Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mulungu Alibe Tsankho

Mulungu Alibe Tsankho

Zoti Achinyamata Achite

Mulungu Alibe Tsankho

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a m’nkhaniyi akumvera mumtima mwawo.

Amene akutchulidwa kwambiri m’nkhaniyi: Koneliyo ndi Petulo.

Chidule cha nkhaniyi: Petulo anatsatira chitsanzo cha Mulungu polalikira mopanda tsankho kwa Koneliyo amene sanali Myuda.

1 ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI MACHITIDWE 10:1-35, 44-48.

Kodi mukuganiza kuti Koneliyo ankaoneka bwanji? Fotokozani.

․․․․․

Mogwirizana ndi zimene zinalembedwa pamavesi 3 mpaka 6, kodi mukuganiza kuti Koneliyo ankamva bwanji pamene ankalankhulana ndi mngelo?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti Koneliyo anakambirana zotani ndi antchito ake, mogwirizana ndi zimene mavesi 7 ndi 8 akunena?

․․․․․

2 FUFUZANI MOZAMA.

N’chifukwa chiyani masomphenya amene Mulungu anapatsa Petulo m’mavesi 10 mpaka 16 anamuthandiza kusintha maganizo ake? (Zokuthandizani: Ganizirani zimene Petulo ankaganiza poyamba chifukwa chakuti anali Myuda, malinga ndi zimene vesi 14 likunena.)

․․․․․

Kodi mukuona khalidwe liti la Koneliyo mu vesi 25? N’chifukwa chiyani anthu ambiri amene ali ndi udindo sakhala ndi khalidwe limeneli? (Zokuthandizani: Onani vesi 1.)

․․․․․

Pogwiritsa ntchito mabuku ofufuzira amene muli nawo, fufuzani kuti mudziwe kuchuluka kwa gulu la asilikali a Italiya limene Koneliyo ankaliyang’anira.

․․․․․

N’chifukwa chiyani mfundo yoti Koneliyo anakhala Mkhristu ndi yochititsa chidwi?

․․․․․

3 GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA ZOKHUDZA . . .

Kugwiritsa ntchito mafanizo mogwira mtima.

․․․․․

Kupanda tsankho kwa Mulungu.

․․․․․

Zimene inuyo mungachite kuti mupewe kuchita zinthu mwatsankho.

․․․․․

4 M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ITI IMENE YAKUKHUDZANI MTIMA KWAMBIRI, NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․

NGATI MULIBE BAIBULO, MUNGAWERENGE LA PA INTANETI PA WEBUSAITI YATHU YA www.pr418.com.