Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chinsinsi cha Banja Losangalala

Kodi Zinthu Zimasintha Bwanji M’banja Mukabadwa Mwana?

Kodi Zinthu Zimasintha Bwanji M’banja Mukabadwa Mwana?

Charles: * “Ine ndi mkazi wanga Mary tinasangalala kwambiri mwana wathu wamkazi atabadwa. Komabe mwa miyezi ingapo mwanayu atangobadwa, sitinkagona mokwanira. Mwana wathu asanabadwe, tinakonzekera mmene tidzamulerere koma atabadwa zonsezo zinaiwalika.”

Mary: “Mwana wathu atangobadwa, moyo wanga unasintha kwambiri. Maganizo anga onse ankangokhala pa kusamalira mwanayo basi. Kumupezera botolo lina la mkaka, kumusintha thewera, kapena kumutonthoza akamalira. Zinthu zinasinthadi kwambiri ndipo panatenga miyezi ingapo kuti ine ndi mwamuna wanga Charles tiyambenso kukondana ngati kale.”

AMBIRI angavomereze kuti kukhala ndi ana ndi chimodzi mwa zinthu zosangalatsa kwambiri. Ndipo Baibulo limanena kuti ana ndi “mphoto” yochokera kwa Mulungu. (Salimo 127:3) Koma mwamuna ndi mkazi ngati Charles ndi Myriam, amene angobereka kumene mwana wawo woyamba, amadziwanso kuti m’banja mukabadwa mwana zinthu zimasintha mosayembekezereka. Mwachitsanzo mayi amene wabereka koyamba angamaganizire kwambiri za mwanayo moti angadabwe kuona kuti mtima wake wonse uli pa mwana wakeyo. Iye nthawi zonse amakhala wokonzeka kumusamalira ngakhale pa zinthu zazing’ono. Komanso mwamuna angachite chidwi kwambiri ndi mmene mkaziyo akukonderana ndi mwana wawoyo komabe angayambenso kuda nkhawa kuti mwina mkazi wake sadzimukondanso ngati kale.

Ndipotu kubadwa kwa mwana woyamba kungabweretse mavuto m’manja. Mwachitsanzo, ngati awiriwo anali ndi nkhawa ndiponso ngati panali mavuto ena amene anali asanawathetse, mwana akabadwa mavuto aja amayamba kuoneka ngati aakulu chifukwa pa nthawiyi udindo wawo umakhala utawonjezeka.

Ndiye kodi mwamuna ndi mkazi amene angobereka kumene mwana woyamba, angatani kuti zinthu ziziyenda bwino pa nthawi imeneyi, yomwe mwanayo akufunika chisamaliro chawo chonse? Kodi angatani kuti apitirizebe kukondana? Nanga angathetse bwanji kusamvana pa nkhani ya mmene angalerere mwanayo? Tiyeni tikambirane mafunso amenewa komanso mfundo za m’Baibulo zimene zingathandize mwamuna ndi mkazi wake kuthana ndi mavuto amenewa.

VUTO LOYAMBA: Chidwi chonse chimayamba kupita kwa mwanayo.

Mwana akabadwa, nthawi komanso maganizo onse a mayi amakhala pa mwanayo. Iye amaganizira kwambiri za udindo wake wokonda komanso kusamalira mwanayo. Pamene mwamuna angamaone ngati mkazi wake sakumusamalanso. Manuel amene amakhala ku Brazil, anati: “Chidwi chonse cha mkazi wanga chinayamba kukhala pa mwana wathu ndipo zimenezi zinanditengera nthawi yaitali kuti ndizizolowere. M’mbuyomu tinkasangalala tili awiriwiri koma kenako zinthu zinasintha, nkhani inkangokhala ya mwana basi.” Kodi mungatani zinthu zikatere?

Zimene mungachite: Khalani oleza mtima.

Baibulo limati: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima.” Limatinso chikondi “sichisamala zofuna zake zokha, sichikwiya.” (1 Akorinto 13:4, 5) M’banja mukabadwa mwana, kodi mwamuna ndi mkazi angagwiritse ntchito bwanji malangizo amenewa?

Mwamuna wanzeru angasonyeze kuti amakonda mkazi wake akamvetsa mmene kubadwa kwa mwana kumakhudzira thupi ndiponso maganizo a mkazi wake. Akatero angamvetsenso chifukwa chake mkazi wake amatha kusinthasintha, pena kukhala wosangalala pena wokhumudwa. * Adam, amene amakhala ku France ndipo ali ndi mwana wamkazi wa miyezi 11, nayenso anavomereza mfundo imeneyi. Iye anati: “Zimakhala zovuta kumumvetsa mkazi wako akamakhumudwakhumudwa. Komabe ineyo ndimadziwa kuti sikuti wandikwiyira ayi koma kuti udindo umene wayamba kukhala nawo ndi umene ukumupangitsa kuti azikhala wotopa komanso wankhawa.”

