Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinkafunitsitsa Kudzagwira Ntchito Yoyenda M’madera Osiyanasiyana

Ndinkafunitsitsa Kudzagwira Ntchito Yoyenda M’madera Osiyanasiyana

Ndinkafunitsitsa Kudzagwira Ntchito Yoyenda M’madera Osiyanasiyana

Yosimbidwa ndi Zoya Dimitrova

Kuyambira ndili mwana ndinkafunitsitsa kudzagwira ntchito yomayenda m’madera osiyanasiyana n’kumachita masewera ndiponso zinthu zina zosangalatsa anthu. Moti pomwe ndinkakwanitsa zaka 15 n’kuti nditayamba kale kugwira ntchitoyi. Koma pa September 4, 1970 ndinachita ngozi moti zinthu zinasinthiratu pa moyo wanga. Pa tsikuli tinkachita masewera olumpha m’mwamba n’kumachita zipidigoliro pofuna kusangalatsa anthu. Kenako ndinagwa pansi mwamphamvu ndipo ndinavulala kwambiri.

NDINABADWA pa December 16, 1952 ndipo ine ndi mchemwali wanga tinkakhala ndi makolo athu ku Sofia, m’dziko la Bulgaria. Pa nthawiyi dziko la Bulgaria linali lachikomyunizimu ndipo m’dzikoli munali ufulu wachipembedzo koma anthu sankalimbikitsidwa kukhala ndi chipembedzo ndipo ambiri sankakhulupirira Mulungu. Komabe panali ena amene ankakhulupirira Mulungu koma ambiri ankachita zimenezo mobisa. Ngakhale kuti makolo anga ankati ndi a tchalitchi cha Orthodox, sankandiphunzitsa za chipembedzo chilichonse ndipo ineyo sindinkaganiza n’komwe zoti kuli Mulungu.

Ndili mwana ndinkakonda kwambiri masewera osiyanasiyana olimbitsa thupi makamaka olumpha m’mwamba n’kumapanga zipidigoliro. Ndili ndi zaka 13, kusukulu kwathu kunabwera munthu wina yemwe ankafuna mtsikana woti amuphunzitse kuchita masewera olumpha pofuna kusangalatsa anthu. Mphunzitsi amene ankatiphunzitsa masewerawa anauza munthu uja kuti atenge ineyo. Ndinkasangalala kwambiri kukwera galimoto yodula zedi ya manijala popita kokafunsidwa mafunso ndi anthu ophunzitsa ntchitoyi. Ndinasangalala atandiuza kuti ndachita bwino. Zitatero ndinayamba kuphunzira ntchitoyi kwa zaka ziwiri ndipo inali ndi malamulo okhwima kwambiri. Kenako ndili ndi zaka 15 ndinamaliza sukuluyi ndipo ndinayamba kukhala moyo umene ndinkafunitsitsa uja, moyo woyendayenda n’kumachita masewera osangalatsa anthu. Poyamba tinayenda m’dziko lonse la Bulgaria. Kenako tinayamba kupita m’mayiko omwe kale ankalamulidwa ndi dziko la Soviet Union mpaka tinakafikanso ku Algeria, Hungary, komanso dziko limene poyamba linali Yugoslavia.

