Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ndimakhulupirira”

“Ndimakhulupirira”

Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

“Ndimakhulupirira”

PANALI patatha masiku anayi chimwalirireni Lazaro ndipo Marita anali akuganizirabe mmene manda a mchimwene wakeyo anali kuonekera. Mandawo anali phanga limene pakhomo pake anatsekapo ndi chimwala. Marita anali ndi chisoni chachikulu ndi imfa ya mchimwene wake Lazaro yemwe ankamukonda kwambiri moti sanakhulupirire kuti wapitadi. Pa nthawiyi Marita anatanganidwa kwambiri chifukwa ankalandirabe mauthenga opepesa, pakhomopo panali padakali anthu ena olira maliro komanso pankabwerabe alendo.

Ndiyeno Yesu, munthu yemwe anali wofunika kwambiri kwa Lazaro, anafika kunyumba kwa Marita, m’tauni yaing’ono ya Betaniya. Marita ataona Yesu, chisoni chake chinawonjezeka chifukwa Yesu anali munthu yekhayo padziko lonse amene akanathandiza kuti Lazaro asafe. Komabe ngakhale zinali choncho, mtima wa Marita unakhala m’malo ataona kuti Yesu wabwera kudzawatonthoza. Pa nthawi yochepa imene anakhala ndi Yesu, Marita analimbikitsidwa chifukwa Yesu anali munthu wachikondi, wokoma mtima ndiponso wachifundo. Yesu anafunsa Marita mafunso amene anamuthandiza kuganizira kwambiri za chikhulupiriro chake pa nkhani yakuti akufa adzauka. Pokambiranapo, Marita analankhula amodzi mwa mawu ofunika kwambiri amene anali asanalankhulepo. Iye ananena kuti: “Ndimakhulupirira kuti ndinu Khristu Mwana wa Mulungu, Amene dziko linali kuyembekezera kubwera kwake.”​—Yohane 11:27.

Marita anali mayi wachikhulupiriro cholimba kwambiri. Pa zochepa zimene Baibulo limanena za iye, tingaphunzirepo mfundo zofunika kwambiri zotithandiza kulimbitsa chikhulupiriro. Kuti mumvetse mfundo imeneyi, tiyeni tione kaye pamene Marita akutchulidwa koyamba m’Baibulo.

Marita ‘Anada Nkhawa Ndiponso Kutanganidwa’

Miyezi yambiri izi zisanachitike, Lazaro anali bwinobwino kunyumba kwawo ku Betaniya, ndipo anali akuyembekezera kulandira Yesu Khristu, mlendo wofunika kwambiri. Lazaro, Marita ndi Mariya anali anthu a banja limodzi ndipo ankakhala m’nyumba imodzi ngakhale kuti anali akuluakulu. Anthu ena ofufuza amanena kuti Marita ayenera kuti anali wamkulu pa onsewo. Iwo amanena choncho chifukwa Marita ndi amene ankathamangathamanga pakabwera alendo komanso chifukwa choti nthawi zambiri iye ndi amene amatchulidwa koyambirira. (Yohane 11:5) Palibe njira imene tingadziwire ngati anthu amenewa anakwatiwa kapena kukwatirapo pa moyo wawo. Koma chomwe tikudziwa n’chakuti, iwo anali mabwenzi apamtima a Yesu. Yesu akamachita utumiki wake ku Yudeya, kumene anthu ambiri anakana kumva uthenga wake komanso ankamuchitira zankhanza zambiri, ankakonda kukacheza kwa Lazaro, Marita ndi Mariya. Yesu ayenera kuti ankayamikira kwambiri chifukwa ankapeza mtendere akafika kunyumba kwa anthu amenewa, omwe anali kumuthandiza kwambiri.

Marita ankaonetsetsa kuti panyumbapo ndi posamalidwa bwino komanso ankaonetsetsa kuti alendo akusamalidwa bwino. Chifukwa choti iye anali wolimbikira ntchito komanso wakhama, nthawi zonse ankakhala wotanganidwa. Pa nthawi imene Yesu anabwera kunyumba kwawo, Marita anatanganidwanso kwambiri. Pokonzekera kubwera kwa Yesu, yemwe mwina analinso limodzi ndi anzake amene ankayenda nawo, Marita anakonza chakudya chabwino cha mitundu yosiyanasiyana. Pa nthawi imeneyo, kulandira bwino alendo chinali chinthu chofunika kwambiri. Mlendo akafika panyumba, ankamupsopsona, kumuvula nsapato, kum’sambitsa mapazi ndipo kenako ankamupaka pamutu mafuta onunkhira. (Luka 7:44-47) Unalinso udindo wa eninyumba kumupatsa mlendo malo ogona abwino ndiponso chakudya chabwino.