Kodi nthawi zina mkazi wanu samakumvetsani mukamayesetsa kuchita zinthu zina zomuthandiza? Ngati ndi choncho, musafulumire kukwiya. (Mlaliki 7:9) M’malomwake lezani mtima ndipo yesetsani kuchita zofuna zake osati zanu ndipo zimenezi zingakuthandizeni kuti musakhumudwe.​—Miyambo 14:29.

Nayenso mkazi wozindikira amayesetsa kulimbikitsa mwamuna wake kuti akwaniritse udindo wake wolera mwana. Amayesetsa kuchita zinthu zimene zingathandize kuti mwamuna wake nayenso azithandiza pa ntchito yosamalira mwana. Moleza mtima amaphunzitsa mwamuna wakeyo kuchita zinthu zina monga kusintha mwana thewera komanso kukonza botolo la mkaka la mwanayo. Iye amachitabe zimenezi ngakhale poyamba zitaoneka kuti mwamunayo akulephera.

Mayi wa zaka 26, dzina lake Ellen, anazindikira kuti anayenera kusintha mmene ankachitira zinthu ndi mwamuna wake. Iye anati: “Ndinayenera kusiya kuchita zinthu zosonyeza ngati mwanayo ndi wanga yekha. Komanso ndinafunika kukumbukira kuti si nthawi zonse pamene ndinkafunikira kudzudzula mwamuna wanga akalakwitsa posamalira mwana wathu.”

TAYESANI IZI: Azimayi, mwamuna wanu akamachita zinthu mosiyana ndi mmene inuyo mumachitira posamalira mwana, pewani kumulankhula mawu onyoza kapena kubwerezanso kuchita zinthu zimene iyeyo wachita kale. Koma muyamikireni pa zimene amachita bwino ndipo zimenezo zidzamulimbikitsa kuti apitirize kukuthandizani nthawi zonse pa ntchito yosamalira mwana. Azibambo, mungachepetse nthawi imene mumathera pa zinthu zosafunika kwenikweni kuti mukhale ndi nthawi yambiri yothandiza mkazi wanu, makamaka pa miyezi yoyambirira mwana akangobadwa.

VUTO LACHIWIRI: Chikondi chimayamba kuchepa.

Chifukwa chosagona mokwanira komanso mavuto ena osayembekezereka, makolo amene angobereka kumene zimawavuta kupitirizabe kukondana. Mayi wina wa ku France dzina lake Vivianne yemwe ali ndi ana aang’ono awiri anavomereza zimenezi. Iye ananena kuti: “Poyamba ndinkatanganidwa kwambiri ndi kusamalira ana moti ndinayamba kuiwala kuti ndine wokwatiwa.”

Nayenso mwamuna angalephere kuzindikira kuti, kukhala woyembekezera komanso uchembere zingakhudze thanzi ndiponso maganizo a mkazi wake. Komanso mwana akabadwa, makolo angamathere mphamvu komanso nthawi yambiri akusamalira mwanayo moti angamakhale ndi nthawi yochepa yocheza ngati munthu ndi mkazi wake. Ndiyeno, kodi makolo angatani kuti mwana wawo amene amamukondayo asasokoneze chikondi chawo?

Zimene mungachite: Muzichita zinthu zosonyeza kuti mukukondanabe.

Ponena za ukwati, Baibulo limati: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.” * (Genesis 2:24) Yehova Mulungu anakonza zoti ana akakula azisiya makolo awo. Koma Mulungu amafuna kuti anthu okwatirana akhale thupi limodzi kwa moyo wawo wonse. (Mateyu 19:3-9) Kodi kuzindikira mfundo imeneyi kungathandize bwanji makolo amene angobereka kumene mwana kupitiriza kuika zinthu zofunika pa malo oyamba?

Vivianne, amene tamutchula poyamba uja ananena kuti: “Ndinaganizira mawu a palemba la Genesis 2:24 ndipo anandithandiza kuzindikira kuti ndine ‘thupi limodzi’ ndi mwamuna wanga, osati ndi mwana wanga. Choncho ndinaona kuti m’pofunika kuti ndiyambenso kukonda kwambiri mwamuna wanga kuti banja lathu lilimbe.” Theresa, mayi yemwe ali ndi mwana wa zaka ziwiri, anati: “Ndikazindikira kuti chikondi chathu chayamba kuchepa, nthawi yomweyo ndimayesetsa kumuchitira mwamuna wanga zinthu zosonyeza kuti ndimamukonda. Ndimayesetsa kuchita zimenezi tsiku ndi tsiku ngakhale zitakhala kuti ndi kwanthawi yochepa.”

Ngati ndinu mwamuna wokwatira, kodi mungatani kuti mulimbitse banja lanu? Muzimuuza mkazi wanu kuti mumamukonda. Mukatero, muzichita zinthu zosonyeza kuti mumamukondadi. Ngati mkazi wanu akuoneka kuti ali ndi nkhawa, yesetsani kumuthandiza kuti nkhawa zakezo zithe. Mayi wina wa zaka 30 dzina lake Sarah ananena kuti: “Mkazi amafuna kuti adziwe kuti mwamuna wake amamukondabe ndiponso mwamunayo amamuonabe kuti ndi wofunika ngakhale kuti sakuonekanso ngati mmene analili asanabereke.” Bambo wina wa ku Germany dzina lake Alan yemwe ali ndi ana awiri, amadziwa kufunika kothandiza mkazi kuti asamakhale ndi nkhawa. Iye ananena kuti: “Nthawi zonse ndimayesetsa kulimbikitsa mkazi wanga akakhala kuti akuda nkhawa ndi zinazake.”

M’banja mukabadwa mwana, nthawi zambiri zimakhala zovuta kuti mwamuna ndi mkazi wake akhale malo amodzi ngati mmene ankachitira poyamba. Choncho iwo ayenera kukambirana kuti adziwe zimene zingakhale zokomera aliyense wa iwo. Baibulo limanena kuti ngati pangafunike kusintha pa nkhani zokhudza kugonana, anthu okwatirana ayenera ‘kugwirizana.’ (1 Akorinto 7:1-5) Koma kuti zimenezi zitheke, pangafunike kukambirana. Mwina chifukwa cha chikhalidwe chanu komanso kumene munakulira zingakhale zovuta kuti mukambirane nkhani zoterezi ndi mkazi kapena mwamuna wanu. Komabe kukambirana n’kofunika kuti muzolowerane ndi moyo watsopano monga makolo. Yesetsani kumva mmene mnzanuyo akumvera, khalani woleza mtima komanso yesetsani kuuzana zakukhosi. (1 Akorinto 10:24) Zimenezi zingathandize kuti muthetse kusamvana komanso mukulitse chikondi chanu.​—1 Petulo 3:7,8.

Kuyamikirana kungathandizenso anthu okwatirana kukulitsa chikondi chawo. Mwamuna wanzeru amazindikira kuti pali ntchito zambiri zimene mkazi wake amachita posamalira mwana wawo zimene mwamunayo sangazidziwe zonse. Vivianne uja ananena kuti: “Ngakhale kuti tsiku lonse ndimachita zinthu zambiri kusamalira mwana, tsiku likamatha, ndimangoona ngati palibe chimene ndachita.” Ngakhale kuti mkazi amakhala wotanganidwa kwambiri, iye sayenera kunyozetsa zimene mwamuna wake akuyesetsa kuchita pothandiza banja lawo.​—Miyambo 17:17.

TAYESANI IZI: Amayi, ngati zingatheke yesetsani kumapeza mpata wogonako pamene mwana wanu wagona. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti mupezenso mphamvu zosamalirira banja lanu. Abambo, ngati mungakwanitse, muzidzuka usiku kuti musinthe thewera mwana wanu kapena kumumwetsa mkaka kuti mkazi wanu agoneko. Nthawi ndi nthawi muziyesetsa kuuza mkazi wanu mawu achikondi, kumulembera kakalata kachikondi, kumutumuzira mauthenga pa foni, kapena kumuimbira foni kumene. Muzipeza nthawi yokambirana nkhani zina muli awiriawiri. Pa nthawi imeneyi muzikambirana nkhani zokhudza awirinu osati za mwana wanu. Yesetsani kuti muzikondana kwambiri chifukwa zimenezi zidzakuthandizani kudziwa zimene mungachite ngati mutakumana ndi vuto lililonse polera mwana.

VUTO LACHITATU: Kusagwirizana pa nkhani yolera mwana.

Chifukwa chakuti makolo anakulira kosiyana, nthawi zina angasemphane maganizo pa nkhani ya mmene angalerere mwana wawo. Zimenezi ndi zimene zinkachitikira mayi wina wa ku Japan, dzina lake Asami ndi mwamuna wake, Katsuro. Asami ananena kuti: “Ndinkaona kuti mwamuna wanga akumulekerera mwana wathu pamene iyeyo ankaona kuti ineyo ndinkamuchitira nkhanza mwanayo.” Ndiyeno kodi mungatani kuti musamapange zosiyana polangiza mwana wanu?