Kwa zaka zitatu zotsatira, ndinkaona kuti zinthu zikundiyendera bwino chifukwa ndinakwanitsa kuchita zimene ndinkalakalaka pa moyo wanga. Koma tsiku lina pomwe tinkachita masewerawa mu mzinda wa Titov Veles m’dziko la Macedonia ndinachita ngozi yomwe ndaifotokoza poyamba ija. Pa nthawiyi ndinalumpha m’mwamba kwambiri n’kumachita zipidigoliro. Mnzanga amene ndinkapanga naye masewerawa anali atapachika miyendo yake pachingwe, n’kuzondotsa mutu wake pansi ndipo ankandiponya m’mwamba n’kumandiwakha pondigwira manja kuti ndisagwe. Koma kenako zimene zinachitika ndi zoti ndili m’maleremo ndinaphonya kugwira manja ake ndipo mwatsoka chingwe choteteza kuti munthu asagwe chinaduka. Choncho, ndinagwa mwamphamvu kuchokera m’mwamba motalika mamita 6. Nthawi yomweyo anathamangira nane kuchipatala kumene anapeza kuti ndathyoka mkono, nthiti komanso msana. Kwa masiku angapo ndinali ndikudwala mwakayakaya ndipo sindinkakumbukira zimene zinachitika. Nditayamba kuzindikira, ndinadziwa kuti ziwalo zanga kuyambira m’chiuno mpakana m’miyendo zinali zitafa. Komabe popeza ndinali ndidakali mwana, ndinkakhulupirira kuti akandipatsa chithandizo choyenera kapena kundichita opaleshoni, ndichira n’kudzayenda bwinobwino mwina n’kuyambiranso kuchita masewera olumpha aja.

Kwa zaka ziwiri ndi theka ndinakhala ndikuyenda m’zipatala zosiyanasiyana ndipo ndinkakhulupirirabe kuti tsiku lina ndidzakhala bwino. Koma m’kupita kwa nthawi ndinavomereza kuti sindidzathanso kuchita masewera amene ndinkawakonda aja. M’malo mokhala ndi moyo umene ndinkaulakalaka, woyenda m’madera osiyanasiyana n’kumachita masewera olumpha, ndinayamba kumangokhala panjinga ya olumala.

Ndinayamba Moyo Watsopano

Poyamba ndinkaona kuti sinditha kumangokhala panjinga ya anthu olumala chifukwa ndinali nditazolowera moyo womayenda m’madera osiyanasiyana. Ndinadziwa kuti sindingathenso kudzachita masewera olumpha aja ndipo izi zinapangitsa kuti ndiyambe kuvutika maganizo. Kenako mu 1977 mnyamata wina dzina lake Stoyan anabwera kunyumba kwathu. Nditadziwa kuti anali mchimwene wa mnzanga wina amene ndinkapanga naye masewera olumpha aja, ndinamulowetsa m’nyumba. Nditacheza naye kwa kanthawi, anandifunsa ngati ndinali ndi chiyembekezo chilichonse choti ndidzayendanso. Chifukwa chokhumudwa kwambiri ndi mmene zinthu zinalili pa moyo wanga, ndinamuyankha kuti ndinalibenso chiyembekezo choti ndingadzayendenso bwinobwino. Atandiuza kuti ndi Mulungu yekha amene angandithandize, ndinayankha mopsa mtima kuti, “Ngati kuli Mulungu n’chifukwa chiyani walola kuti ndikumane ndi mavuto amenewa?”

Stoyan anali atabatizidwa kumene ku United States n’kukhala wa Mboni za Yehova pamene ankagwira ntchito yofanana ndi imene ndinkagwira ija. Choncho iye anandifotokozera mokoma mtima kwambiri malonjezo osiyanasiyana onena za m’tsogolo opezeka m’Baibulo. Ndinasangalala kwambiri kumva kuti posachedwapa dziko lapansi lidzakhala paradaiso. Komanso lonjezo lakuti: “Imfa sidzakhalaponso. sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka,” linandikhudza mtima kwambiri. (Chivumbulutso 21:4) Ndinkafunitsitsa nditayambiranso kuyenda bwinobwino choncho nthawi yomweyo, ndinavomera kuyamba kuphunzira Baibulo. Chimenechi chinali chiyambi cha kusintha kwa zinthu pa moyo wanga. Tsopano ndinayamba kuona kuti ndili ndi chiyembekezo.