Choncho Marita ndi Mariya anali ndi ntchito yambiri yokonzekera mlendo wawoyo. Mariya, amene anthu ambiri amaganiza kuti anali munthu wosachedwa kukhumudwa komanso ankaganiza kwambiri, ayenera kuti anathandiza mchemwali wakeyo ntchito. Koma Yesu atangofika zinthu zinasintha. Yesu anaona kuti imeneyi ndi nthawi yoti aphunzitse anthu ndipo anachitadi zimenezo. Mosiyana ndi atsogoleri achipembedzo a nthawi imeneyo, Yesu ankalemekeza kwambiri akazi ndipo ankawaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu, womwe unali mfundo yaikulu ya zimene ankaphunzitsa. Mariya anasangalala ndi zimene Yesu ankaphunzitsa moti anakhala pansi pafupi naye n’kumamvetsera mwachidwi.

Taganizani mmene Marita anamvera mumtima mwake ndi zimene Mariya anachitazi. Marita anali ndi nkhawa kwambiri komanso anasokonezeka maganizo chifukwa panali zakudya zambiri zoti ziphikidwe komanso ntchito zambiri zofunika kugwira kuti asamalire alendowo. Kodi Marita ankamva bwanji mumtima akamadutsa n’kuona Mariya atangokhala m’malo momuthandiza ntchito? Kodi anapsa mtima, kumangonyinyirika mwinanso kumuyang’anitsitsa mokwiya? Ngati anachitadi zimenezi, n’zosadabwitsa chifukwa zinali zovuta kuti agwire yekha ntchito yonseyo.

Kenako Marita anaona kuti sangathenso kupirira moti ananena zimene zinali kukhosi kwake. Iye anadula mawu Yesu n’kunena kuti: “Ambuye, kodi sizikukukhudzani kuti m’bale wangayu wandilekerera ndekha ntchito? Tamuuzani kuti andithandize.” (Luka 10:40) Marita ananena mawu amenewa atakwiya kwambiri. Mabaibulo ena anamasulira mawu a Marita amenewa kuti: “Ambuye, kodi mulibe nazo ntchito . . . ?” Kenako anauza Yesu kuti amudzudzule Mariya n’kumuuza kuti apite kukamuthandiza ntchito.

Marita ayenera kuti anadabwa ndi yankho la Yesu ndipo anthu ambiri amene amawerenga Baibulo amadabwanso ndi yankho limeneli. Yesu anayankha modekha kuti: “Marita, Marita, ukuda nkhawa ndiponso kutanganidwa ndi zinthu zambiri. Komatu zinthu zofunika kwenikweni n’zochepa chabe, mwinanso n’chimodzi chokha basi. Kumbali yake, Mariya wasankha chinthu chabwino kwambiri, ndipo sadzalandidwa chinthu chimenechi.” (Luka 10:41, 42) Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani? Kodi ankatanthauza kuti Marita anali wokonda kwambiri zinthu zakuthupi? Kapena kodi iye ankaona kuti Marita akungotaya nthawi yake kukonza chakudyacho?

Ayi, chifukwa Yesu ankadziwa kuti Marita ankachita zimenezi chifukwa chowakonda. Komanso Yesu sankatanthauza kuti kukonzera alendo zakudya zosiyanasiyana n’kulakwa. Zili choncho chifukwa nthawi ina m’mbuyomo, iye anapezeka pa “phwando lalikulu” limene Mateyu anamukonzera. (Luka 5:29) Choncho pamenepa vuto silinali chakudya chimene Marita ankakonza, koma zinthu zimene Marita ankaona kuti ndi zofunika kwambiri. Maganizo ake onse anali pa kukonza chakudya moti sanathenso kuganizira zinthu zofunika kwambiri. Kodi pamenepa chinali chofunika kwambiri n’chiyani?

Yesu, yemwe ndi Mwana wobadwa yekha wa Yehova Mulungu, anali atabwera m’nyumba ya Marita kudzaphunzitsa choonadi. Chinthu china chilichonse chimene Marita anachita, kuphatikizapo kukonzekera alendo ndiponso kuwaphikira chakudya, sichinali chofunika kwambiri kuposa kuphunzira mawu a Mulungu. Yesu ayenera kuti anakhumudwa poona kuti Marita akumanidwa mwayi womvetsera zimene iye akuphunzitsa, zomwe zikanathandiza Marita kulimbitsa chikhulupiriro chake. Komabe Yesu sanafune kumusankhira Marita zochita. Marita anali ndi ufulu wosankha yekha zimene zinali zofunika kwambiri kwa iye. Koma Marita analibe ufulu wosankhira Mariya zoyenera kuchita.

