Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Inu Mulungu Wanga, Mundikumbukire pa Zabwino Zimene Ndinachita”

“Inu Mulungu Wanga, Mundikumbukire pa Zabwino Zimene Ndinachita”

Yandikirani Mulungu

“Inu Mulungu Wanga, Mundikumbukire pa Zabwino Zimene Ndinachita”

MAYI wina yemwe ndi Mkhristu wokhulupirika ndipo ankalimbana ndi maganizo odziona kuti ndi wosafunika, analemba kuti: “Ndinkaganiza kuti popeza Yehova amandidziwa bwino kwambiri, sangandikonde kapena kundiona ngati munthu wabwino.” Kodi inunso mumavutika ndi maganizo oterowo? Kodi mumadziona kuti Mulungu alibe nanu ntchito ndipo sangakukondeni? Ngati mumamva choncho mawu opezeka pa Nehemiya 13:31 angakulimbikitseni kwambiri.

Nehemiya anali bwanamkubwa wa Ayuda m’zaka za m’ma 400 B.C.E. ndipo anayesetsa kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu. Anatsogolera pa ntchito yomanganso mpanda wa Yerusalemu ngakhale kuti panali adani ambiri amene ankadana ndi ntchitoyi. Anathandizanso anthu kuti azitsatira Chilamulo cha Mulungu, anasamalira anthu oponderezedwa ndiponso anathandiza Aisiraeli anzake kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Kodi Mulungu anaona zinthu zabwino zimene Nehemiya anachitazi? Kodi Yehova anakondwera naye? Mayankho a mafunso amenewa tingawapeze m’mawu omaliza a buku la Nehemiya.

Nehemiya anapemphera kuti: “Inu Mulungu wanga, mundikumbukire pa zabwino zimene ndinachita.” * Kodi Nehemiya anapemphera chonchi chifukwa choda nkhawa kuti mwina Mulungu sanaone ntchito zake zabwino kapenanso kuti sadzamukumbukira? Ayi, chifukwa n’zachidziwikire kuti Nehemiya ankadziwa zimene anthu ena amene analemba Baibulo ananena zokhudza Yehova kuti amakonda anthu amene amamulambira ndipo amaona zabwino zimene anthuwo akuchita. (Ekisodo 32:32, 33; Salimo 56:8) Ndiyeno pamenepa kodi Nehemiya ankapempha Mulungu chiyani? Buku lina limati mawu achiheberi amene m’Baibulo anawamasulira kuti “mundikumbukire,” amatanthauza “chikondi chimene wokumbukirayo amakhala nacho mumtima ndiponso zimene amachita akakumbukira chinachake.” Choncho Nehemiya ankadziwa kuti pemphero limathandiza kwambiri ndipo anapempha Mulungu kuti amukumbukire, kumukonda komanso kumudalitsa.​—Nehemiya 2:4.

Kodi Yehova anayankha pemphero la Nehemiya limeneli? Tinganene kuti anayamba kale kuliyankha. Yehova anaona kuti ndi zoyenera kuti pemphero limeneli lilembedwe n’kukhala mbali ya Malemba ouziridwa. Umenewu ndi umboni wosonyeza kuti Yehova anakumbukira Nehemiya ndipo amamukonda. Kodi “Wakumva pemphero” ameneyu adzachitanso chiyani poyankha pemphero lochokera pansi pa mtima la Nehemiya?​—Salimo 65:2.

Mulungu adzapatsa Nehemiya mphoto chifukwa cha zabwino zonse zimene anachita pa nkhani ya kulambira koona. (Aheberi 11:6) M’dziko latsopano lachilungamo limene likubweralo, limene Yehova watilonjeza, iye adzakumbukira Nehemiya pomuukitsa kwa akufa. * (2 Petulo 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4) M’dziko limenelo, Nehemiya adzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha m’paradaiso ndipo adzaona kuti Yehova wamukumbukiradi pa zabwino zimene anachita.

Pemphero la Nehemiya limasonyeza kuti mawu a Mfumu Davide ndi oona. Iye anati: “Inu Yehova mudzadalitsa aliyense wolungama. Mudzamutchinga ndi chivomerezo chanu ngati kuti mukum’teteza ndi chishango chachikulu.” (Salimo 5:12) Dziwani kuti Mulungu amaona ndipo amasangalala ndi zimene tikuchita ndi mtima wonse pofuna kumusangalatsa. Ngati mukuyesetsa kumutumikira, musakayikire ngakhale pang’ono kuti amakukondani, adzakukumbukirani ndi kukudalitsani kwambiri.

Mavesi amene mungawerenge mu February:

Nehemiya 1-13

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Aka ndi kachinayi ndiponso komaliza m’buku limeneli kuti Nehemiya apemphe kuti Mulungu amuchitire zabwino kapena kumudalitsa chifukwa kukhulupirika kwake.​—Nehemiya 5:19; 13:14, 22, 31.

^ ndime 5 Kuti mudziwe zambiri zimene Mulungu adzachitire anthu okhulupirika padziko lapansi, werengani mutu 3 ndi 7 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.