Pewani Kudziyerekezera ndi Ena
Mfundo Yachiwiri
Pewani Kudziyerekezera ndi Ena
ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: “Aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake, osati modziyerekezera ndi munthu wina.”—Agalatiya 6:4.
N’CHIFUKWA CHIYANI ZIMENEZI ZIMAKHALA ZOVUTA? Anthu amakonda kudziyerekezera ndi ena. Nthawi zina amadziyerekezera ndi anthu amene ali ndi zinthu zochepa poyerekeza ndi iwo. Koma nthawi zambiri amadziyerekezera ndi anthu amene ali ndi mphamvu zambiri, chuma kapena luso kuposa iwowo. Kaya munthu adziyerekezera ndi anthu otani, zotsatirapo zake zimakhala zoipa. Anthu ambiri amaganiza kuti munthu amakhala wofunika kwambiri ngati ali ndi chuma kapena luso linalake. Koma zimenezi sizoona. Kudziyerekezera ndi ena kungachititse munthu kuyamba nsanje komanso kukhala ndi mzimu wampikisano.—Mlaliki 4:4.
ZIMENE MUNGACHITE: Yesetsani kumadziona ngati mmene Mulungu amakuonerani. Lolani kuti zimene zimamuchititsa Mulungu kukuonani kuti ndinu ofunika, zizikuchititsaninso inuyo kudziona choncho. Baibulo limati: “Mmene munthu amaonera si mmene Mulungu amaonera. Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova * amaona mmene mtima ulili.” (1 Samueli 16:7) Yehova satiyerekezera ndi ena kuti aone ngati ndife ofunika. M’malomwake iye amaona kuti ndife ofunika poona mumtima mwathu, malingaliro athu, mmene tikumvera komanso zolinga zathu. (Aheberi 4:12, 13) Yehova amadziwa kuti pali zimene sitingathe kuchita ndipo amafuna kuti nafenso tidziwe zimenezo. Mukamaganiza kuti ndinu ofunika chifukwa chodziyerekezera ndi anthu ena, mudzakhala odzikuza, apo ayi osakhutira ngakhale pang’ono ndi zimene muli nazo. Choncho vomerezani modzichepetsa kuti simungathe kuchita bwino pa chilichonse.—Miyambo 11:2.
Komano kodi mungatani kuti Mulungu adzikuonani kuti ndinu wofunika kwambiri? Iye anauzira mneneri Mika kulemba kuti: “Iwe munthu wochokera kufumbi, iye anakuuza zimene zili zabwino. Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo, ukhale wokoma mtima ndiponso uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.” (Mika 6:8) Mukamatsatira malangizo amenewa, Mulungu adzayamba kuona kuti ndinu wofunika kwambiri. (1 Petulo 5:6, 7) Chimenechi ndi chifukwa chachikulu chokuchititsani kukhala wokhutira.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Dzina la Mulungu limene limapezeka m’Baibulo.
[Chithunzi patsamba 5]
Yehova amaona kuti ndife ofunika mwa kuona zimene zili mumtima mwathu