Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pezani Zosowa Zanu Zauzimu

Pezani Zosowa Zanu Zauzimu

Mfundo Yachisanu

Pezani Zosowa Zanu Zauzimu

ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”​—Mateyu 5:3.

N’CHIFUKWA CHIYANI ZIMENEZI ZIMAKHALA ZOVUTA? Pali zipembedzo zambirimbiri zimene zimaphunzitsa zinthu zosiyana kwambiri pa nkhani ya zimene tingachite kuti tipeze zosowa zathu zauzimu. Kodi mungadziwe bwanji chipembedzo chimene chimaphunzitsa zoona ndiponso chimene chimakondweretsadi Mulungu? Anthu ena otchuka olemba mabuku amanena kuti kukhulupirira Mulungu ndiponso kudzipereka kwa iye, n’kosathandiza komanso n’koopsa. Magazini ina inanena mwachidule zimene munthu wina wotchuka kwambiri amene sakhulupirira kuti kuli Mulungu ananena. Magaziniyo inati: “Zimene Akhristu amakhulupirira, zonena kuti pali chinachake choposa sayansi komanso nzeru za anthu, . . . zimachititsa kuti moyo uzioneka otchipa kwambiri komanso zimachititsa kuti anthu azichita zachiwawa.”

ZIMENE MUNGACHITE: Fufuzani umboni wosonyeza kuti kuli Mulungu. (Aroma 1:20; Aheberi 3:4) Musalole kuti winawake akufooketseni kupeza mayankho amafunso ofunika kwambiri monga akuti: N’chifukwa chiyani tili ndi moyo? N’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri chonchi? Kodi Mulungu amafuna kuti ndizichita chiyani? Kupeza mayankho ogwira mtima a mafunso amenewa kudzakuthandizani kukhala okhutira.

Komabe musamangokhulupirira zilizonse zimene anthu ena akuuzani. Mawu a Mulungu amatilimbikitsa “kugwiritsa ntchito luntha la kuganiza” kuti tizindikire zimene iye amaona kuti n’zoyenera. (Aroma 12:1, 2) Mudzadalitsidwa kwambiri chifukwa cha khama lanu pa nkhani imeneyi. Mukamaphunzira Baibulo ndiponso kutsatira zimene mukuphunzirazo pa moyo wanu, mudzapewa mavuto ambiri, mudzachepetsa nkhawa ndiponso mudzakhala osangalala kwambiri. Zimenezi sinkhambakamwa ayi. Anthu ambirimbiri azikhalidwe zosiyanasiyana apindula kale chifukwa chophunzira zenizeni zokhudza Mulungu komanso zolinga zake. Mwachitsanzo tawerengani nkhani zonena za anthu amene apindula kwambiri chifukwa chophunzira Baibulo, pamasamba 18 mpaka 21 a magazini ino.

Mukamagwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo, mudzakhala wodzipereka kwambiri kwa Mulungu. Mungachite bwino kwambiri kuyamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Mukachita zimenezi, mudzagwirizana ndi mawu a mtumwi Paulo akuti: “Kukhala wodzipereka kwa Mulungu . . . limodzi ndi kukhala wokhutira ndi zimene tili nazo, ndi njiradi yopezera phindu lalikulu.”​—1 Timoteyo 6:6.

[Chithunzi patsamba 8]

Zindikirani zimene Mulungu amaona kuti n’zoyenera