Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mmisiri wa Matabwa”

“Mmisiri wa Matabwa”

Moyo wa Akhristu a M’nthawi ya Atumwi

“Mmisiri wa Matabwa”

“Kodi si mwana wa mmisiri wa matabwa uyu?”​—MATEYO 13:55.

YESU sanali kungodziwika monga “mwana wa mmisiri wa matabwa,” koma anali kudziwikanso kuti iyeyo ndi “mmisiri wa matabwa.” (Maliko 6:3) Iye ayenera kuti anaphunzira ntchito imeneyi kwa Yosefe, amene anali bambo ake omulera.

Kodi Yesu anafunikira kuphunzira luso lotani kuti akhale mmisiri wa matabwa? Nanga ankagwiritsa ntchito zipangizo zotani? Kodi iye ankapanga zinthu zotani, ndipo ankagwira ntchito zotani ku Nazareti? Kodi ntchito ya umisiri wa matabwa imene anaiphunzira ali mnyamata inamuthandiza bwanji atakula?

Ntchito Yophunzira kwa Makolo Chithunzi chimene chili m’munsichi chikusonyeza bambo akuphunzitsa mwana wawo wamkulu mmene angagwiritsire ntchito dirilu yoboolera matabwa. Mng’ono wake akuonerera komanso akumvetsera mwatcheru.

Kawirikawiri, anyamata ankayamba kuphunzira ntchitoyi atakwanitsa zaka pakati pa 12 ndi 15 ndipo nthawi zambiri bambo awo ndi amene ankawaphunzitsa. Maphunziro amenewa ankatenga zaka zambiri, ndipo anyamatawo ankayenera kuyesetsa mwakhama kwambiri kuti akhale akatswiri. Yosefe ayenera kuti nthawi zambiri ankakhala limodzi ndi Yesu. Ankagwira naye ntchito limodzi, kulankhulana naye ndiponso kumuthandiza kuti aidziwe bwino ntchitoyo. Iye ayenera kuti ananyadira kwambiri kuona Yesu akukhala katswiri pa ntchito yake monga mmisiri wa matabwa.

Ntchito Yofunika Luso, Mphamvu, ndi Nzeru Mmisiri wa matabwa ankafunika kudziwa mtundu wa matabwa amene akugwiritsa ntchito. Mmisiri anali kugwiritsa ntchito mitengo yosavuta kupeza m’dera lawolo monga paini, mkungudza, mkuyu, olivi ndi mtengo wina wofanana ndi m’bawa. Komabe, m’nthawi ya atumwi, kunalibe mafakitale odula matabwa pamakina kapena masitolo ogulitsa zinthu zomangira nyumba. Choncho zinali zovuta kuti mmisiri apeze matabwa asaizi imene akufuna ngati mmene zilili masiku ano m’madera ambiri. M’malo mwake, mmisiri wa matabwa ankalowa m’nkhalango, kusankha mitengo yabwino, kuigwetsa, kenako n’kuinyamula, ngakhale kuti inkakhala yolemera kwambiri. Mitengoyi amapita nayo kumalo ake ogwirira ntchito.

Kodi matabwawo ankapangira chiyani? Nthawi zambiri anali kumangira nyumba za anthu. Iye ankacheka matabwawo kuti akhale mtanda wa denga la nyumba. Matabwa ena ankapangira masitepe a m’kati mwa nyumba ndipo ena ankapangira zitseko ndi mawindo.

Mmisiri wa matabwa ankapanganso zinthu za m’nyumba. Zithunzi zili m’munsizi zikusonyeza zina mwa zinthu zimenezo. Ankapanga makabati okhala ndi madilowa, mashelefu kapena zitseko (1), timipando tating’ono (2), mipando (3), ndi matebulo (4). Zonsezi zinkakhala zamasaizi osiyanasiyana ndiponso zopangidwa mosiyanasiyana. Komanso ankatha kupanga timabedi ta ana. Pofuna kuti zinthu zina zimene mmisiriyo wapanga zizioneka zokongola, ankaika timatabwa tokongoletsa tooneka mosiyanasiyana. Ndiponso kuti zimene wapanga zisawonongeke msanga komanso kuti zikongole, ankazipaka phula, vanishi, kapena mafuta.

Mmisiri wa matabwa ankapanganso zipangizo za alimi monga magoli (5) opangidwa ndi matabwa olimba kwambiri, makasu amanomano, mareki ndiponso mafosholo (6). Iye anafunikanso kupanga mapulawo (7) olimba kwambiri, okhala ndi mano achitsulo chifukwa nthaka yake inali yamiyala. Ankapanganso ngolo zamatabwa (8) zokhala ndi mateyala ndipo ena mwa mateyalawa ankakhala ndi masipokosi. Mmisiri wa matabwa anali kukonzanso zinthu zimenezi zikawonongeka.

