Kodi Mulungu Amakukondanidi?
Kodi Mulungu Amakukondanidi?
KODI mumaona kuti anthu amakukondani? Kapena kodi nthawi zina mumaona kuti palibe amene amakukondani? M’dzikoli anthu amakhala otanganidwa kwambiri komanso odzikonda, choncho n’zosavuta kuyamba kuona kuti ndinu wosafunika ndiponso kuti anthu sakuwerengerani. Zimene Baibulo limanena zokhudza anthu masiku athu ano ndi zoona, chifukwa ambiri amangosamala za iwo okha basi ndipo za munthu wina alibe nazo ntchito.—2 Timoteyo 3:1, 2.
Mwachibadwa, aliyense amafuna kukonda winawake komanso kuti azikondedwa, mosayang’ana zaka, chikhalidwe, chinenero kapena mtundu wa munthuyo. Malinga ndi zimene anthu ena amanena, ubongo wathu unapangidwa moti tizitha kuzindikira kuti anthu amatikonda ndiponso amatiganizira. Yehova Mulungu ndi amene anatilenga ndipo amadziwa bwino kuposa aliyense kuti anthufe timafuna kukondedwa ndiponso kuyamikiridwa. Kodi mungamve bwanji Mulungu atakuuzani kuti ndinu wofunika kwambiri kwa iye? Mungaone kuti ndi chinthu chapamwamba kwambiri. Kodi ndi zoonadi kuti Yehova ali nafe chidwi anthu opanda ungwirofe? Kodi amachita chidwi ndi munthu aliyense payekha? Ngati ndi choncho, kodi n’chiyani chimachititsa kuti munthu azikondedwa ndi Mulungu?
Yehova Amatikonda
Zaka zoposa 3,000 zapitazo, munthu wina yemwe analemba nawo buku la Masalimo, anakhudzika mtima kwambiri ataona nyenyezi ndi mwezi zikuwala mochititsa chidwi usiku. Iye sanakayikire kuti Mlengi wa nyenyezi zosawerengeka zimenezi ndi wamkulu kwambiri kuposa aliyense. Poganizira kuti Yehova ndi wamkulu kwambiri ndipo munthu ndi wochepa kwambiri, wolemba masalimoyo anadabwa kuona kuti Yehova amakonda anthu. Iye anati: “Ndikayang’ana kumwamba, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi zimene munapanga, ndimaganiza kuti: Munthu ndani kuti muzimuganizira, ndipo mwana wa munthu wochokera kufumbi ndani kuti muzimusamalira?” (Salimo 8:3, 4) Ndi zosavuta kuganiza kuti Mulungu, amene ndi Wamkulukulu ali kutali kwambiri kapena ndi wotanganidwa kwambiri ndi zinthu zina moti sangamachite chidwi ndi anthu opanda ungwirofe. Komabe wolemba masalimo anazindikira kuti, ngakhale kuti munthu ndi wotsika kwambiri poyerekeza ndi Yehova, ndiponso moyo wake ndi waufupi, Mulungu amamuonabe kuti ndi wofunika.
Munthu winanso amene analemba nawo buku la Masalimo ananena mawu olimbikitsa akuti: “Yehova amasangalala ndi anthu amene amamuopa, amene amayembekezera kukoma mtima kwake kosatha.” (Salimo 147:11) Zimene zanenedwa m’malemba awiri onsewa ndi zokhudza mtima kwambiri, chifukwa ngakhale kuti Yehova ndi wapamwamba kwambiri, sikuti amangodziwa kuti kuli anthu. M’malomwake, iye ‘amawasamalira’ mwachikondi ndiponso ‘amasangalala nawo.’
Ulosi wina wa m’Baibulo, wofotokoza kusintha kumene kukuchitika masiku ano, umatitsimikizira mfundo imeneyi. Kudzera mwa mneneri Hagai, Yehova ananena mawu osonyeza kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu idzachitika padziko lonse lapansi. Kodi zotsatira zake ndi zotani? Mwa zina, Yehova anati: “Zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse ya anthu zidzalowa m’nyumba imeneyi. Ine ndidzadzaza nyumbayi ndi ulemerero.”—Hagai 2:7.
