Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Akufa Adzauka?

Kodi Akufa Adzauka?

Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

Kodi Akufa Adzauka?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi pali chiyembekezo chotani chokhudza anthu amene anamwalira?

Tsiku lina Yesu anafika ku Betaniya, mudzi womwe unali pafupi ndi Yerusalemu ndipo pa nthawiyi n’kuti patatha masiku anayi kuchokera pamene mnzake Lazaro anamwalira. Yesu anapita kumanda kumene Lazaro anali ataikidwa. Iye anapita ndi Marita komanso Mariya omwe anali alongo ake a Lazaro ndipo pasanapite nthawi anthu ambiri anafikanso kumandako. Taganizirani mmene Marita ndi Mariya anasangalalira Yesu ataukitsa Lazaro.​—Werengani Yohane 11:20-24, 38-44.

Marita ankakhulupirira kuti anthu amene anamwalira adzaukitsidwa. Kuyambira kale, atumiki okhulupirika a Yehova amadziwa kuti m’tsogolo, Mulungu adzaukitsa anthu amene anamwalira kuti akhalenso ndi moyo padziko lapansi.​—Werengani Yobu 14:14, 15.

2. Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

Munthu ali ndi mphamvu yamoyo, kapena kuti “mzimu,” imene imapangitsa kuti akhale wamoyo. Komabe iye si mzimu umene anthu amakhulupirira kuti umakhala m’thupi la munthu. (Mlaliki 3:19; Genesis 7:21, 22) Anthufe tili ndi thupi lopangidwa ndi fumbi. (Genesis 2:7; 3:19) Ubongo wathu ukafa, timasiya kuganiza. N’chifukwa chake Lazaro ataukitsidwa sanafotokoze kuti pali chilichonse chimene chinamuchitikira chifukwa pa nthawi yonse imene anali wakufa, sankadziwa chilichonse.​—Werengani Salimo 146:4; Mlaliki 9:5, 10.

Ndiyetu n’zoonekeratu kuti akufa savutika. Choncho chiphunzitso chakuti Mulungu amazunza anthu oipa akafa n’chabodza. Chiphunzitso chimenechi chimachititsa kuti anthu aziona ngati Mulungu ndi woipa. Mulungu amanyansidwa kwambiri ndi khalidwe lowotcha anthu pamoto.​—Werengani Yeremiya 7:31.

3. Kodi n’zotheka kulankhula ndi anthu akufa?

Anthu akufa sangalankhule. (Salimo 115:17) Ziwanda ndi zimene zimalankhula ndi anthu ponamizira kuti mzimu wa munthu wakufa ndi umene ukulankhula. (2 Petulo 2:4) Yehova amaletsa anthu kulankhula ndi akufa.​—Werengani Deuteronomo 18:10, 11.

4. Kodi ndani amene adzaukitsidwe?

M’dziko latsopano limene likubweralo, anthu mamiliyoni ambirimbiri amene ali m’manda adzaukitsidwa. Nawonso anthu amene ankachita zoipa chifukwa chosadziwa Yehova adzaukitsidwa.​—Werengani Luka 23:43; Machitidwe 24:15.

Anthu amene adzaukitsidwe adzapatsidwa mwayi wophunzira za Mulungu komanso woti amvere Yesu posonyeza kuti akumukhulupirira. (Chivumbulutso 20:11-13) Anthu amene azidzachita zinthu zabwino, adzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi. Komabe pa anthu oukitsidwawo padzakhalanso ena amene azidzachitabe zinthu zoipa. Anthu oterewa adzaweruzidwa malinga ndi zochita zawo zoipazo, choncho adzakhala kuti ‘anauka kuti aweruzidwe.’​—Werengani Yohane 5:28, 29.

5. Kodi mfundo yakuti akufa adzauka ikutiphunzitsa chiyani za Yehova?

Mulungu anatumiza Mwana wake kuti adzatifere ndipo imfa imeneyi ndi yomwe idzachititse kuti akufa adzaukitsidwe. Choncho kuuka kwa anthu akufa ndi umboni wakuti Yehova ndi wachikondi ndiponso wokoma mtima kwambiri.​—Werengani Yohane 3:16; Aroma 6:23.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 6 ndi 7 m’buku ili Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 16]

Mulungu anagwiritsa ntchito dothi polenga Adamu