Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Amagi amene anapita kukaona Yesu ali mwana anali ndani?

Malinga ndi nkhani yonena za kubadwa kwa Yesu, yopezeka mu Uthenga Wabwino wa Mateyo, anthu ena ochokera “kumadera a kum’mawa” anaona nyenyezi yosonyeza kuti kwabadwa mfumu yatsopano. Choncho iwo anapita kukapereka mphatso kwa Yesu ali mwana. M’Chigiriki anthu amenewa amatchedwa kuti maʹgoi kapena kuti amagi. (Mateyu 2:1) Kodi anthu amenewa anali ndani kwenikweni?

Munthu woyambirira kunenapo zoona pa nkhani ya amagi ndi katswiri wina wa ku Greece wolemba mbiri yakale dzina lake Herodotus, yemwe anakhalako cha m’ma 400 B.C.E. Iye analemba kuti Amagi anali m’gulu la ansembe a ku Perisiya omwe anali akatswiri pa nkhani yokhulupirira nyenyezi, kumasulira maloto ndiponso kuombeza. Nthawi imeneyi chipembedzo cha anthu a ku Perisiya chinali Chizorowasita ndipo Amagi amene Herodotus anawatchula anali ansembe achipembedzochi. Buku lina loikila ndemanga nkhani za m’Baibulo linanena kuti: “Tinganene kuti a mágos kapena kuti okhulupirira nyenyezi a ku Girisi anali ndi nzeru zodabwitsa ndipo nthawi zina ankachita zamatsenga.”​—The International Standard Bible Encyclopedia.

Ena mwa anthu oikira ndemanga nkhani za m’Baibulo, amenenso ankadzitcha kuti ndi Akhristu, monga Justin Martyr, Origen, ndi Tertullian ananena kuti Amagi amene anapita kukaona Yesu anali okhulupirira nyenyezi. Mwachitsanzo Tertullian analemba m’buku lake kuti: “Tikudziwa kuti kukhulupirira nyenyezi n’kogwirizana ndi matsenga. Choncho okhulupirira nyenyezi ndi amene anali oyambirira . . . kukapereka ‘mphatso’ kwa Iye [Yesu].” (On Idolatry) Mogwirizana ndi mfundo imeneyi, mabaibulo ambiri anamasulira mawu akuti maʹgoi kuti “okhulupirira nyenyezi.”

Kodi n’chifukwa chiyani Mateyu ananena kuti mawu amene ali m’buku la Zekariya ananenedwa ndi mneneri Yeremiya?

Mawu amenewa akupezeka pa Mateyu 27:9, 10. Palembali, wolemba Uthenga Wabwino Mateyu ananena za ndalama zimene Yudasi Isikariyoti anapatsidwa chifukwa chopereka Yesu. Lembali limati: “Pamenepo zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yeremiya zinakwaniritsidwa. Iye anati: ‘Ndipo anatenga ndalama 30 zasiliva, zomwe zinali mtengo wogulira munthu . . . ndipo anagulira munda wa woumba mbiya.’” Ulosi umenewu wonena za ndalama 30 za siliva umapezeka m’buku la Zekariya osati la Yeremiya.​—Zekariya 11:12, 13.

Zikuoneka kuti nthawi zina buku la Yeremiya, osati la Yesaya, ndi limene linkaikidwa koyamba pa mndandanda wa mabuku otchedwa “Zolemba za aneneri.” Choncho, pamene Mateyu ananena za “Yeremiya” kwenikweni ankatanthauza mabuku amene onse pamodzi ankadziwika ndi dzina la buku limene lili koyambirira pa mndandandawo. Mabuku amenewa akuphatikizaponso buku la Zekariya.

N’chimodzimodzinso Yesu. Iye anatchula mabuku ena a m’Baibulo kuti “Masalimo” koma mabukuwo amatchedwanso kuti Malembo. Choncho, pamene ananena kuti zonse zokhudza iyeyo zolembedwa “m’chilamulo cha Mose, m’Zolemba za aneneri ndi m’Masalimo” zinayenera kukwaniritsidwa, ankatanthauza maulosi onse opezeka m’Malemba Achiheberi.​—Luka 24:44.