Choncho Yesu mokoma mtima anamusonyeza Marita kuti maganizo amenewo anali olakwika. Anatchula dzina lake kawiri n’cholinga chofuna kumukhazika mtima pansi. Kenako anamutsimikizira kuti panalibe chifukwa ‘chodera nkhawa ndiponso chotanganidwa ndi zinthu zambiri.’ Chakudya chochepa chinali chokwanira pa nthawiyi, makamakanso chifukwa chakuti panali chakudya chambiri chauzimu. N’chifukwa chake Yesu anaona kuti panalibe chifukwa chakuti alande Mariya “chinthu chabwino kwambiri” chimene anasankha chomwe ndi kumvetsera zimene Yesu ankaphunzitsa.

Nkhani yonena za zimene zinachitika kunyumba ya Marita imeneyi, ili ndi zambiri zimene otsatira a Yesu angaphunzirepo masiku ano. Tikuphunzirapo kuti sitiyenera kulola china chilichonse kutilepheretsa kupeza “zosowa zathu zauzimu.” (Mateyu 5:3) N’zoona kuti tikufunika kutsanzira Marita pa nkhani yochereza alendo ndiponso kulimbikira ntchito. Komabe, sitifunika ‘kumada nkhawa ndiponso kutanganidwa ndi zinthu zambiri’ zosafunika kwenikweni pa nkhani yochereza alendo, moti mpaka kulephera kumachita zinthu zofunika kwambiri. Tikamacheza ndi okhulupirira anzathu, cholinga chathu chimakhala kulimbikitsana ndiponso kupatsana mphatso zauzimu, osati kuwaphikira kapena kuti atiphikire chakudya chamtengo wapatali. (Aroma 1:11, 12) Pocheza ndi Akhristu anzathu, tingathe kulimbikitsana ngakhale titakhala kuti chakudya chimene tadya nawo si chamtengo wapatali.

Mchimwene Wawo Anaukitsidwa

Kodi Marita anamvera malangizo a Yesu amene anamupatsa chifukwa chomukonda? N’zosachita kufunsa chifukwa mtumwi Yohane poyamba kulemba nkhani yochititsa chidwi yokhudza mchimwene wa Marita, ananena kuti: “Yesu anali kukonda onsewa, Marita ndi m’bale wake, ndiponso Lazaro.” (Yohane 11:5) Kenako panapita miyezi ingapo kuchokera pamene Yesu anacheza ku Betaniya. Marita anagwiritsa ntchito malangizo a Yesu ndipo sanamusungire chakukhosi chifukwa chomudzudzula. Pamenepanso Marita ndi chitsanzo chabwino kwa ife pa nkhani yachikhulupiriro chifukwa tonsefe nthawi zina timafunika kudzudzulidwa.

Pa nthawi imene mchimwene wake ankadwala, Marita anatanganidwanso kwambiri kumusamalira. Anachita chilichonse chimene akanatha kuti amuthandize kuchepetsa ululu umene ankamva komanso kuti apeze bwino. Komabe matenda a Lazaro ankangokulirakulira. Nthawi zonse azichemwali akewa ankakhala naye pafupi n’kumamusamalira. N’zodziwikiratu kuti nthawi zambiri Marita ankayang’ana nkhope ya mchimwene wakeyo, yomwe inkamvetsa chisoni, ndipo ankakumbukira zaka zambiri zimene anakhalira limodzi komanso zinthu zabwino komanso mavuto amene anakumana nawo pa moyo wawo.

Marita ndi Mariya ataona kuti matendawa awakulira, anatumiza uthenga kwa Yesu. Pa nthawiyi n’kuti Yesu akulalikira kudera lina, ndipo unali ulendo wa masiku awiri kukafika kumeneko. Uthenga wake unali wachidule, wakuti: “Ambuye! amene mumamukonda uja akudwala.” (Yohane 11:1, 3) Iwo ankadziwa kuti Yesu ankakonda kwambiri Lazaro ndipo anali ndi chikhulupiriro chakuti ayesetsa kumuthandiza. Kodi mwina iwo ankakhulupirira kuti Yesu afika zinthu zisanafike poipa? Ngati ndi choncho, zimene ankayembekezerazo si zimene zinachitika chifukwa Lazaro anamwalira Yesu asanafike.

