Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Nkhani ya Munda wa Edeni Imakukhudzani Bwanji?

Kodi Nkhani ya Munda wa Edeni Imakukhudzani Bwanji?

Kodi Nkhani ya Munda wa Edeni Imakukhudzani Bwanji?

IMODZI mwa mfundo zodabwitsa zimene akatswiri ena amanena zokhudza munda wa Edeni ndi yakuti, nkhani zina za m’Baibulo sizisonyeza kuti kunalidi munda wa Edeni. Mwachitsanzo, Pulofesa wina wa Maphunziro Azachipembedzo dzina lake Paul Morris analemba kuti: “Kupatula m’buku la Genesis, palibe paliponse m’Baibulo pamene amanena mwachindunji za munda wa Edeni.” Anthu ena omwe amati ndi odziwa zinthu angagwirizane ndi maganizo amenewa koma zimenezi ndi zosagwirizana ndi mmene zinthu zililidi.

M’Baibulo muli nkhani zambiri zosonyeza kuti kunalidi munda wa Edeni ndiponso kunali Adamu, Hava ndi njoka. * Koma zimene akatswiri ochepa amaphunziro amanena potsutsa nkhani yokhudza munda wa Edeni ndi nkhani yaikulu. Atsogoleri achipembedzo ndiponso anthu otsutsa Baibulo akamatsutsa nkhani ya m’buku la Genesis yonena za munda wa Edeni, ndiye kuti kwenikweni akutsutsa Baibulo lonse. N’chifukwa chiyani tikutero?

Kumvetsa bwino zimene zinachitika m’munda wa Edeni n’kofunika kwambiri kuti timvetsenso bwino nkhani zina za m’Baibulo. Mwachitsanzo, Mawu a Mulungu analembedwa kuti atithandize kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri onena za zimene zimachitikira anthu. Nthawi zambiri mayankho amene Baibulo limapereka pa mafunso amenewa, amakhala okhudzana ndi zimene zinachitika m’munda wa Edeni. Taonani zitsanzo izi.

Kodi n’chifukwa chiyani anthufe timakalamba ndiponso kumwalira? Adamu ndi Hava akanamvera Yehova akanakhala ndi moyo kwamuyaya, ndipo imfa ikanabwera pokhapokha ngati sanamvere. Choncho kuyambira pa tsiku limene iwo anapanduka, anakhala ndi moyo woti nthawi ina iliyonse adzafa. (Genesis 2:16, 17; 3:19) Iwo sanalinso angwiro ngati poyamba ndipo anapatsira ana awo kupanda ungwiroko. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’​—Aroma 5:12.

N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti zinthu zoipa zizichitika? M’munda wa Edeni, Satana ananena kuti Mulungu ndi wabodza ndipo amabisira zolengedwa zake zinthu zabwino. (Genesis 3:3-5) Choncho iye anatsutsa ulamuliro wa Yehova. Adamu ndi Hava anasankha kumvera Satana, choncho nawonso anakana ulamuliro wa Yehova. Mwakuchita zimenezi anasonyeza kuti munthu atha kusankha yekha zabwino ndi zoipa popanda kutsogoleredwa ndi Mulungu. Mwa chilungamo chake ndi nzeru zake zangwiro, Yehova anadziwa kuti pali njira imodzi yokha imene angathetsere nkhaniyi moyenera. Njira imeneyo ndi kulola kuti papite nthawi anthu akudzilamulira okha ngati mmene iwo anafunira. Zotsatira zake n’zakuti padziko lapansili pakhala pakuchitika zoipa zambiri ndipo zina mwa zimenezi akuchititsa ndi Satana. Zimenezi zachititsa kuti anthu azindikire mfundo yoona ndiponso yofunika yakuti: Anthu sangathe kudzilamulira okha popanda Mulungu.​—Yeremiya 10:23.

Kodi cholinga cha Mulungu polenga dzikoli ndi chiyani? Yehova anafuna kuti dziko lonse lapansi lidzakhale lokongola ngati munda wa Edeni. Iye analamula Adamu ndi Hava kuti abereke ana ndi kudzaza dziko lapansi ndipo ‘aliyang’anire’ n’cholinga choti dziko lonse lapansi likhale lokongola mofanana ndi munda wa Edeni. (Genesis 1:28) Choncho cholinga cha Mulungu polenga dzikoli chinali choti likhale paradaiso, ndipo ana a Adamu ndi Hava angwiro azikhala mmenemo mogwirizana. Mbali yaikulu ya Baibulo imafotokoza mmene Mulungu adzakwaniritsira cholinga chake choyambirira chimenechi.

