Ulosi Wofunika Kwambiri
Ulosi Wofunika Kwambiri
“Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—MATEYU 24:14.
AKATSWIRI a nkhani za m’Baibulo amavomereza kuti vesi limeneli ndi lofunika kwambiri. Iwo amanena choncho chifukwa chakuti vesili limafotokoza za ntchito imene ikuchitika padziko lonse. Komanso ndi vesi lofunikadi chifukwa limanena zimene Akhristu ayenera kuchita, zomwe ndi kugwira ntchito yolalikira. Ntchitoyi ndi imene idzatsatizane ndi nthawi yofunika kwambiri, yokhala ndi zochitika zambirimbiri, imene Yesu anaitchula kuti “mapeto.”
Ulosi umene uli pavesili ukukwaniritsidwa masiku ano ndipo ukukukhudzani. Zili choncho chifukwa mu uthenga wabwino muli chenjezo komanso pempho loti muchite zinazake. Uthengawu ukukupatsani mwayi wosankhapo chinthu chimodzi pa zinthu izi: Kuvomereza Ufumu wa Mulungu kapena kutsutsana nawo. Koma dziwani kuti zimene mungasankhezo zingakhudzenso moyo wanu.
Mwachitsanzo taganizirani mfundo iyi. Kutatsala masiku angapo kuti Yesu apachikidwe, ophunzira ake anamufunsa zimene zidzachitike m’tsogolo. Iwo anafuna kuti Yesu awauze za kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu umene iye ankawauza kawirikawiri. Komanso ankafuna kudziwa za “mapeto a nthawi ino,” kapena monga mmene Mabaibulo ena amanenera, “kutha kwa dziko.”—Mateyu 24:3, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono.
Poyankha funso limenelo, Yesu analosera kuti kudzakhala nkhondo zikuluzikulu, njala, miliri, ndi zivomezi zamphamvu. Anawauzanso kuti anthu azidzachita kwambiri zinthu zosamvera malamulo, aphunzitsi onyenga azipembedzo azidzasocheretsa anthu ambiri ndipo Akhristu azidzadedwa. Zonsezi si uthenga wabwino.—Mateyu 24:4-13; Luka 21:11.
Koma Yesu anatchulanso zinthu zina zimene ndi uthenga wabwino. Iye anapitiriza ulosi wake mwa kunena mawu amene ali m’vesi limene lili kumayambiriro kwa nkhani ino. Kwa zaka zambiri mawu amenewa achititsa chidwi komanso kupatsa chiyembekezo anthu ambiri. Ngakhale kuti anthu amavomereza kuti mawu a Yesu amenewa ndi ofunika, iwo sagwirizana ndi zimene mawuwa amatanthauza. Kodi uthenga wabwino ndi chiyani kwenikweni? Kodi Ufumu umene watchulidwa palemba limeneli n’chiyani? Kodi ulosi umenewu udzakwaniritsidwa liti, ndipo amene adzaukwaniritse ndani? Nanga, kodi “mapeto” ndi chiyani? Tiyeni tikambirane mayankho a mafunso amenewa.
[Chithunzi pamasamba 2, 3]
Chithunzi cha Buku la Washington Manuscript la Mauthenga Abwino Anayi. Pamene Awalitsapo ndi[Mawu a Chithunzi]
From the book Facsimile of the Washington Manuscript of the Four Gospels in the Freer Collection 1912.