Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yandikirani Mulungu

Kodi Yehova Amasangalala Kapena Kukhumudwa Ndi Zochita Zathu?

Kodi Yehova Amasangalala Kapena Kukhumudwa Ndi Zochita Zathu?

NGATI mukuyankha funso limeneli kuti inde, funso lina lingakhale lakuti: Kodi khalidwe lathu limamukhudza bwanji Yehova? M’mawu ena tingafunse kuti, kodi zochita zathu zingathe kusangalatsa Mulungu kapena kumukhumudwitsa? Akatswiri ena akale ofufuza nzeru za anthu ankanena kuti Mulungu sangasangalale kapena kukhumudwa ndi zochita zathu. Iwo ankanena kuti palibe munthu amene angasangalatse kapena kukhumudwitsa Mulungu, ndipo Mulungu sakhudzidwa ndi zochita zathu. Komabe Baibulo limatiuza zosiyana ndi zimenezi, chifukwa limanena kuti Yehova ndi wachifundo komanso amakhudzidwa mtima ndi zimene timachita. Taonani mawu amene ali pa Salimo 78:40, 41.

Salimo 78, limafotokoza mmene Mulungu ankachitira zinthu ndi mtundu wakale wa Isiraeli. Yehova atatulutsa mtunduwu mu ukapolo ku Iguputo, anachita pangano ndi Aisiraeli kuti akhale nawo pa ubwenzi wapadera. Iye analonjeza Aisiraeli kuti ngati adzakhalabe okhulupirika kwa iye, adzakhala ‘chuma chake chapadera’ ndipo adzawagwiritsa ntchito pokwaniritsa cholinga chake. Anthuwo anagwirizana ndi zimenezi, ndipo anachita pangano la Chilamulo. Koma kodi iwo anachitadi zinthu zogwirizana ndi zimene analonjeza?​—Ekisodo 19:3-8.

Palibenso chinthu china chamtengo wapatali chimene tingamupatse Yehova, koma kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene amakondweretsa mtima wake

Wamasalimo ananena kuti: “Iwo analitu kumupandukira kawirikawiri m’chipululu.” (Vesi 40) Vesi lotsatira limanena kuti: “Mobwerezabwereza, anali kumuyesa Mulungu.” (Vesi 41) Kodi mwaona kuti salimo limeneli likusonyeza kuti zimenezi zinkachitika mobwerezabwereza? Aisiraeli anayamba kusalemekeza Mulungu komanso kumupandukira ali m’chipululu, pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Mulungu anawapulumutsa ku Iguputo. Iwo anayamba kung’ung’udza komanso kukayikira ngati Mulungu angathe kuwasamalira komanso ngati ankafunadi kuwasamalira. (Numeri 14:1-4) Buku lina lothandiza anthu omasulira Baibulo limanena kuti mawu akuti ‘anali kumupandukira’ angamasuliridwenso kuti ‘anaumitsa mitima yawo kuti asamvere Mulungu’ kapena ‘anauza Mulungu kuti, “sitikufuna kuti mukhale Mulungu wathu.”’ Komabe, popeza Yehova ndi Mulungu wachifundo, iye ankakhululukira anthu akewa akalapa. Koma zikatero iwo ankayambiranso kuchita zinthu zoipa ndipo ankamupandukiranso. Akalapa, Yehova ankawakhululukiranso ndipo izi zinkachitika mobwerezabwereza.​—Salimo 78:10-19, 38.

Kodi Yehova ankamva bwanji Aisiraeli osamverawa akamupandukira? Vesi 40 limanena kuti: “Anali kumukhumudwitsa.” Baibulo lina linamasulira mawu amenewa kuti, “ankachititsa kuti Mulungu amve chisoni.” Buku lina lofotokoza nkhani za m’Baibulo limati: “Mawu amenewa akutanthauza kuti zimene Ayuda ankachita zinkamupweteketsa mtima Yehova ngati mmene makolo amamvera, mwana wawo akamawachitira mwano komanso akawapandukira.” Mofanana ndi mmene mwana wosamvera amapweteketsera kwambiri mtima makolo ake, Aisiraeli “anali kumvetsa chisoni Woyera wa Isiraeli.”​—Vesi 41.

Kodi salimo limeneli likutiphunzitsa chiyani? Likutiphunzitsa kuti Yehova amakonda kwambiri atumiki ake ndipo akamulakwira amawakhululukira. Koma salimo limeneli lilinso ndi mfundo yofunika kuiganizira kwambiri. Mfundo imeneyi ndi yakuti, zochita zathu zingathe kukhumudwitsa kapena kusangalatsa Yehova. Kodi kudziwa zimenezi kuyenera kukukhudzani bwanji? Kodi sizikukupangitsani kuganiza kuti muyenera kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu?

M’malo mopitirizabe kuchita zinthu zoipa n’kumapweteketsa mtima Yehova, muyenera kumumvera komanso kusangalatsa mtima wake. Ndipotu zimenezo n’zimene Yehova akupempha anthu amene amamulambira kuti achite. Iye akuti: “Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga.” (Miyambo 27:11) Palibenso chinthu china chamtengo wapatali chimene tingamupatse Yehova, koma kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene amakondweretsa mtima wake.

Mavesi amene mungawerenge mu July: