Ulosi Wachisanu: Kuwononga Dziko
Ulosi Wachisanu: Kuwononga Dziko
‘[Mulungu] adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.’—CHIVUMBULUTSO 11:18.
● A Pirri, omwe amakhala ku Kpor ku Nigeria, amagwira ntchito yokonza uchema, mowa wopangidwa kuchokera ku mtengo wa mgwalangwa. Koma ntchito yawoyi sikuyenda bwino chifukwa cha mafuta amene anatayikira kudera la Niger Delta. A Pirri ananena kuti: “Mafuta amenewa akupha nsomba. Akuwononganso khungu lathu komanso madzi a m’timitsinje tina moti panopa ndikusowa njira yopezera ndalama.”
KODI ULOSIWU UKUKWANIRITSIDWADI? Malinga ndi zimene akatswiri ena anena, chaka chilichonse zinyalala zolemera matani 6.5 miliyoni zimatayidwa mu nyanja zikuluzikulu. Ndipo ena akuganiza kuti hafu ya zinyalala zimenezi, ndi zinthu zapulasitiki zimene zimatenga zaka zambiri kuti ziwole. Kuwonjezera pa kuwononga dzikoli, anthu akuwononganso zinthu zachilengedwe mochititsa mantha kwambiri. Kafukufuku akusonyeza kuti pangafunike chaka ndi miyezi isanu kuti dziko lapansili libwezeretse zinthu zachilengedwe zimene anthu amawononga pa chaka chimodzi. Ndipo nyuzipepala ina ya ku Australia inanena kuti: “Ngati chiwerengero cha anthu chipitirire kukwera komanso ngati tipitirize kuwononga zachilengedwe, ndiye kuti podzafika chaka cha 2035 tidzafunika kukhala ndi dziko lapansili ndi linanso ngati lomweli kuti tizikhala bwinobwino.”—Sydney Morning Herald.
KODI ANTHU AMBIRI AMATI CHIYANI POTSUTSA ULOSI UMENEWU? Anthu ndi anzeru kwambiri moti akhoza kupeza njira zothetsera mavuto amenewa, dzikoli n’kubweranso mwakale.
KODI ZIMENEZI N’ZOONA? Pali mabungwe ndiponso anthu ambiri amene akuphunzitsa anthu kufunika koteteza zinthu zachilengedwe. Koma anthu akupitirizabe kuwononga kwambiri dzikoli.
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi m’pofunikadi kuti Mulungu achite zimene analonjeza n’kupulumutsa dzikoli m’manja mwa anthu amene akuliwononga?
Kuwonjezera pa maulosi asanu amene takambiranawa, Baibulo limanenanso za ulosi wina wabwino umene ukukwaniritsidwa m’masiku otsiriza ano. Taonani ulosi umenewu m’nkhani yotsatira.
[Mawu Otsindika patsamba 8]
“Ndikungoona ngati ndachoka pamalo aparadaiso n’kukhala pamalo omwe atayirako zinyalala zapoizoni.”—ERIN TAMBER, WA KU GULF COAST M’DZIKO LA UNITED STATES. IYE ANANENA ZIMENEZI POFOTOKOZA MMENE KUTAIKA KWA MAFUTA KU GULF OF MEXICO M’CHAKA CHA 2010 KUNAMUKHUDZIRA.
[Bokosi patsamba 8]
Kodi Mulungu Ndi Amene Akuchititsa Mavuto Padzikoli?
Popeza Baibulo linaneneratu za zinthu zoipa zimene zikuchitika masiku ano, kodi ndiye kuti Mulungu ndi amene akuzichititsa? Kodi iye ndi amene amachititsa kuti tizivutika? Mungapeze mayankho ogwira mtima a mafunso amenewa m’mutu 11 wa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi chachikulu patsamba 8]
U.S. Coast Guard photo