Muzitonthoza Anthu Amene Aferedwa, Ngati Mmene Yesu Anachitira
Muzitonthoza Anthu Amene Aferedwa, Ngati Mmene Yesu Anachitira
MUNTHU wina dzina lake Lazaro ankakhala ku Betaniya ndipo tsiku lina anadwala kwambiri. Alongo ake, Marita ndi Mariya amene ankacheza kwambiri ndi Yesu, anatuma anthu ena kwa Yesu, kuti akamuuze za matendawo. Koma matenda a Lazaro anakula ndipo anamwalira. Lazaro ataikidwa m’manda, anzawo komanso achibale a Marita ndi Mariya anabwera “kudzawatonthoza.” (Yohane 11:19) Kenako Yesu anafika ku Betaniya ndipo anapita kukaona Marita ndi Mariya. Kuganizira zimene iye ananena ndiponso zimene anachita ali kumeneko, kutithandiza kuphunzirapo zimene tingachite potonthoza anthu amene aferedwa.
Kukawaona Kumasonyeza Kuti Mumawaganizira
Kuti akafike ku Betaniya, Yesu anayenda masiku awiri. Pa ulendowu, anawoloka Mtsinje wa Yorodano komanso anayenda msewu wa zitunda ndiponso wokhotakhota wochokera ku Yeriko. Yesu atangofika mumzindawu, Marita anathamanga kukakumana naye. Kenako Mariya atamva kuti Yesu wafika, nayenso anathamanga kukakumana naye. (Yohane 10:40-42; 11:6, 17-20, 28, 29) N’zosakayikitsa kuti kubwera kwa Yesu kunalimbikitsa kwambiri Marita ndi Mariya amene anali achisoni kwambiri.
N’chimodzimodzinso masiku ano. Anthu amene aferedwa amalimbikitsidwa kwambiri tikapita kukawaona. Mwachitsanzo, Scott ndi mkazi wake Lydia anali ndi chisoni pamene Theo, mwana wawo wa mwamuna wazaka 6, anamwalira pangozi. Iwo ananena kuti: “Tinkafunitsitsa kuti abale athu komanso anzathu atithandize ndipo iwo anabweradi pakati pa usiku kuchipatala kumene tinali.” Kodi odzawaonawo ananena chiyani? Scott ndi Lydia ananena kuti: “Pa nthawi imeneyi sitinkafuna kuuzidwa mawu aliwonse, kubwera kwawo kokhako kunatithandiza kwambiri ndipo kunasonyeza kuti amatiganizira.”
Baibulo limanena kuti pamene Yesu anaona anthu akulira maliro a Lazaro, nayenso ‘anamva chisoni’ ndipo “anagwetsa misozi.” (Yohane 11:33-35,38) Yesu sanatsatire mfundo yakuti, mwamuna salira. Mofanana ndi oferedwawo, iyenso anamva ululu mumtima mwake ndipo ankaonanso kuti waferedwa. Kodi pamenepa tikuphunzirapo chiyani? mukapita kukaona anthu amene aferedwa, musamachite manyazi kulira. (Aroma 12:15) Komabe musakakamizike kuchita zinthu zochititsa kuti oferedwawo agwetse misozi. Ena zimawavuta kulira pagulu koma amalira pamene ali kwa okha.
Muziwamvetsera Mwachifundo
N’kutheka kuti Yesu anali ndi mawu amene akanatha kunena polimbikitsa Marita ndi Mariya, koma iye anasiya dala osalankhula n’cholinga choti ayambe ndiwo kulankhula. (Yohane 11:20, 21, 32) Komanso pamene analankhula ndi Marita, anamufunsa funso kenako anakhala chete n’kumamvetsera pamene Maritayo anali kulankhula.—Yohane 11:25-27.
Tikamamvetsera mwachidwi wina akamalankhula timasonyeza kuti tikumuganizira. Choncho kuti muthe kutonthoza munthu amene waferedwa, mufunika kumvetsera kwambiri pamene munthuyo akulankhula. Ndipo mungasonyeze kuti mukumvetsera pofunsa mafunso amene angachititse woferedwa kufotokoza zakukhosi kwake. Komabe muyenera kusamala kuti musawakakamize kulankhula ngati iwo sakufuna. N’kutheka kuti mwina atopa ndipo akufuna kupuma.
Nthawi zina munthu amene waferedwa angamasowe chonena, mwinanso angamangobwereza zimene wanena kale. Koma ena savutika kufotokoza zakukhosi kwawo. Mariya komanso Marita anauza Yesu kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalira.” (Yohane 11:21, 32) Kodi pamenepa Yesu anachita chiyani? Anamvetsera modekha ndiponso mwachifundo. Iye sanawadzudzule chifukwa chonena zakukhosi kwawo. Yesu ankadziwa bwino kuti munthu amene waferedwa amakhala ndi chisoni kwambiri komanso amawawidwa mtima.
Mukapita kukatonthoza woferedwa ndipo mukusowa chonena, munganene kuti, “Kodi mungandifotokozere zimene zinachitika?” Kenako mvetserani pamene iye akufotokoza. Muziganizira zimene iye akufotokozazo ndipo muzimuyang’ana akamalankhula ndipo yesetsani kumvetsa mmene iye akumvera.
Komabe kumvetsa mmene munthu amene waferedwa akumvera, n’kovuta. Lydia amene tamutchula poyamba uja, ananena kuti: “Pa nthawi imene tinaferedwa zinthu zinasintha kwambiri. Nthawi zina tinkalephera kudzigwira ndipo tinkangolira anthu akabwera kudzationa. Chomwe tinkafuna pa nthawiyo ndi choti ena amvetse mmene tikumvera ndipo anzathu anayesetsa kuchita zimenezo.”