Marita ndi Mariya analira maliro a mchimwene wawo ndipo anakonza dongosolo lonse lomuika m’manda komanso kulandira anthu obwera pamaliropo, ochokera ku Betaniya ndi m’madera ena apafupi. Koma mpaka pa nthawiyi Yesu anali asanafikebe. Marita ayenera kuti anayamba kudabwa kwambiri kuona kuti nthawi ikupita koma Yesu sakubwera. Tsopano patatha masiku anayi Lazaro atamwalira, Marita anamva kuti Yesu ali pafupi kufika ku Betaniya. Popeza Marita anali mayi wakhama kwambiri nthawi yomweyo ananyamuka kukakumana ndi Yesu ngakhale anali ndi chisoni. Iye anapita osatsazika Mariya.​—Yohane 11:20.

Marita atangoona Mbuye wakeyo anamuuza zimene iyeyo ndi Mariya anakhala akuganiza kwa masiku ambiri. Iye anati: “Ambuye, mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalira.” Ngakhale kuti Marita anali ndi chisoni, iye anali ndi chiyembekezo chakuti akufa adzauka ndipo ankakhulupirirabe Yesu. Iye ananenanso kuti: “Komabe, ngakhale tsopano ndikudziwa kuti zilizonse zimene mungapemphe Mulungu, Mulungu adzakupatsani zonsezo.” Nthawi yomweyo Yesu analankhula mawu omulimbikitsa akuti: “Mlongo wako adzauka.”​—Yohane 11:21-23.

Marita ankaganiza kuti Yesu ankanena za kuuka kwa akufa kumene kudzachitike m’tsogolo. Choncho anayankha kuti: “Ndikudziwa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa m’tsiku lomaliza. (Yohane 11:24) Marita ankakhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka. Atsogoleri ena achiyuda otchedwa Asaduki ankatsutsa zoti akufa adzauka. Iwo ankachita zimenezi ngakhale kuti, zoti akufa adzauka zinafotokozedwa momveka bwino m’Malemba. (Danieli 12:13; Maliko 12:18) Marita ankadziwa kuti Yesu ankaphunzitsa kuti akufa adzauka. Iye ankadziwanso kuti Yesu anaukitsapo akufa ngakhale kuti pa anthu amene anawaukitsawo panalibe amene anali atakhala m’manda kwa nthawi yaitali ngati Lazaro. Marita sanadziwe zimene Yesu achite.

Kenako Yesu ananena mawu osaiwalika akuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo.” Zimenezi n’zoona chifukwa Yehova Mulungu wapatsa Mwana wake mphamvu zoti m’tsogolo adzaukitse anthu padziko lonse lapansi. Choncho, Yesu anafunsa Marita kuti: “Kodi ukukhulupirira zimenezi?” Apa m’pamene Marita ananena mawu amene ndi mutu wa nkhani ino. Iye ankakhulupirira kuti Yesu ndi Khristu kapena kuti Mesiya komanso kuti ndi Mwana wa Yehova Mulungu. Ankakhulupiriranso kuti aneneri analosera kuti Yesu adzabwera padziko lapansi.​—Yohane 5:28, 29; 11:25-27.

Kodi Yehova Mulungu ndi Mwana wake Yesu Khristu amaona kuti chikhulupiriro ngati chimene Marita anali nacho ndi cha mtengo wapatali? Zimene Marita anaona zikuchitika, zingatithandize kupeza yankho lomveka bwino la funso limeneli. Kenako, Marita anathamanga kukaitana Mariya. Atabwera limodzi, iye anaona kuti Yesu anali ndi chisoni kwambiri pamene ankalankhula ndi Mariyayo komanso anthu ena amene ankalira malirowo. Marita anaona Yesu akugwetsa misozi posonyeza chisoni chachikulu chimene anali nacho chifukwa cha imfa ya Lazaro. Kenako, Marita anamva Yesu akuuza anthu kuti achotse chimwala chimene anatsekera pamanda a mchimwene wake.​—Yohane 11:28-39.