Mlungu uliwonse ndinkayembekezera mwachidwi kuti ndiphunzire Baibulo. Poyamba ndinkaphunzira ndi Stoyan ndipo kenako ndinayamba kuphunzira ndi mayi wina wokoma mtima kwambiri dzina lake Totka. Mayiyu anandithandiza kudziwa zambiri za m’Baibulo ndipo patapita nthawi ndinadzipereka kwa Yehova Mulungu. Nthawi imeneyi panalibe munthu woyenerera kuti andibatize. Choncho ndinadikira m’bale wina kuti abwere kuchoka ku Macedonia. Pa September 11, 1978, ndinabatizidwa m’bafa ya m’nyumba yathu ndipo pa nthawiyi n’kuti patatha chaka chimodzi chiyambireni kuphunzira Baibulo. Nditabatizidwa, ndinayamba kukhala wosangalala komanso kuona kuti moyo wanga ndi wofunika.

Anthu akabwera kunyumba kwathu ndinkawafotokozera zimene ndikuphunzira. Ndinkachita zimenezi chifukwa ndinkaona kuti sindikanatha kumangokhala osauza munthu zimene ndikuphunzira. Komabe anthu sankamvetsera kwenikweni chifukwa ankangoona ngati mutu wanga wasokonekera chifukwa cha ngozi ija.

Ndinachita Tchimo Lalikulu

Pa nthawiyi, m’dziko la Bulgaria a Mboni za Yehova tinali ochepa kwambiri chifukwa chipembedzo chathu chinali choletsedwa. Sindinkatha kupita ku misonkhano iliyonse ndipo nthawi zambiri ndinkacheza ndi anthu omwe si Mboni chifukwa a Mboni za Yehova anali ochepa. Chifukwa cha zimenezi komanso chifukwa chakuti sindinkadziwa kuopsa kocheza ndi anthu amene satsatira mfundo za m’Baibulo, ndinachita tchimo lalikulu.

Chikumbumtima changa chinayamba kundivutitsa ndipo mumtima mwanga ndinkamva ululu chifukwa chodziwa kuti ubwenzi wanga ndi Yehova Mulungu wasokonezeka. Chifukwa chovutika maganizo komanso kudziimba mlandu, ndinapemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima kuti andikhululukire. Kenako akulu achikhristu mu mpingo anandithandiza mwachikondi ndipo ndinakhalanso pa ubwenzi ndi Yehova n’kuyambanso kumutumikira mosangalala. Panopa ndimaona kuti kutumikira Yehova limodzi ndi gulu lake loyera, ndili ndi chikumbumtima choyera, ndi chinthu cha mtengo wapatali.

Ndikusangalala Kwambiri Ngakhale Kuti Ndine Wolumala

Ngozi yomwe ndinachita zaka 40 zapitazo inasokoneza cholinga changa choyenda m’madera osiyanasiyana n’kumachita masewera olumpha. Panopa ndimangokhala panjinga ya anthu olumala. Komabe ndikaganizira zimene zandichitikira pa moyo wanga, sindinong’oneza bondo n’kumaona ngati palibe chaphindu chilichonse chimene ndachita. Kuphunzira Baibulo kwandithandiza kudziwa kuti zinthu zimene ndinkaziona ngati zikhoza kundibweretsera chimwemwe pamoyo wanga, ndi zopanda phindu kwenikweni. Ndaonapo anthu ena amene ndinkapanga nawo masewera aja akukhala moyo wosasangalala. Koma ineyo ndapeza chinthu chamtengo wapatali kwambiri kuposa zonse, chomwe ndi kukhala pa ubwenzi ndi Mlengi wathu Yehova Mulungu. Zimenezi zandipangitsa kukhala wosangalala kwambiri kuposa mmene zikanakhalira ndikanapitiriza kuchita masewera aja.

Ndasangalalanso kuona anthu ambiri akuphunzira Baibulo ndiponso akudzipereka kwa Yehova Mulungu wathu wachikondi. Pamene ndinkayamba kuphunzira Baibulo mu 1977, n’kuti m’dziko la Bulgaria muli a Mboni za Yehova ochepa kwambiri. Komanso mu 1991, pamene boma linachotsa lamulo loletsa Mboni za Yehova ku Bulgaria, m’dzikoli munali a Mboni za Yehova osapitirira 100. Koma panopa chosangalatsa n’chakuti chiwerengero cha Mboni za Yehova chawonjezeka mpaka kufika pafupifupi 1,800.

