta ndi moto.” Komanso Baibulo limanena kuti Mulungu ‘adzawononga iwo owononga dziko lapansi.’—Chivumbulutso 11:18.
Anthu ophwanya malamulo ndiponso osachita chilungamo adzatha. M’mawu a Mulungu timapezamo lonjezo lakuti: “Oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, *—Miyambo 2:21, 22.
achiwembu adzazulidwamo.”2 Kodi Mapeto a Zonsezi Adzafika Liti?
Yehova Mulungu ‘anaika nthawi’ imene adzawononge zoipa zonse ndi kukhazikitsa boma la Ufumu wake. (Maliko 13:33) Koma Baibulo limanena momveka bwino kuti sitingathe kudziwiratu tsiku limene mapeto adzafike. Yesu anati: “Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyo 24:36) Komabe Yesu ndi ophunzira ake ananeneratu mmene dziko lapansili lidzakhalire Mulungu asanabweretse mapeto. Ngati zinthu zonse zotsatirazi zikuchitika panthawi imodzi komanso padziko lonse lapansi, ndiye kuti mapeto ali pafupi.
Mavuto obwera chifukwa cha ndale, kuwonongedwa kwa dziko ndiponso kuipa kwa makhalidwe a anthu awonjezereka kuposa kale. Yesu anayankha mafunso a ophunzira ake okhudza mapeto powauza kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu wina, kudzakhala zivomezi m’malo osiyanasiyana, kudzakhala njala. Zimenezi ndi chiyambi cha masautso, ngati mmene zimayambira zopweteka za kubereka.” (Maliko 13:8) Kenako mtumwi Paulo analemba kuti: “Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, opanda chikondi chachibadwa, osagwirizanitsika, odyerekeza, osadziletsa, owopsa, osakonda zabwino, achiwembu, aliuma, otukumuka chifukwa cha kunyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.”—2 Timoteyo 3:1-5.
Ntchito yolalikira ikuchitika mu zinenero zosiyanasiyana padziko lonse. Yesu anati: “Ndipo uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse; kenako mapeto adzafika.”—Mateyo 24:14.
3 Kodi Kenako Chidzachitika N’chiyani?
Baibulo silinena kuti anthu onse adzatengedwa padziko lapansi n’kumakakhala mosangalala kumwamba mpaka kalekale. Yesu anaphunzitsa kuti zimene Mulungu ankafuna kuchitira anthu poyambirira zidzakwaniritsidwa. Iye anati: “Osangalala ali iwo amene ali ofatsa, popeza adzalandira dziko lapansi.” (Mateyo 5:5; 6:9, 10) Baibulo limalonjeza kuti anthu amene adzamwalire mapeto asanafike, adzaukitsidwa. (Yobu 14:14, 15; Yohane 5:28, 29) Koma kodi kenako chidzachitika n’chiyani Mulungu akadzawononga anthu oipa?
Yesu adzalamulira ali kumwamba monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu Mneneri Danieli analemba kuti: “Ndinaona m’masomphenya a usiku, taonani anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu [Yesu ataukitsidwa], nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe [Yehova Mulungu]; ndipo anam’yandikizitsa pamaso pake. Ndipo [Yehova Mulungu] anam’patsa [Yesu] ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, am’tumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzawonongeka.”—Danieli 7:13, 14; Luka 1:31, 32; Yohane 3:13-16.
Anthu olamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu adzakhala athanzi labwino, otetezeka nthawi zonse, ndiponso adzakhala ndi moyo wosatha. Mneneri Yesaya analemba kuti: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya.” (Yesaya 65:21-23) Mtumwi Yohane analemba zimene zidzachitike nthawi imeneyo kuti: “Taonani! chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Inde, Mulungu mwini adzakhala nawo. Iye adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
4 Kodi Tiyenera Kuchita Chiyani Kuti Tidzapulumuke Anthu Oipa Akamadzawonongedwa?
Mtumwi Petulo anafotokoza kuti anthu ena amene akukhala m’nthawi ya mapeto azidzaseka anthu amene amakhulupirira kuti Mulungu adzathetsa mavuto a anthu ndiponso kuti adzawononga anthu oipa padziko lapansi. (2 Petulo 3:3, 4) Petulo anatilimbikitsa kuti tiyenera kuchita zotsatirazi.
Tiphunzirepo kanthu pa zimene zinachitika kale. Petulo analemba kuti Mulungu “anaperekanso chilango pa dziko lakale lija osalilekerera, koma anasunga Nowa, mlaliki wa chilungamo, pom’pulumutsa pamodzi ndi ena asanu ndi awiri, pamene anabweretsa chigumula pa dziko la anthu osaopa Mulungu.” (2 Petulo 2:5) Ponena za anthu amene adzanyoze, Petulo anati: “Mwakufuna kwawo, amalephera kuzindikira mfundo iyi yakuti, kunali miyamba kuchokera kalekale, ndipo mwa mawu a Mulungu, dziko lapansi linali loumbika motsendereka pamwamba pa madzi ndi pakati pa madzi; ndipo mwa zimenezi, dziko la panthawiyo linawonongeka pamene linamizidwa ndi madzi. Ndipo mwa mawu amodzimodziwo, miyamba imene ilipo tsopano limodzi ndi dziko lapansi *, azisungira moto m’tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.”—2 Petulo 3:5-7.
Khalani ndi makhalidwe amene Mulungu amasangalala nawo. Petulo analemba kuti anthu amene akufuna kudzapulumuka, ayenera kukhala ndi ‘khalidwe loyera ndiponso [kusonyeza] ntchito za kudzipereka kwa Mulungu.’ (2 Petulo 3:11) Palembali, Petulo akunena kuti chofunika kwambiri ndi “khalidwe loyera” ndiponso kusonyeza ‘ntchito za kudzipereka kwa Mulungu.’ Choncho munthu sadzapulumuka chifukwa chongonena kuti amakhulupirira Mulungu, kapena chifukwa chongosintha zina ndi zina pa moyo kungoti apulumuke.
Kodi Mulungu amafuna kuti tizikhala ndi khalidwe lotani komanso tizichita ntchito zotani? Mungachite bwino kuyerekeza zimene mumadziwa pa mafunso amenewa ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukuthandizani. Afunseni mafunso ndipo apempheni kuti akuonetseni mayankho awo m’Baibulo lanu. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti musamaope kuti dziko lapansili lidzatha, ngakhale kuti pali zinthu zambiri zoopsa zimene zikuchitika masiku ano.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 Onaninso nkhani yakuti “Kodi Anthu Onse Ali ndi Mwayi Wophunzira za Mulungu?” patsamba 22 m’magazini ino.
^ ndime 19 Pamenepa, Petulo sanali kunena za dziko lapansi lenilenili. Mose, yemwe analemba nawo Baibulo, anagwiritsanso ntchito mawu akuti “dziko lapansi” mophiphiritsa. Iye anati: “Dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi.” (Genesis 11:1) Dziko lapansi lenilenili si limene limalankhula “chinenedwe chimodzi.” Mofananamo, si dziko lenilenili limene lidzawonongedwe. M’malo mwake, mogwirizana ndi zimene Petulo ananena, amene adzawonongedwe ndi anthu osaopa Mulungu.
[Mawu Otsindika patsamba 7]
Dziko lenilenili silidzatha, m’malo mwake anthu amene amaliwononga ndi amene adzathe