Kodi “zinthu zamtengo wapatali,” zimene zikuchokera ku mitundu yonse ndi chiyani? Zinthu zimenezi sizingakhale katundu kapena ndalama. (Hagai 2:8) Zimene zimasangalatsa mtima wa Yehova si siliva kapena golide. M’malomwake, iye amasangalala ndi anthu amene amamulambira chifukwa chomukonda, ngakhale kuti anthuwo amalakwitsa zinthu zina. (Miyambo 27:11) Anthu oterewa ndiwo “zinthu zamtengo wapatali” zimene zimabweretsa ulemerero kwa Yehova. Iye amayamikira kwambiri kudzipereka kwawo ndiponso khama lawo pomutumikira. Kodi ndinu mmodzi mwa anthu amenewa?
Mwina ena angaone kuti ndi zovuta kukhulupirira kuti anthu, omwe ndi opanda ungwiro, ndi amtengo wapatali kwa Mulungu. Komatu mfundo imeneyi ndi imene iyenera kutilimbikitsa kuyandikira kwa Mulungu yemwe akutiitana mwachikondi kuti tikhale naye pa ubwenzi.—Yesaya 55:6; Yakobo 4:8.
“Ndiwe Munthu Wokondedwa Kwambiri”
Tsiku lina madzulo, mneneri Danieli anaona zinthu zodabwitsa kwambiri. Pa nthawiyi n’kuti iye ali wokalamba. Akupemphera, mwadzidzidzi panafika mlendo winawake wapadera. Dzina lake anali Gabirieli. Iye anamuzindikira kuti ndi mngelo wa Yehova chifukwa aka sikanali koyamba kuti Danieli aonane ndi mlendo ameneyu. Gabirieli anafotokoza chifukwa chimene wabwerera mwadzidzidzi. Iye anati: “Iwe Danieli, tsopano ndabwera kuti ndikuthandize kumvetsa zinthu zonsezi . . . chifukwa iwe ndiwe munthu wokondedwa kwambiri.”—Danieli 9:21-23.
Pa nthawi inanso, mngelo wa Yehova anauza Danieli kuti anali “munthu wokondedwa kwambiri.” Ndiyeno pofuna kulimbikitsa Danieli, mngeloyo anati: “Iwe munthu wokondedwa kwambiri, usachite mantha. Mtendere ukhale nawe.” (Danieli 10:11, 19) Choncho katatu konse Danieli anauzidwa kuti ndi “wokondedwa kwambiri.” Mawu “wokondedwa kwambiri” angatanthauzenso kuti munthu “wamtengo wapatali” kapenanso “wapamtima.”
N’zosakayikitsa kuti Danieli ankakonda kwambiri Mulungu wake Yehova ndipo ankadziwa kuti iye akusangalala ndi kudzipereka kwake pomutumikira. Koma mawu achikondi ochokera kwa Mulungu, amene angelowa ananena, ayenera kuti anamulimbikitsa kwambiri. N’chifukwa chake Danieli ananena kuti: “Mwandilimbikitsa.”—Danieli 10:19.
Nkhani yolimbikitsa kwambiri imeneyi yonena za chikondi cha Yehova kwa mneneri wake wokhulupirika, inalembedwa m’Mawu a Aroma 15:4) Kuganizira mozama za chitsanzo cha Danieli kumatithandiza kuzindikira chimene chimachititsa munthu kukhala wokondedwa kwa Atate wathu wakumwamba amene ndi wachikondi.
Mulungu kuti itithandize. (Muziphunzira Mawu a Mulungu Nthawi Zonse
Danieli ankaphunzira Malemba mwakhama kwambiri. Tikudziwa zimenezi chifukwa iye analemba kuti: “Ineyo . . . ndinazindikira chiwerengero cha zaka za kuwonongedwa kwa Yerusalemu . . . mwa kuwerenga mawu . . . olembedwa m’mabuku.” (Danieli 9:2) Mabuku amene iye anali nawo pa nthawi imeneyo ayenera kuti anali zolembedwa zouziridwa ndi Mulungu za Mose, Davide, Solomo, Yesaya, Yeremiya, Ezekieli ndiponso aneneri ena. Tingathe kumuona Danieli m’maganizo mwathu atakhala pamalo amene pali mipukutu yosiyanasiyana, akuwerenga ndi kuyerekezera maulosi okhudza kubwezeretsa kulambira koona ku Yerusalemu. Danieli ayenera kuti powerenga mipukutuyi ankakhala pamalo aphee popanda zosokoneza, mwina m’chipinda chake chapadenga, ndipo anali kuganizira mozama tanthauzo la malembawo. Kuphunzira Malemba mwakhama kumeneku kunalimbitsa chikhulupiriro chake ndipo kunamuchititsa kuti ayandikire kwa Yehova.