Popeza Yesu anali wangwiro, anatha kumvetsa bwinobwino mmene Mariya ndi Marita ankamvera. Iye ankadziwa kuti aliyense wa iwo anali ndi “mliri wake ndi ululu wake.” (2 Mbiri 6:29) Zimene Yesu anayankha Marita atamulonjera, zinali zosiyana ndi zimene anamuyankha Mariya. Popeza Marita anapitiriza kulankhula, Yesu anapitirizanso kulankhula naye. Koma Yesu sanalankhule ndi Mariya kwa nthawi yaitali chifukwa choti panthawiyi Mariyayo ankangolira. (Yohane 11:20-28, 32-35) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Mungachite bwino kuchita zinthu zimene zingachititse kuti woferedwayo azilankhula kwambiri pamene mukucheza naye. Mukamamvetsera mwachidwi pamene iye akufotokoza mmene akumvera, zimamutonthoza kwambiri.
Mawu Olimbikitsa
Pamene Mariya ndi Marita anauza Yesu kuti, “mukanakhala kuno,” iye sanakhumudwe kapena kuwaimba mlandu chifukwa cha mawu amenewa. Iye anangomutsimikizira Marita kuti: “Mlongo wako adzauka.” (Yohane 11:23) Ndi mawu achidule koma okoma mtima amenewa, Yesu anathandiza Maritayo kukhazikitsa mtima pansi komanso anamukumbutsa kuti pali chiyembekezo choti Lazaro adzauka.
Mukamalankhula ndi munthu amene waferedwa, musaiwale kuti mawu abwino, ngakhale atakhala achidule, angamulimbikitse kwambiri. Mungathe kunena kapena kulemba mawu olimbikitsa amene mukufuna kuuza woferedwa. Munthu amatonthozedwa kwa nthawi yaitali ngati mwamulembera kalata kapena khadi chifukwa akhoza kudzawerenganso zimene munalembazo. Mwachitsanzo, patapita miyezi 9 Bob mwamuna wa Kath atamwalira, Kath anawerenganso makhadi onse amene anthu anamulembera. Iye anati: “Ndinaona kuti zimene zinali m’makhadiwo, zinandithandiza kwambiri kuposa mmene zinandithandizira poyamba. Pamenepa ndi pamene ndinaona kuti ndatonthozedwadi.”
Kodi mungalembe chiyani m’kalata kapena khadi yopepesa munthu amene waferedwa? Mukhoza kulemba za munthu womwalirayo, zimene munachitira naye limodzi kapena khalidwe labwino limene anali nalo. Kath ananena kuti: “Mawu oyamikira khalidwe la Bob anandichititsa kumwetulira komanso kufuna kulira. Nkhani zoseketsa za zimene Bob ankachita zinandiseketsa ndiponso kundikumbutsa nthawi imene ineyo ndi iye tinkasangalalira limodzi. Makhadi ambiri amene anthu anatitumizira anali ndi mavesi a m’Baibulo ndipo makhadi amenewa amandilimbikitsa kwambiri.”
Mmene Mungathandizire
Zimene Yesu anachitira banja la Lazaro ndi zoti ifeyo sitingathe kuchita. Iye anaukitsa Lazaro. (Yohane 11: 43, 44) Komabe ifenso tikhoza kuchitira munthu amene waferedwa zinthu zina zimene tingathe. Zinthu zimenezi ndi monga kumuphikira chakudya, kukonza malo ogona anthu amene abwera, kumuchapira, kusamalira ana, kukamugulira zinthu zofunika kapenanso kuthandiza pa nkhani ya thiransipoti. N’zosakayikitsa kuti woferedwayo angayamikire zinthu zimene tingamuchitire chifukwa choti timamukondadi mochokera pansi pa mtima, ngakhale zitakhala zochepa.
Tizikumbukiranso kuti munthu amene waferedwa angafune kuti nthawi ina akhale payekha. Komabe mungayesetse kupeza nthawi yoyenera yoti muzilankhula naye. Mayi wina amene anaferedwapo ananena kuti: “Chisoni chilibe malire ndipo simungadziwe kuti chisoni cha munthuyo chidzatha liti.” Anthu ena amakalimbikitsa anthu amene anaferedwa pa zochitika ngati pa tsiku lawo laukwati kapena tsiku limene m’bale wawoyo anamwalira. Kuchita zimenezi kungasonyeze kuti ndinu bwenzi lenileni ngakhale pa nthawi yamavuto.—Miyambo 17:17.
Potonthoza ophunzira ake, Yesu anawauzanso za chiyembekezo chakuti akufa adzauka. Iye anati: “Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo akupumula, koma ndikupita kumeneko kukamudzutsa ku tulo take.” (Yohane 11:11) Ndi mawu amenewa Yesu anatsimikizira otsatira ake kuti akufa adzauka. Iye anafunsa Marita kuti: “Kodi ukukhulupirira zimenezi?” Marita anayankha kuti: “Inde, Ambuye.”—Yohane 11:24-27.
Kodi inuyo mumakhulupirira kuti Yesu adzaukitsadi anthu amene anamwalira? Ngati mumakhulupirira, mungachite bwino kuuzako anthu amene aferedwa za chiyembekezo chimenechi. Yesetsani kuwathandiza. Dziwani kuti mawu ndiponso zochita zanu zingatonthoze anthu amene aferedwa.—1 Yohane 3:18.
[Mapu patsamba 9]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
PEREYA
Mtsinje wa Yorodano
Yeriko
Betaniya
Nyanja Yamchere
Yerusalemu
SAMARIYA