Kodi Akhristu Onse Okhulupirika Amapita Kumwamba?
Zimene Owerenga Amafunsa . . .
Kodi Akhristu Onse Okhulupirika Amapita Kumwamba?
▪ Anthu ambiri anawerengapo mawu olimbikitsa a Yesu akuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Kodi palembali Yesu ankatanthauza kuti atumiki okhulupirika onse a Atate wake Yehova Mulungu, adzapita kumwamba kukasangalala ndi moyo wosatha?
Taonaninso mawu awa ofunika kuwaganizira amene Yesu ananena. Iye anati: “Palibe munthu amene anakwera kumwamba koma Mwana wa munthu yekha, amene anatsika kuchokera kumwambako.” (Yohane 3:13) Zimenezi zikutanthauza kuti atumiki okhulupirika akale monga Nowa, Abulahamu, Mose ndiponso Davide sanapite kumwamba. (Machitidwe 2:34) Ndiyeno kodi anthu amenewa anapita kuti? Kunena mwachidule, anthu okhulupirika amenewa ali kumanda ndipo akugona mu imfa. Iwo sakudziwa chilichonse ndipo akungoyembekezera kudzaukitsidwa.—Mlaliki 9:5, 6; Machitidwe 24:15.
Yesu ndi amenenso anali munthu woyamba kutchula mfundo yakuti anthu ena akadzamwalira adzapita kumwamba. Iye anauza atumwi ake kuti akukawakonzera malo kumwamba. (Yohane 14:2, 3) Mfundo imeneyi inali yatsopano kwa atumiki a Mulungu. Patapita nthawi, mtumwi Paulo anafotokoza kuti pambuyo poti Yesu wafa n’kuukitsidwa kupita kumwamba, ‘anakhazikitsira ophunzira ake njira yatsopano yamoyo’ imene panalibe wina aliyense amene anayendamo chiyambire.—Aheberi 10:19, 20.
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti kuyambira nthawi imeneyo anthu onse okhulupirika amapita kumwamba? Ayi, chifukwa anthu amene amaukitsidwa n’kupita kumwamba ndi okhawo amene anapatsidwa ntchito yoti akagwire kumwambako. Pa usiku womaliza ali ndi ophunzira ake, Yesu anawauza kuti iwo ‘akakhala m’mipando yachifumu,’ mu Ufumu wake kumwamba. Zimenezi zikutanthauza kuti iwo adzagwira ntchito yolamulira ndi Yesu kumwamba.—Luka 22:28-30.
Kuwonjezera pa atumwi a Yesu, palinso anthu ena amene adzagwire nawo ntchito yapadera imeneyi. Mtumwi Yohane anaona m’masomphenya Yesu ali ndi anthu omwe anaukitsidwa n’kupita kumwamba omwe Baibulo limati ndi ‘mafumu ndi ansembe olamulira dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 3:21; 5:10) Kodi anthu amenewa anali angati? Monga zimakhalira ndi boma lina lililonse, pamakhala anthu ochepa amene amalamulira. Ndi mmenenso zilili ndi Ufumu wakumwamba. Yesu, yemwe ndi Mwanawankhosa wa Mulungu, adzalamulira ndi anthu 144,000 amene “anagulidwa kuchokera mwa anthu.”—Chivumbulutso 14:1, 4, 5.
Anthu okwana 144,000 ndi ochepa kwambiri tikayerekeza ndi chiwerengero cha anthu onse okhulupirika akale komanso a masiku ano. Koma zimenezi n’zomveka chifukwa anthu 144,000 amenewa amaukitsidwa kuti apite kumwamba n’cholinga choti adzagwire ntchito yapadera. Mwachitsanzo, kodi inuyo mutakhala kuti mukufuna kumanga nyumba, mungalembe ntchito anthu onse a m’dera lanu odziwa kumanga nyumba? N’zodziwikiratu kuti simungatero, koma mungalembe anthu ochepa okha mogwirizana ndi kuchuluka kwa ntchitoyo. Mofanana ndi zimenezi, Mulungu sanasankhe anthu okhulupirika onse kuti akagwire ntchito yapadera imeneyi yolamulira ndi Khristu kumwamba.
Boma lakumwamba limeneli lidzakwaniritsa cholinga chimene Mulungu anali nacho poyamba chokhudza anthu. Yesu ndi olamulira anzake okwana 144,000 azidzayang’anira ntchito yosintha dziko lonse lapansi kukhala paradaiso. M’dziko limeneli, anthu osawerengeka okhulupirika adzakhalamo mosangalala kwamuyaya. (Yesaya 45:18; Chivumbulutso 21:3, 4) Anthu amenewa akuphatikizapo anthu amene Mulungu akuwakumbukira omwe adzawaukitse.—Yohane 5:28, 29.
Anthu onse olambira Mulungu mokhulupirika, kaya a m’nthawi yakale kapena a masiku ano, angalandire mphatso yamtengo wapatali ya moyo wosatha. (Aroma 6:23) Choncho, anthu owerengeka adzapita kumwamba kukagwira ntchito yapadera ndipo anthu ambirimbiri adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi m’paradaiso.