Kodi n’chifukwa chiyani Yesu Khristu anabwera padziko lapansi? Kupanduka kwa Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni kunachititsa kuti iwo afe komanso kuti ana awo azifa. Komabe chifukwa cha chikondi, Mulungu anapereka chiyembekezo choti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo. Iye anatumiza Mwana wake padziko lapansi kuti adzapereke chimene Baibulo limati, dipo. (Mateyu 20:28) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Yesu anali “Adamu womalizira,” ndipo anachita zimene Adamu analephera kuchita. Yesu anakhalabe munthu wangwiro chifukwa anapitirizabe kumvera Yehova. Kenako mofunitsitsa anapereka moyo wake monga nsembe kapena kuti dipo ndipo zimenezi zinachititsa kuti anthu onse okhulupirika azikhululukidwa machimo ndiponso kuti m’tsogolo adzakhale ndi moyo wofanana ndi umene Adamu ndi Hava anali nawo mu Edeni asanachimwe. (1 Akorinto 15:22, 45; Yohane 3:16) Mwa kuchita zimenezi, Yesu anatitsimikizira kuti cholinga cha Yehova chokonzanso dziko lapansi kuti likhale paradaiso, ngati mmene zinalili mu Edeni, chidzachitikadi. *

Cholinga cha Mulungu chimenechi chidzachitikadi ndipo sikuti ndi zinthu zongoyerekezera chabe. Munda wa Edeni anali malo enieni padzikoli ndipo m’mundamo munali nyama ndiponso anthu. Mofanana ndi zimenezi, zimene Mulungu walonjeza ndi zenizeni ndipo posachedwapa zidzakwaniritsidwa. Kodi inuyo mudzakhalapo pa nthawi imeneyi? Kuti zimenezi zitheke, zikudalira inuyo. Mulungu akufuna kuti aliyense amene angasinthe, ngakhale amene anali wochimwa kwambiri, adzakhalepo pa nthawi imeneyo.​—1 Timoteyo 2:3, 4.

Yesu atatsala pang’ono kufa, analankhula ndi munthu amene anali wochimwa kwambiri. Munthu ameneyu anali chigawenga ndipo ankadziwa kuti ankayeneradi kuphedwa. Koma anakhulupirira kuti Yesu ndi amene angamutonthoze ndiponso kum’patsa chiyembekezo. Kodi pamenepa Yesu anatani? Anamuuza kuti: “Iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Yesu akufuna kudzaonanso munthu ameneyu ataukitsidwa ndiponso kupatsidwa mwayi wokhala ndi moyo wosatha m’paradaiso wofanana ndi munda wa Edeni, ngakhale kuti munthuyu poyamba anali chigawenga. Ndiye kodi si zoona kuti Yesu amafunanso kuti inuyo mudzakhale m’paradaiso? N’zosakayikitsa kuti amafuna zimenezi ndipo Atate ake amafunanso zimenezi. Ngati mukufuna kuti mudzakhale m’paradaiso ameneyu, yesetsani kuphunzira za Mulungu amene analenga munda wa Edeni.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Kuti mudziwe zambiri zokhudza nsembe ya dipo ya Khristu, werengani mutu 5 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 10]

Ulosi Umene Umasonyeza Kuti Nkhani Zonse Za M’baibulo Ndi Zogwirizana

“Ndidzaika chidani pakati pa iwe [njoka] ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Mbewu ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza chidendene.”​—Genesis 3:15.

Umenewu ndi ulosi woyamba m’Baibulo ndipo Mulungu ndi amene analosera zimenezi m’munda wa Edeni. Kodi mkazi, mbewu ya mkazi, njoka ndiponso mbewu ya njoka zimene zatchulidwa mu ulosi umenewu zikuimira ndani? Nanga “chidani” chimene anachinenacho ndi chotani?

NJOKA

Satana Mdyerekezi.​—Chivumbulutso 12:9.

MKAZI

Gulu la Yehova la zolengedwa zakumwamba. (Agalatiya 4:26, 27) Yesaya analosera kuti “mkazi” ameneyu adzabereka ana amene m’tsogolo adzakhale mtundu waukulu wauzimu.​—Yesaya 54:1; 66:8.

MBEWU YA NJOKA

Anthu amene asankha kuchita chifuniro cha Satana.​—Yohane 8:44.

MBEWU YA MKAZI

Yesu Khristu ndiye mbewu yoyambirira ya mkazi ndipo anachokera m’mbali yakumwamba ya gulu la Yehova. Koma enanso amene ali m’gulu la “mbewu” imeneyi ndi abale auzimu a Khristu omwe adzalamulire naye kumwamba. Akhristu odzozedwa amenewa ndi amene amapanga mtundu wauzimu wotchedwa “Isiraeli wa Mulungu.”​—Agalatiya 3:16, 29; 6:16; Genesis 22:18.

KUVULAZA CHIDENDENE

Ululu umene Mesiya anamva kwa kanthawi. Satana anakwanitsa kupha Yesu pamene Yesuyo anali padziko lapansi. Koma Yesu anaukitsidwa.

KUPHWANYA MUTU

Kupha Satana. Yesu adzawononga Satana ndipo sadzakhalakonso. Koma ngakhale asanachite zimenezi, Yesu adzathetsa zoipa zonse zimene Satana anayambitsa mu Edeni.​—1 Yohane 3:8; Chivumbulutso 20:10.

Kuti mudziwe zambiri zokhudza nkhani yaikulu ya m’Baibulo lonse, onani kabuku kakuti, Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani? komwe kamafotokoza nkhaniyi mwachidule. Kabukuka kamafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 11]

Adamu ndi Hava anavutika kwambiri chifukwa chakuti anachimwa