Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chiyani Chingatithandize Kulimbana ndi Mavuto Amene Tikukumana Nawo?

Kodi N’chiyani Chingatithandize Kulimbana ndi Mavuto Amene Tikukumana Nawo?

Nkhani ya Onse Yapadera

Kodi N’chiyani Chingatithandize Kulimbana ndi Mavuto Amene Tikukumana Nawo?

Masiku ano malangizo ali ponseponse. Pali mabuku ndiponso mapulogalamu a pa TV amene amapereka malangizo a zimene anthu angachite kuti azitha kuthetsa okha mavuto awo. Koma ngakhale zili choncho, mavuto pa dzikoli sakutha. Mwina mungafunse kuti, ‘Kodi pali malangizo amene tingawadaliredi?’ Yankho la funso limeneli ndi lakuti inde.

Ngakhale kuti Baibulo linalembedwa zaka zambiri zapitazo, lili ndi malangizo amene satha ntchito. Malangizo amenewa angatithandize kupeza mayankho a mafunso monga akuti:

▪ Ngati sindikugwirizana ndi munthu wina, kodi ndingathetse bwanji vutolo? Nanga ndingatani kuti ndizikhala bwino ndi anthu?

▪ Kodi ndingatani kuti ndizikhala wosangalala?

▪ Kodi ndingathane bwanji ndi mavuto azachuma?

▪ Kodi ndingachepetse bwanji nkhawa?

Mafunso amenewa adzayankhidwa m’nkhani ya onse ya mutu wakuti, “Kodi Mfundo za m’Baibulo Zingatithandize pa Mavuto a Masiku Ano?” Nkhani yochokera m’Baibulo imeneyi, idzakambidwa padziko lonse m’mayiko oposa 230. M’madera ambiri idzakambidwa m’Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova, Lamlungu pa May 1, 2011.

A Mboni za Yehova akudera lanulo, adzakuuzani nthawi ndi malo kumene nkhani imeneyi idzakambidwire. Tikukuitanani kuti mudzamvere nkhani imeneyi.