Zimene mungachite: Muzikambirana komanso muzithandizana.

Solomo, yemwe anali mfumu yanzeru, analemba kuti: “Chifukwa cha kudzikuza, munthu amangoyambitsa mavuto, koma anthu amene amakhala pamodzi n’kumakambirana amakhala ndi nzeru.” (Miyambo 13:10) Kodi mumadziwa zimene mwamuna kapena mkazi wanu amaganiza kuti n’zoyenera pa nkhani yolera mwana? Ngati mungadikire kuti mwana abadwe musanakambirane nkhani zimenezi, mudzaona kuti muzidzangokangana m’malo mopeza njira zabwino zothetsera mavuto.

Mwachitsanzo, mungafunike kukambirana ndi kugwirizana zimene mudzachite pa nkhani ngati izi: “Kodi tingaphunzitse bwanji mwana wathu makhalidwe abwino pa nkhani ya kudya ndi kugona? Mwana akayamba kulira usiku, kodi nthawi zonse tiyenera kumunyamula? Kodi tingaphunzitse bwanji mwana wathu zinthu zoyenera kuchita akapita kuchimbudzi?” N’zodziwikiratu kuti zimene inu mungasankhe pa nkhani zimenezi zingakhale zosiyana ndi zimene mabanja ena angasankhe. Bambo wina dzina lake Ethan ndipo ali ndi ana awiri ananena kuti: “Pamafunika kukambirana kuti mugwirizane. Zimenezi zingathandize kuti muzisamalira bwino mwana wanu.”

TAYESANI IZI: Ganizirani njira zimene makolo anu ankatsatira pokulerani ndipo onani ngati pali njira zina zabwino zimene iwo ankatsatira zomwe mukuona kuti mungathe kuzitsanzira polera mwana wanu. Muonenso njira zimene makolo anu ankatsatira zomwe inuyo simuyenera kuzitsatira. Kenako kambiranani zimene mwasankhazo.

Mwana Angathandize Kuti Banja Liziyenda Bwino

Munthu amene akungophunzira kumene kukwera njinga amafunika kuchita khama chifukwa zimatenga nthawi kuti aidziwe bwinobwino. Mofanana ndi zimenezi, makolo amene angobereka kumene mwana afunikanso kuchita khama mpaka atafika podziwa bwino kusamalira mwana wawo.

Ntchito yolera mwana ingachititse kuti musonyeze ngati mukukondanabe kapena ayi. Ingathenso kusintha ubwenzi wanu mpaka kalekale. Ingakuthandizeninso kukhala ndi makhalidwe abwino. Kutsatira malangizo a m’Baibulo pa nkhaniyi, kungakuthandizeni ngati mmene kunathandizira bambo wina dzina lake Kenneth. Iye anati: “Kulera mwana kwathandiza kwambiri ineyo komanso mkazi wanga chifukwa kwatichititsa kuti aliyense asamangoganizira zofuna zake ngati mmene tinkachitira poyamba. Panopa timakondana kwambiri komanso timamvetsetsana.” Mosakayikira, banja lililonse lingafune kuti kubadwa kwa mwana kuthandize kuti banja lawo liziyenda bwino.

^ ndime 3 Tasintha mayina ena m’nkhani ino.

^ ndime 11 Azimayi ambiri amavutika maganizo kwa milungu yochepa akangobereka kumene. Koma ena amadwala matenda enaake ovutika maganizo amene azimayi omwe angobereka kumene amadwala. Kuti mudziwe zimene mungachite pofuna kuzindikira komanso kuthana ndi matenda amenewa, werengani nkhani yakuti “Ndinagonjetsa Vuto Langa Losokonezeka Maganizo Nditabereka,” mu Galamukani! ya August 8, 2002, ndi yakuti “Understanding Postpartum Depression,” mu Galamukani! yachingerezi ya June 8, 2003. Magazini amenewa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Mungawerengenso nkhani zimenezi m’Chingelezi pa Intaneti pogwiritsa ntchito adiresi iyi, www.pr418.com.

^ ndime 19 Buku lina linanena kuti mawu achiheberi amene pa Genesis 2:24 anawamasulira kuti “kudziphatika” angatanthauze ‘kusafuna kusiya munthu winawake chifukwa chomukonda ndiponso kufuna kukhalabe wokhulupirika kwa iye.’

DZIFUNSENI KUTI:

  • Mlungu wathawu, kodi ndinachita chiyani pofuna kusonyeza kuti ndimayamikira zimene mwamuna kapena mkazi wanga amachita pothandiza banja lathu?

  • Kodi ndi liti pamene ndinacheza ndi mwamuna kapena mkazi wanga nkhani zakukhosi, osati zokhudza mwana wathu?