Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi “a m’nyumba ya Kaisara” amene anauza Paulo kuti awaperekere moni kwa Akhristu a ku Filipi anali ndani?

Ali ku Roma, mtumwi Paulo analembera kalata mpingo wa ku Filipi, cha pakati pa 60 C.E. ndi 61 C.E ndipo Kaisara amene anamutchula m’kalatayi anali Mfumu Nero. Komano kodi a m’nyumba ya Nero amene anapereka moni kwa Akhristu a ku Filipi anali ndani?​—Afilipi 4:22.

Kungakhale kulakwitsa kuganiza kuti mawu akuti a “m’nyumba ya Kaisara” akunena za abale ake enieni a mfumu Nero. Mawu amenewa ankatanthauza anthu onse amene anali antchito a mfumu. Anthu amenewa anali akapolo ndiponso anthu amene sanali akapolo, a ku Roma ndi m’madera amene ankalamulidwa ndi ufumuwo. Choncho mawu akuti “a m’nyumba ya Kaisara” ayenera kuti akutanthauza antchito ambirimbiri. Antchito amenewa ankagwira ntchito ngati mamaninjala kapenanso akapolo kunyumba yachifumu komanso m’minda ndi m’malo ena amene munali zinthu za mfumu. Ena mwa antchitowa anali ndi maudindo akuluakulu mu ufumu wa Roma.

Zikuoneka kuti ena mwa antchito a mfumu Nero ku Roma anakhala Akhristu. Sizikudziwika ngati anthu amenewa anakhala Akhristu atalalikidwa ndi Paulo ku Roma. Baibulo silinena chimene chinachititsa kuti anthu amenewa akhale Akhristu, koma zikuoneka kuti iwo anali ndi chidwi kwambiri ndi anthu a mumpingo wa ku Filipi. Filipi linali dera lolamulidwa ndi ufumu wa Roma ndipo kunkakhala asilikali ambiri opuma pantchito komanso anthu ambiri ogwira ntchito m’boma. Choncho, n’kutheka kuti ena mwa Akhristu kumeneko anali ndi anzawo ku Roma amene anatuma Paulo kuti akawapelekere moni.

Kodi ukwati wa pachilamu kapena kuti wolowa chokolo, wotchulidwa m’Chilamulo cha Mose unali wotani?

Kale ku Isiraeli munthu akamwalira opanda mwana wamwamuna, mchimwene wake ankayenera kukwatira mkazi wamasiyeyo n’cholinga chakuti amuberekere ana kuti dzina la munthu womwalira uja lisafe. (Genesis 38:8) Kenako, dongosolo limeneli linakhala mbali ya Chilamulo cha Mose ndipo linkatchedwa ukwati wapachilamu kapena kulowa chokolo. (Deuteronomo 25:5, 6) Zimene Boazi anachita, zomwe zafotokozedwa m’buku la Rute, zikusonyeza kuti ngati munthu womwalirayo analibe mchimwene wake aliyense, wachibale wake wina ankayenera kulowa chokolo kwa mkazi wa masiyeyo.​—Rute 1:3, 4; 2:19, 20; 4:1-6.

Umboni wosonyeza kuti m’nthawi ya Yesu anthu ankachitabe ukwati wa pachilamu ndi nkhani yopezeka pa Maliko 12:20-22, pamene Asaduki anatchula za ukwati umenewu. Myuda wina wolemba mbiri yakale, dzina lake Flavius Josephus ndipo anakhalapo m’nthawi ya atumwi, ananena kuti ukwati wa pachilamu unkathandiza kuti dzina lisafe komanso kuti chuma cha banjalo chitetezeke. Unkathandizanso kuti mkazi wamasiyeyo asavutike ndi umasiye. Nthawi imeneyo mkazi sankapatsidwa chilichonse pa chuma cha mwamuna wake. Koma mwana wobadwa mu ukwati wa chokolo ankapatsidwa chuma cha munthu womwalira uja.

Chilamulo chinkalola wachibale wa munthu womwalira kukana kulowa chokolo ngati sakufuna. Koma anthu ankaona kuti munthu wokana “kumanga nyumba ya m’bale wake” anali wochititsa manyazi kwambiri.​—Deuteronomo 25:7-10; Rute 4:7, 8.