Kuphunzira Mawu a Mulungu kunathandizanso Danieli kuti akhale ndi khalidwe labwino komanso kunakhudza moyo wake wonse. Chifukwa chakuti anaphunzitsidwa Malemba kuyambira ali mwana, zinamuthandiza kuti ali mnyamata asunge malamulo okhudza zimene ayenera kudya ndi zimene sayenera kudya malinga ndi zimene Chilamulo cha Mulungu chinkanena. (Danieli 1:8) Nthawi ina Danieli analengeza uthenga wa Mulungu mopanda mantha kwa olamulira a ku Babulo. (Miyambo 29:25; Danieli 4:19-25; 5:22-28) Aliyense ankadziwa kuti iye anali wakhama, wokhulupirika komanso wodalirika. (Danieli 6:4) Ndiponso chofunika kwambiri ndi chakuti, Danieli sananyalanyaze malamulo a Yehova n’cholinga choti apulumutse moyo wake. Koma iye anakhulupirira Yehova ndi mtima wake wonse. (Miyambo 3:5, 6; Danieli 6:23) N’chifukwa chake anali “wokondedwa kwambiri” kwa Mulungu.
Masiku ano, tinganene kuti kuphunzira Baibulo n’kosavuta kwa ife tikayerekezera ndi mmene zinalili ndi Danieli. Panopa, mipukutu yolembedwa pamanja, yomwe inali ikuluikulu ndiponso yolemera, inalowedwa m’malo ndi mabuku osavuta kuwerenga. Tili ndi Baibulo lonse, limene lilinso ndi nkhani zofotokoza mmene ena mwa maulosi a Danieli anakwaniritsidwira. Tilinso ndi mabuku ambiri otithandiza kulimvetsa bwino Baibulo ndiponso zinthu zotithandiza kufufuza nkhani za m’Baibulo. * Kodi zinthu zimenezi mumazigwiritsa ntchito? Kodi muli ndi nthawi imene munakonza kuti muziwerenga Baibulo ndi kuganizira mozama zimene mwawerengazo? Ngati mumatero, mudzakhala ngati Danieli. Mudzakhala ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso ubwenzi wanu ndi Yehova udzalimba. Mudzayamba kutsogoleredwa ndi Mawu a Mulungu pa moyo wanu, ndiponso mudzakhala otsimikiza kuti Mulungu amakusamalirani mwachikondi.
Limbikirani Kupemphera
Danieli anali munthu wokonda kupemphera. Iye ankapempha Mulungu kuti amuthandize pa zinthu zosiyanasiyana. Ali mnyamata, Nebukadinezara mfumu ya Babulo inaopseza Danieliyo ndi anthu ena kuti aphedwa akalephera kumasulira loto lake. Danieli sanazengereze kuchonderera Yehova kuti amuthandize ndi kumuteteza. (Danieli 2:17, 18) Patapita zaka, mneneri wokhulupirika ameneyu pozindikira kuti ndi wopanda ungwiro, anavomereza modzichepetsa kuti iye komanso Aisiraeli onse ndi anthu ochimwa ndipo anapempha Yehova kuti awakhululukire. (Danieli 9:3-6, 20) Komanso atalephera kumvetsa zinthu zina zimene anauziridwa kulemba, Danieli anapempha Mulungu kuti amuthandize. Pa nthawi ina atapempha zimenezi, mngelo amene anadzabweranso kudzathandiza Danieli kumvetsa zinthu zina, analankhula ndi Danieli ndipo anamutsimikizira kuti: “Mawu ako akhala akumveka.”—Danieli 10:12.
