Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu

Kodi Umaona Kuti Ana Anzako Safuna Kucheza Nawe?

Kodi Umaona Kuti Ana Anzako Safuna Kucheza Nawe?

ANTHU ena safuna kuti munthu wina akhale m’gulu lawo. Iwo amachita zimenezi mwina chifukwa chakuti munthuyo akusiyana nawo khungu, dziko limene anachokera, chilankhulo kapenanso mmene amachitira zinthu. Kodi nthawi zina nawenso umaona kuti ana anzako amakusankha?​ *

Tiye tikambirane za munthu wina amene ankaona kuti anthu ena akumusankha. Dzina la munthu ameneyu ndi Mefiboseti. Tiye tione kuti Mefiboseti anali ndani ndipo n’chiyani chinachititsa kuti aziona kuti ena akumusankha. Ngati iwenso nthawi zina umamva kuti ena akukusankha ungaphunzire zambiri pa nkhani ya Mefiboseti.

Mefiboseti anali mwana wa Yonatani, mnzake wapamtima wa Davide. Yonatani asanaphedwe kunkhondo, anapempha Davide kuti: ‘Mudzakomere mtima ana anga.’ Kenako Davide anakhala mfumu ndipo patapita nthawi anakumbukira mawu a Yonatani aja. Pa nthawiyi n’kuti Mefiboseti ali moyo. Ali wamng’ono, Mefiboseti anachita ngozi yoopsa. Ngoziyo inachititsa kuti alumale ndipo ankayenda movutikira kwambiri moyo wake wonse. Kodi tsopano wadziwa chifukwa chake Mefiboseti ankaona kuti anthu ena akumusankha?​

Davide anaona kuti ndi bwino kumukomera mtima mwana wa Yonatani ameneyu. Choncho anakonza zoti Mefiboseti azikhala pafupi ndi nyumba ya Davide ku Yerusalemu ndiponso azidya naye limodzi. Komanso Mefiboseti anapatsidwa wantchito dzina lake Ziba kuti azimusamalira. Choncho Ziba ndi ana ake komanso anyamata ake ankakhala limodzi ndi Mefiboseti. Apa n’zoonekeratu kuti Davide anamulemekeza kwambiri mwana wa Yonatani ameneyu. Kodi ukudziwa zimene kenako zinachitika?​

Davide anayamba kukumana ndi mavuto. Mwana wake wina dzina lake Abisalomu anamuukira ndipo anafuna kumulanda ufumu. Chifukwa cha zimenezi, Davide anathawa poopa kuphedwa. Anthu ambiri anapita limodzi ndi Davide ndipo Mefiboseti nayenso anafuna kuti apite nawo. Anthu amenewa, omwe anali mabwenzi a Davide, ankadziwa kuti Davide ndiye woyenera kukhala mfumu. Koma Mefiboseti sanathe kupita nawo chifukwa sakanatha kuyenda poti anali wolumala.

Ndiyeno Ziba anauza Davide kuti Mefiboseti sanapite nawo chifukwa ankafuna kulanda ufumu. Davide anakhulupirira bodza limeneli. Choncho anapatsa Ziba zinthu zonse zimene zinali za Mefiboseti. Pasanapite nthawi, Davide anapambana nkhondo yolimbana ndi Abisalomu ndipo anabwerera ku Yerusalemu. Tsopano Mefiboseti anafotokozera Davide zoona za nkhani ija. Choncho, Davide analamula kuti Mefiboseti ndi Ziba agawane zinthu zija. Kodi ukuganiza kuti Mefiboseti anatani pamenepa?​

Iye sanadandaule kuti Davide sanagamule bwino. Mefiboseti ankadziwa kuti si bwino kuti pakhale mikangano chifukwa zimenezi zingachititse kuti mfumuyi izivutika kugwira bwino ntchito yake. Choncho Mefiboseti ananena kuti Ziba atenge zinthu zonsezo. Kwa iye chimene chinali chofunika kwambiri chinali chakuti Davide mtumiki wa Yehova wabwereranso ku Yerusalemu kudzapitiriza ntchito yake monga mfumu.

Choncho ungaone kuti Mefiboseti anavutika kwambiri. Nthawi zambiri ankaona kuti anthu akumusankha. Koma Yehova ankamukonda kwambiri ndipo anamusamalira. Kodi pamenepa tikuphunzirapo chiyani?​— Tikuphunzira kuti, ngakhale ifeyo titakhala kuti tikuchita zabwino, anthu ena akhoza kutinenera zinthu zabodza. Chitsanzo cha zimenezi, ndi zimene zinachitikira Yesu. Iye anati: “Ngati dziko likudana nanu, mukudziwa kuti linadana ndi ine lisanadane ndi inu.” Anthu ena ankadana ndi Yesu mpaka anafika pomupha. Komabe, tingakhale ndi chikhulupiriro kuti ngati tikuchita zabwino, Yehova Mulungu ndiponso Mwana wake Yesu azitikonda.

^ ndime 3 Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana, mukapeza mzera muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.