Komabe pali ntchito yambiri yoti tichite mu dziko la Bulgaria chifukwa pali anthu ambiri amene akufuna kudziwa choonadi cha m’Mawu a Mulungu. Umboni wa zimenezi ndi chiwerengero cha anthu okwana 3,914 amene anapezeka pa mwambo wokumbukira imfa ya Khristu m’chaka cha 2010. Ndimasangalala kwambiri ndikamaganizira zimene Yehova wachita kuti chiwerengero cha Mboni zake chiwonjezeke m’dziko la Bulgaria. Ndaona ndi maso anga “wochepa” akusanduka “mtundu wamphamvu” monga mmene lemba la Yesaya 60:22 linaloserera.

Chinanso chomwe chimandisangalatsa kwambiri pa moyo wanga ndi kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika m’Chibugariya. Baibuloli linatulutsidwa mu August 2009 pamsonkhano wachigawo wa mutu wakuti “Khalani Maso!” womwe unachitikira ku Sofia. Baibuloli litatuluka m’chinenero chathu tinangoona ngati kutulo. Ndikukhulupirira kuti Baibuloli litithandiza zedi kuphunzitsa anthu ambiri ku Bulgaria kuti adziwe choonadi cha m’Baibulo.

Ngakhale kuti kulumala kwanga kwandichititsa kuti ndisamathe kuchita zimene ndimalakalaka kuchita polalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndimasangalalabe kugawana choonadi cha m’Baibulo ndi anthu omwe ndimakhala nawo pafupi komanso anthu amene amabwera kunyumba kwathu. Tsiku lina nditakhala pakhonde ndinaona aneba anga akudutsa mumsewu ndipo ndinawaitana. Anabwera ndipo ndinakambirana nawo mfundo zosiyanasiyana zolimbikitsa zochokera m’Baibulo. Nditawapempha ngati angakonde kuti ndiziwaphunzitsa Baibulo anavomera ndipo ndinasangalala chifukwa patapita nthawi anabatizidwa n’kukhala wa Mboni mnzanga. Ndakhala ndi mwayi wothandiza anthu anayi kuphunzira Baibulo mpaka anadzipereka kwa Yehova.

Chomwe chimandithandiza kwambiri kukhala wosangalala, ndi kusonkhana ndi abale komanso alongo anga opitirira 100, omwe ali ngati abale anga enieni. Boma la Bulgaria lilibe ndondomeko yothandiza anthu okalamba ndi olumala pa nkhani ya mayendedwe, choncho nthawi zina ndimavutika kupita kumisonkhano. Koma ndimayamikira kwambiri m’bale wina wachinyamata yemwe amandithandiza. Nthawi zonse iye amabwera kunyumba kudzanditenga kupita nane ku Nyumba ya Ufumu, n’kudzandisiyanso misonkhano ikatha. Ndimathokoza kwambiri Yehova kuti ndili m’banja lauzimu lachikondi limeneli.

Ndikaganiza zimene ndakumana nazo pa moyo wanga, ndikuona kuti zinthu sizinayende mmene ndinkafunira ndili wamng’ono. Koma kutumikira Yehova kwandibweretsera chimwemwe chosaneneka komanso chiyembekezo chabwino cha m’tsogolo. Ndikuyembekezera mwachidwi dziko lapansi la paradaiso pamene, “munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo.” (Yesaya 35:6) Ndikukhulupirira ndi mtima wanga wonse kuti pa nthawi ina sindidzakhalanso wolumala ndipo ndidzalumpha kuchoka panjingayi ndili wamphamvu komanso wathanzi labwino.

[Mawu Otsindika patsamba 30]

“Kusonkhana ndi abale anga achikhristu kumandithandiza kukhala wosangalala komanso kumandilimbikitsa kwambiri”

[Mawu Otsindika patsamba 31]

“Chimene chinandisangalatsa kwambiri pa moyo wanga ndi kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika m’Chibugariya

[Chithunzi patsamba 29]

Ndinayamba kuchita masewera olumpha ndili ndi zaka 15