Marita anatsutsa zimenezi ponena kuti Lazaro ayenera kuti wayamba kununkha. Zimenezi zinali zomveka chifukwa panali patatha masiku anayi ali m’manda. Koma Yesu anamukumbutsa kuti: “Kodi sindinakuuze kuti ngati ukhulupirira udzaona ulemerero wa Mulungu?” Marita anakhulupiriradi ndipo anaona ulemerero wa Yehova Mulungu. Nthawi yomweyo Yehova anapatsa mphamvu Mwana wake zoukitsa Lazaro. Taganizirani zimene zinachitika pa nthawiyi, zimene mwina Marita sanaziiwale moyo wake wonse: Mawu a Yesu akuti, “Lazaro, tuluka!,” kaphokoso kochokera m’manda kosonyeza kuti Lazaro akudzuka ndipo akuyenda mpaka pakhomo la mandawo thupi lake litakulungidwa ndi nsalu zamaliro, Yesu akuuza anthu kuti, “m’masuleni ndi kumuleka apite” komanso chimwemwe chodzaza tsaya chimene Marita ndi Mariya anali nacho pamene anathamanga n’kukumbatira mchimwene wawoyo. (Yohane 11:40-44) Chisoni chonse chimene Marita anali nacho chinatheratu.

Nkhani imeneyi ikusonyeza kuti, mfundo yakuti akufa adzauka si nkhambakamwa chabe, koma ndi zimenedi Baibulo limaphunzitsa. Zimene zinachitikazi ndi umboni wakuti akufa adzaukadi. Yehova ndi Mwana wake amafuna kupereka mphoto kwa anthu amene ali ndi chikhulupiriro ngati mmene anachitira ndi Marita, Mariya ndi Lazaro. Inunso, Yehova ndi Yesu adzakupatsani mphoto ngati muli ndi chikhulupiriro champhamvu ngati cha Marita. *

“Marita Anali Kutumikira”

Palinso nkhani ina m’Baibulo imene Marita akutchulidwa komaliza. Nthawi imeneyi ndi chakumayambiriro kwa mlungu womaliza wa utumiki wa Yesu padziko lapansi. Podziwa kuti akumana ndi mavuto posachedwa, Yesu anasankhanso kukakhala ku Betaniya. Anakonza zoti akakachoka kumeneko, ayende ulendo wamakilomita atatu wopita ku Yerusalemu. Yesu ndi Lazaro anapita limodzi ku nyumba ya Simoni wa khate kumene anakadya chakudya. Pa nthawi imeneyi ndi pamene Baibulo limatchulanso za Marita kuti: “Marita anali kutumikira.”​—Yohane 12:2.

Mayi ameneyu analidi wolimbikira ntchito kwambiri. Pomwe Baibulo linamutchula koyamba, n’kuti akugwira ntchito ndipo pamene likumutchula komaliza n’kutinso akugwira ntchito potumikira anthu. Masiku ano m’mipingo ya otsatira Khristu mulinso azimayi ofanana ndi Marita. Azimayi amenewa, amasonyeza chikhulupiriro chawo mwa kudzipereka potumikira ena ndipo amachita zimenezi ndi mtima wonse. Zikuoneka kuti Marita anapitirizabe kuchita zimenezi. Ngatidi ndi choncho ndiye kuti anachita zinthu mwanzeru chifukwa posapita nthawi iye anali kudzakumananso ndi mavuto.

Patangopita masiku ochepa, Marita anamva chisoni kwambiri chifukwa cha imfa ya Mbuye wake Yesu. Komanso anthu oipa amene anapha Yesu, anafunanso kupha Lazaro chifukwa kuuka kwake kunachititsa kuti anthu ambiri akhulupirire Yesu. (Yohane 12:9-11) Komanso patapita nthawi imfa inalekanitsa Marita ndi abale ake. Sitikudziwa kuti anthu amenewa anafa imfa yotani komanso kuti anafa liti. Komabe sitikukayika kuti Marita anali ndi chikhulupiriro cholimba kwambiri chimene chinamuthandiza moyo wake wonse. N’chifukwa chake Akhristu masiku ano ayenera kutsanzira chikhulupiriro cha Marita.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 27 Kuti mudziwe zambiri za zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani yakuti akufa adzauka, werengani mutu 7 m’buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 11]

Ngakhale pa nthawi imene anali ndi chisoni, Marita analola kuti Yesu amuthandize kuganizira zinthu zimene zingalimbikitse chikhulupiriro chake

[Chithunzi patsamba 12]

Ngakhale kuti Marita ‘anada nkhawa ndiponso anatanganidwa,’ iye anamvera malangizo a Yesu modzichepetsa

[Chithunzi patsamba 15]

Marita anadalitsidwa chifukwa chokhulupirira Yesu ndipo anaona mchimwene wake akuukitsidwa