Mutha kuona m’maganizo mwanu mmene Yesu ankaonekera chifukwa cha ntchito imene ankagwira. Ayenera kuti nkhope yake ndi mikono yake inali yodera chifukwa cha kutentha kwa dzuwa la ku Palesitina. Ayeneranso kuti anali wamphamvu chifukwa chogwira ntchito yolimba imeneyi kwa zaka zambiri. Komanso mwina zikhato za m’manja mwake zinali zokhakhala chifukwa chonyamulanyamula matabwa, kugwetsa mitengo ndi nkhwangwa, kukhoma zinthu ndi hamala, komanso kucheka matabwa.

Ena mwa mafanizo ake anali ogwirizana ndi ntchito yake Pophunzitsa mfundo zozama za choonadi, Yesu ankagwiritsa ntchito zinthu zosavuta kumva komanso zodziwika kwa aliyense. Koma kodi ananenapo mafanizo okhudzana ndi umisiri wa matabwa? Taganizirani mafanizo awa: “N’chifukwa chiyani umayang’ana kachitsotso m’diso la m’bale wako, koma osaganizira mtanda wa denga umene uli m’diso lako?” N’kutheka kuti iye ananena zimenezi chifukwa monga mmisiri wa matabwa, ankadziwa kuti mtanda wa denga umakhala waukulu kwambiri. (Mateyo 7:3) Kenako, Yesu anauza gulu lina la anthu kuti: “Aliyense wogwira pulawo koma akuyang’ana zinthu za m’mbuyo sayenera ufumu wa Mulungu.” Mawu amenewa akusonyeza kuti mwina Yesu anapangapo mapulawo. (Luka 9:62) Ena mwa mawu okhudza mtima kwambiri amene Yesu ananenapo anali onena za chipangizo chinachake chopangidwa ndi mmisiri wa matabwa. Iye anati: “Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine.” Kenako ananena kuti: “Goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mateyo 11:29, 30) Mosakayikira, Yesu ankadziwa kupanga goli losaperepesa pakhosi limene linali “lofewa” kapena kuti lokwana bwino pakhosi.

Mwina anthu amene ankadana ndi Yesu anagwiritsa ntchito mawu akuti “mwana wa mmisiri wa matabwa” pofuna kumunyoza. Ngakhale zili choncho, Akhristu masiku ano, monga mmenenso zinalili m’nthawi ya atumwi, amaona kuti ndi mwayi waukulu kukhala otsatira a Yesu, amene nthawi ina anali mmisiri wa matabwa.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 26]

Zipangizo za Mmisiri wa Matabwa

M’nthawi ya Yesu, mmisiri wa matabwa ankafunika kudziwa mmene angagwiritsire ntchito zipangizo zotsatirazi. Anali kugwiritsa ntchito macheka (1) amene anali mpeni wamanomano wokhala ndi chigwiriro chathabwa. Chifukwa cha mmene mano ake analili, macheka amenewa anali kudula thabwa powakokera m’mbuyo. Mmisiri wa matabwa ankagwiritsa ntchito sikweya (2) poyeza zimene akukhoma. Ankagwiritsanso ntchito pulameti kapena kuti chingwe (3) poyeza kuwongoka kwa zinthu zimene akupanga. Zinanso zimene ankagwiritsa ntchito ndi levulo (4), ndodo yoyezera kutalika kwa zinthu (5), puleni yopalira matabwa kuti asalale. Puleni imeneyi inkakhala ndi mpeni wakuthwa kumunsi kwake ndipo ankatha kuutalikitsa kapena kuufupikitsa (6). Iye ankagwiritsanso ntchito nkhwangwa (7) pogwetsa mitengo.

Mmisiri wa matabwa ankakhalanso ndi makina opangira maguluvu (8). Makina amenewa kuti aziyenda ankawapukusa ndi chinthu chooneka ngati uta. Popanga maguluvuwo, ankagwiritsanso ntchito chipangizo chooneka ngati tchezulo (9). Muthanso kuona kuti pamwamba pa chotsekera bokosi losungiramo zipangizo pali maleti, kapena kuti hamala yathabwa (10), imene ankaigwiritsa ntchito kukhomera zisonga zimene amazikhoma molumikizira. Ankagwiritsanso ntchito hamala imeneyi pogoba thabwa ndi tchezulo. Palinso chochekera chamanomano chooneka ngati mpeni (11), komanso pali mpeni wopalira matabwa wokhala ndi zigwiriro mbali zonse ziwiri (12) umene ankagwiritsa ntchito popalira matabwa. Pabokosipo palinso misomali (13). Kutsogolo kwa bokosili kuli hamala yachitsulo (14), ndi kasemasema (15) wosemera matabwa. Pachotsekeracho palinso mpeni (16) komanso matchezulo (17) osiyansiyana. Chimene chatsamira bokosicho ndi choboolera (18) chimene chinkazungulira pochiyendetsa ndi chinthu chooneka ngati uta.