Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Moyo Wosatha M’Paradaiso Udzafika Potopetsa?

Kodi Moyo Wosatha M’Paradaiso Udzafika Potopetsa?

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Moyo Wosatha M’Paradaiso Udzafika Potopetsa?

▪ Baibulo limapereka chiyembekezo choti anthu angathe kukhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso pa dziko lapansi. (Salimo 37:29; Luka 23:43) Kodi kukhala ndi moyo mpaka kalekale m’dziko lopanda mavuto kudzakhala kotopetsa?

M’pofunikadi kudziwa yankho la funso limeneli chifukwa ofufuza apeza kuti munthu akamangopanga chinthu chomwechomwecho amayamba kukhala ndi nkhawa, kukhala wosasangalala komanso amayamba kupanga zinthu zoti zikhoza kumupha. Anthu amene amaona kuti alibe cholinga pamoyo kapena amene amangochita zinthu zomwezo tsiku ndi tsiku, ndi amene amatopa ndi moyo. Kodi anthu amene adzakhale ndi moyo m’Paradaiso adzakhala opanda cholinga pa moyo wawo? Kodi zimene tizidzachita tsiku ndi tsiku zidzatitopetsa moti tidzayamba kunyong’onyeka?

Choyamba, dziwani kuti Yehova Mulungu, amene analemba Baibulo, ndi yemwe akutilonjeza za moyo wosatha. (Yohane 3:16; 2 Timoteyo 3:16) Khalidwe lalikulu la Mulungu ndi chikondi. (1 Yohane 4:8) Yehova amatikonda kwambiri ndipo iye ndi amene anatipatsa zinthu zabwino zonse zimene tili nazo.​—Yakobo 1:17.

Mlengi wathu amadziwa kuti, kuti tisangalale tikufunikira kukhala ndi ntchito yopindulitsa. (Salimo139:14-16; Mlaliki 3:12) M’Paradaiso anthu sazidzagwira ntchito mongodzikakamiza koma adzakhala ndi ntchito yabwino ndiponso yosangalatsa. Ntchito imene azidzagwirayo idzakhala yopindulitsa kwa iwowo komanso kwa anthu amene amawakonda. (Yesaya 65:22-24) Ndiye kodi mutakhala pa ntchito yabwino komanso imene mumaikonda kwambiri, mungatope nayo?

Chinanso chimene mungadziwe n’choti Yehova Mulungu sikuti adzangolola wina aliyense kuti akhale m’Paradaiso. Iye adzapereka mphatso ya moyo wosatha kwa anthu okhawo omwe amatsanzira Mwana wake Yesu. (Yohane17:3) Pamene Yesu anali padziko lapansi, ankasangalala kuchita chifuniro cha Atate wake. Zimene ankalankhula komanso kuchita zinathandiza otsatira ake kudziwa kuti kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira. (Machitidwe 20:35) M’dziko la Paradaiso likubweralo, anthu onse azidzayendera malamulo akuluakulu awiri. Malamulo amenewa ndi kukonda Mulungu ndiponso kukonda anthu. (Mateyu 22:36-40) Tangoganizani, anthu onse azidzakukondani ndiponso azidzakonda ntchito yawo. Kodi mukuganiza kuti kukhala ndi anthu oterewa kungakupangitseni kuti mutope ndi moyo?

Palinso chinthu china chomwe chidzapangitse kuti moyo m’Paradaiso usakhale wotopetsa. Tsiku lililonse tizidzaphunzira zinthu zatsopano zokhudza Mlengi wathu. Akatswiri ofufuza apeza zinthu zambiri zodabwitsa zimene Yehova analenga. (Aroma 1:20) Komabe panopa timangodziwa zinthu zochepa chabe za zimene Mulungu analenga. Zaka zambiri zapitazo Yobu, yemwe anali munthu wokhulupirika, anafotokoza zomwe ankadziwa ponena za zimene Mulungu analenga ndipo zomwe ananenazo zidakali zoona. Iye anati: “Zimenezi ndi kambali kakang’ono chabe ka zochita [za Mulungu], ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake. Koma kodi mabingu ake amphamvu, angawamvetse ndani?”​—Yobu 26:14.

Ngakhale kuti tidzakhala ndi moyo wosatha, sitidzatha kuphunzira zonse zokhudza Yehova Mulungu ndi zimene analenga. Baibulo limanena kuti Mulungu anatipatsa mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Koma limanenanso kuti sizingatheke kuti anthufe tidziwe ‘ntchito imene Mulungu woona wagwira, kuyambira pa chiyambi mpaka pa mapeto.’ (Mlaliki 3:10, 11) Kodi mukuganiza kuti moyo ungadzakhale wotopetsa mukamadzaphunzira zinthu zatsopano zokhudza Mlengi wanu?

Ngakhale masiku ano, anthu omwe amatanganidwa ndi ntchito yothandiza ena komanso yothandiza kuti dzina la Mulungu lilemekezedwe saona kuti moyo ndi wotopetsa. Ifenso tikamatanganidwa kugwira nawo ntchito imeneyi, sitingatope ndi moyo panopa ndipo sitidzatopanso ndi moyo wosatha m’Paradaiso.

[Mawu a Chithunzi patsamba 27]

Earth: Image Science and Analysis Laboratory, NASA-Johnson Space Center; Galaxy: The Hubble Heritage Team (AURA/​STScI/​NASA)