Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

Kodi Yesu Khristu Ndani?

Kodi Yesu Khristu Ndani?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi Yesu Khristu ndani?

Yesu ndi wosiyana ndi munthu wina aliyense chifukwa iye anakhalapo kumwamba ngati mzimu asanadzabadwe padziko lapansi. (Yohane 8:23) Iye ndi amene Mulungu anayambirira kumulenga ndipo anathandiza pa ntchito yolenga zinthu zina zonse. Yesu yekha ndi amene analengedwa mwachindunji ndi Yehova, choncho amatchedwa Mwana “wobadwa yekha” wa Mulungu. Komanso Mulungu akafuna kulankhula ankagwiritsa ntchito Yesu, choncho amatchedwanso “Mawu.”​—Yohane 1:1-3, 14; werengani Miyambo 8:22, 23, 30; Akolose 1:15, 16.

2. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anabwera padziko lapansi?

Mulungu anatumiza Mwana wake padziko lapansi mwa kusamutsira moyo wake m’mimba mwa namwali wachiyuda dzina lake Mariya. Choncho Yesu analibe bambo padziko lapansi. (Luka 1:30-35) Yesu anabwera padziko lapansi, (1) kudzaphunzitsa anthu choonadi ponena za Mulungu, (2) kudzatipatsa chitsanzo pa nkhani ya kuchita chifuno cha Mulungu komanso, (3) kudzapereka moyo wake wangwiro monga “dipo.”​—Werengani Mateyu 20:28; Yohane 18:37.

3. Kodi n’chifukwa chiyani timafunikira dipo?

Dipo ndi chinthu chimene chimaperekedwa pofuna kuwombola munthu mu ukapolo. Pamene Mulungu analenga anthu, analibe cholinga chakuti anthuwo azifa kapena kukalamba. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Mulungu anauza munthu woyambirira kulengedwa, Adamu, kuti akapanda kumvera, adzafa. Baibulo limati kusamvera Mulungu ndi tchimo. Adamu akanapanda kuchimwa sanakafa. Ngakhale kuti Adamu anakhalabe ndi moyo kwa zaka zambiri atachimwa, tinganene kuti kuchokera tsiku limene sanamvere Mulungu iye anayamba kufa. (Genesis 2:16, 17; 5:5) Adamu anapatsira mbadwa zake uchimo ndiponso chilango cha uchimowo chimene ndi imfa. Choncho imfa ‘inalowa’ m’dziko kudzera mwa Adamu. N’chifukwa chake anthufe timafunika dipo.​—Werengani Aroma 5:12; 6:23.

4. N’chifukwa chiyani Yesu anafa?

Kodi ndani akanapereka dipo kuti atipulumutse ku imfa? Munthu akafa, ndiye kuti wapereka malipiro a machimo ake okha basi. Palibe munthu wopanda ungwiro amene angapereke malipiro a machimo a ena.​—Werengani Salimo 49:7-9.

Popeza kuti Yesu analibe bambo padziko lapansi, anabadwa wopanda machimo. Choncho iye anafa chifukwa cha machimo athu, osati ake. Mulungu anatumiza Mwana wake padziko lapansi kuti adzatifere. Zimenezi zinasonyeza kuti iye amakonda kwambiri anthu. Nayenso Yesu anasonyeza kuti amatikonda mwa kumvera Atate wake ndiponso kupereka moyo wake chifukwa cha machimo athu.​—Werengani Yohane 3:16; Aroma 5:18, 19.

5. Kodi panopa Yesu akuchita chiyani?

Yesu anachiritsa odwala, kuukitsa akufa ndiponso kuthandiza anthu amene moyo wawo unali pangozi. Iye anachita zimenezi posonyeza zimene adzachitire anthu onse omvera m’tsogolo. (Luka 18:35-42; Yohane 5:28, 29) Yesu atafa, Mulungu anamuukitsa kuti akhale mzimu ngati mmene analili poyamba. (1 Petulo 3:18) Ndiyeno Yesu anakhala kudzanja lamanja la Mulungu mpaka pamene Yehova anamuika kukhala Mfumu ya dziko lapansi. (Aheberi 10:12, 13) Panopa Yesu akulamulira kumwamba ndipo otsatira ake akulengeza uthenga wabwino padziko lonse lapansi.​—Werengani Danieli 7:13, 14; Mateyu 24:14.

Posachedwapa Yesu adzagwiritsa ntchito mphamvu zake monga Mfumu, kuthetsa mavuto onse komanso kuwononga amene amayambitsa mavutowo. Anthu ambirimbiri amene amakhulupirira Yesu ndiponso kumumvera adzakhala m’paradaiso padziko lapansi.​—Werengani Salimo 37:9-11.