Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi tikuphunzira chiyani za mtumwi Petulo pa mfundo yoti iye anali kunyumba ya munthu wofufuta zikopa asanauzidwe kuti apite kwa Koneliyo?

Nkhani yomwe ili m’buku la Machitidwe imanena kuti Petulo anakhala “kwa masiku angapo . . . mu Yopa kwa munthu wina wofufuta zikopa, dzina lake Simoni” yemwe ‘nyumba yake inali m’mbali mwa nyanja.’ (Machitidwe 9:43; 10:6) Ayuda ankaona kuti munthu wogwira ntchito yofufuta zikopa ndi wodetsedwa ndipo ankamunyoza kwambiri. Buku lina la Ayuda lotchedwa Talmud limanena kuti ntchito yofufuta zikopa ndi yonyozeka kwambiri kuposa ntchito yotolera ndowe. Ntchito imene Simoni ankagwirayi inkachititsa kuti nthawi zambiri azigwira nyama zakufa ndipo zimenezi zinkachititsa kuti nthawi zonse azikhala wodetsedwa. (Levitiko 5:2; 11:39) Malinga ndi zimene mabuku ambiri amanena pa nkhaniyi, Simoni ayenera kuti ankagwiritsa ntchito madzi a m’nyanja pa ntchito yakeyi. N’kuthekanso kuti malo amene ankagwirira ntchitoyi anali kunja kwa tauni chifukwa pamalo pamene munthu akugwirira ntchito yofufuta zikopa “pankanunkha kwambiri.”

Ngakhale kuti Ayuda ankaona kuti munthu wofufuta zikopa ndi wodetsedwa, zikuoneka kuti Petulo sanaone vuto kupita kukakhala masiku angapo kunyumba kwa Simoni. Zimenezi zikusonyeza kuti mwina Petulo anali atasiya khalidwe latsankho limene Ayuda ankachitira anthu amene ankawaona kuti ndi odetsedwa. Petulo ayenera kuti anachita zimenezi potsanzira Yesu yemwenso ankachita zinthu mopanda tsankho.​—Mateyu 9:11; Luka 7:36-50.

Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene anati “mwanena nokha”?

Pamene Kayafa, mkulu wa ansembe wa Ayuda anauza Yesu kuti anene mwatchutchutchu ngati iye analidi Khristu Mwana wa Mulungu, Yesu anayankha kuti: “Mwanena nokha.” (Mateyu 26:63, 64) Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani?

Sikuti Yesu ankazemba kuyankha funso la Kayafa. Mawu akuti “mwanena nokha” ayenera kuti anali okuluwika komanso odziwika bwino kwa Ayuda ndipo ankatanthauza kuti zimene zanenedwazo ndi zoona. Mwachitsanzo buku la Talmud la ku Yerusalemu, limene linalembedwa cha m’ma 300 C.E. limanena kuti Myuda wina atafunsidwa kuti afotokoze ngati rabi wina wamwaliradi, anayankha kuti, “Mwanena nokha.” Pamenepa wofunsayo anadziwa kuti yankho limeneli likutanthauza kuti rabi ameneyo wamwaliradi.

Yesu ankadziwa bwino kuti mkulu wa ansembeyo anali ndi mphamvu zomufunsa kuti anene zoona zokhazokha. Komanso Yesu akanangokhala chete osayankha, mkulu wa ansembeyu akanaganiza kuti Yesu akukana kuti si Khristu. Choncho yankho la Yesu lakuti, “Mwanena nokha” linasonyeza kuti akutsimikiza pamaso pa mkulu wa ansembeyu kuti iye analidi Khristu, Mwana wa Mulungu. M’nkhani yomweyi, imene Maliko analemba, Kayafa atafunsa Yesu kuti anene ngati analidi Mesiya, iye anayankha mopanda mantha kuti: “Inde ndinedi.”​—Maliko 14:62; onaninso Mateyu 26:25; ndi Maliko 15:2.

[Chithunzi patsamba 18]

Malo Ofufutira Zikopa Mumzinda wa Fez ku Morocco