Koma Danieli sankangopempha Mulungu kuti amuthandize. Lemba la Danieli 6:10 limati: “Iye anali . . . kupemphera kwa Mulungu wake ndi kumutamanda katatu pa tsiku, monga mmene anali kuchitira nthawi zonse.” Danieli anali ndi zifukwa zambirimbiri zomuchititsa kuthokoza komanso kutamanda Yehova ndipo ankachita zimenezi kawirikawiri. Danieli ankaona kuti pemphero ndi lofunika kwambiri pa kulambira kwake moti sanalole kusiya kupemphera ngakhale pamene anadziwa kuti akapemphera aphedwa. N’zodziwikiratu kuti Yehova ankamukonda kwambiri Danieli chifukwa cha khama lake limeneli.
Pamenepatu tikuona kuti pemphero ndi mphatso ya mtengo wapatali komanso ndi mwayi wapadera. Musamalole tsiku kudutsa musanapemphere kwa Atate wanu wakumwamba. Muzikumbukira kumuthokoza komanso kumutamanda chifukwa cha zabwino zonse zimene amakuchitirani. Muzimufokozera nkhawa ndiponso mavuto anu momasuka. Muziganizira mmene Yehova wayankhira mapemphero ndi mapembedzero anu ndipo muzimuyamikira chifukwa cha zimenezo. Musamangopemphera mwachidule nthawi zonse. Mukamapemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima mudzaona kuti iye amakukondani inuyo panokha. Chimenechi ndi chifukwa chabwino kwambiri chotichititsa ‘kulimbikira kupemphera.’—Aroma 12:12.
Muzilemekeza Dzina la Yehova
Palibe ubwenzi umene ungakhale wolimba ngati mmodzi mwa mabwenziwo ali wodzikonda. N’chimodzimodzinso ndi ubwenzi wathu ndi Yehova. Danieli ankaidziwa mfundo imeneyi. Taganizirani mmene iye ankaonera nkhani yokhudza kulemekeza dzina la Yehova.
Mulungu atayankha pemphero lake mwa kumuthandiza kudziwa maloto a Nebukadinezara ndiponso tanthauzo lake, Danieli anati: “Dzina la Mulungu likhale lotamandika kuyambira kalekale mpaka kalekale, pakuti nzeru ndi mphamvu ndi zake.” Kenako pamene Danieli ankauza Nebukadinezara maloto ake komanso tanthauzo lake, iye mobwerezabwereza anasonyeza kuti Yehova ndiye woyenera kutamandidwa ndipo anatsindika kuti Yehova yekha ndiye “Woulula zinsinsi.” Pa nthawi inanso pamene ankapempha Mulungu kuti akhululukire Aisiraeli ndiponso kuwapulumutsa, Danieli anapemphera kuti: “Inu Mulungu wanga, . . . mzinda wanu ndi anthu anu amatchedwa ndi dzina lanu.”—Danieli 2:20, 28; 9:19.
Ifenso tingathe kutsanzira Danieli pa nkhani imeneyi. Tikamapemphera, tizisonyeza kuti timafuna kuti dzina la Mulungu “liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9, 10) Sitikufuna kuti khalidwe lathu linyozetse dzina loyera la Yehova. M’malomwake, tizilemekeza Yehova nthawi zonse mwa kuuzako ena zimene tikuphunzira zokhudza uthenga wabwino wa Ufumu wake.
Ndi zoona kuti m’dzikoli chikondi ndiponso kuderana nkhawa ndi zosowa. Koma ndi zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amakondadi munthu aliyense amene amamulambira. Munthu wina amene analemba nawo buku la Masalimo anati: “Yehova amasangalala ndi anthu ake. Iye amakongoletsa anthu ofatsa ndi chipulumutso.”—Salimo 149:4.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 18 A Mboni za Yehova atulutsa mabuku ndi zinthu zosiyanasiyana zothandiza kuphunzira komanso kufufuza nkhani za m’Baibulo. Zinthu zimenezi zingakuthandizeni kuti mupindule powerenga Baibulo. Ngati mukufuna kupeza zinthu zimenezi, funsani a Mboni za Yehova.
[Mawu Otsindika patsamba 21]
Mulungu anasonyeza kuti ankakonda Danieli mwa kumutumizira mngelo Gabirieli kuti akamulimbikitse
[Mawu Otsindika patsamba 23]
Danieli ankapemphera ndiponso kuphunzira Malemba mwakhama ndipo izi zinachititsa kuti akhale ndi khalidwe labwino komanso kuti Mulungu azimukonda