Amakumbukira Kuti “Ndife Fumbi”
Yandikirani Mulungu
Amakumbukira Kuti “Ndife Fumbi”
“SINDINAKHULUPIRIRE kuti Yehova angandikhululukiredi machimo anga, moti ndinkaganiza kuti ndidzapitiriza kudziimba mlandu kwa moyo wanga wonse.” Mawu amenewa analemba ndi mayi wina wachikhristu yemwe anachitapo machimo enaake m’mbuyomu. Kunena zoona, munthu akamavutika ndi chikumbumtima amakhala ngati wasenza chimtolo cholemetsa. Komabe m’Baibulo muli mawu olimbikitsa amene amathandiza anthu olapa omwe akumva ululu mumtima mwawo chifukwa cha tchimo limene anapanga. Taganizirani mawu a Davide amene akupezeka pa Salimo 103:8-14.
Davide ankadziwa kuti “Yehova ndi wachifundo” ndipo “sadzakhalira kutiimba mlandu.” (Vesi 8-10) Mulungu akaona kuti pali zifukwa zomveka zoti amuchitire chifundo munthu, amachita zimenezo mosaumira komanso ndi mtima wonse. Davide, yemwe analemba ndakatulo zabwino kwambiri, anagwiritsa ntchito mafanizo atatu pofuna kusonyeza chifundo chosatha chimene Mulungu ali nacho pa anthufe.
“Monga mmene kumwamba kulili pamwamba kwambiri kuposa dziko lapansi, kukoma mtima kwake kosatha nakonso ndi kwapamwamba kwa onse omuopa.” (Vesi 11) Tikayang’ana kumwamba komwe kuli nyenyezi usiku, timaona kuti n’kotalikirana kwambiri ndi dziko lapansili ngakhale kuti sitingadziwe kuti n’kotalikirana bwanji. Choncho Davide anatsindika mfundo yakuti Yehova ndi wachifundo kwambiri ndipo khalidwe limeneli ndi njira ina imene amasonyezera chikondi chake chosatha. Yehova amasonyeza chifundo chimenechi kwa anthu amene ‘amamuopa.’ Katswiri wina wamaphunziro ananena kuti amenewa ndi anthu “odzichepetsa, amene amalemekeza kwambiri ulamuliro wa Mulungu.”
“Monga mmene kum’mawa kwatalikirana ndi kumadzulo, momwemonso, watiikira kutali zolakwa zathu.” (Vesi 12) Apa mfundo ya Davide ndi yakuti Mulungu akatikhululukira machimo, amawaika kutali kwambiri ndi ife.
“Monga mmene bambo amasonyezera chifundo kwa ana ake, Yehova wasonyezanso chifundo kwa onse omuopa.” (Vesi 13) Popeza Davide anali ndi ana, iye ankadziwa mmene bambo wachikondi amamvera mumtima mwake. Bambo wachikondi amasonyeza ana ake chifundo, makamaka pamene anawo akumva ululu chifukwa cha zinthu zina. Davide akutitsimikizira kuti Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachikondi, amasonyeza chifundo kwa ana ake apadziko lapansi, makamaka ngati mitima yolapa ya anawo ili ‘yosweka ndi yophwanyika’ chifukwa cha machimo awo.—Salimo 51:17.
Pambuyo pofotokoza mafanizo atatuwa, Davide analongosola chimene chimachititsa Yehova kuti achitire chifundo anthu opanda ungwiro. Iye anati: “Iye akudziwa bwino mmene anatiumbira, amakumbukira kuti ndife fumbi.” (Vesi 14) Yehova amadziwa kuti tinapangidwa ndi fumbi ndipo amadziwanso zimene sitingathe kuchita. Poganizira kuti ndife anthu ochimwa, Yehova ndi “wokonzeka kukhululuka,” ngati titasonyeza kulapa kochokera pansi pa mtima.—Salimo 86:5.
Kodi simukukhudzidwa mtima ndi mawu a Davidewa osonyeza kuti Yehova ndi wachifundo? Mayi amene tamugwira mawu koyambirira kwa nkhani ino uja anaphunzira zimene Baibulo limanena pa nkhani yoti Mulungu ndi wokonzeka kukhululuka, ndipo anati: “Ndayamba kuona kuti n’zothekadi kuyandikira Yehova, moti ndikumva kupepukidwa kwambiri ngati kuti ndatula chimtolo cholemetsa.” * Tikukupemphani kuti muphunzire zambiri zokhudza chifundo cha Mulungu komanso zimene mungachite kuti Mulungu azikuchitirani chifundo. Mwina inunso mungayambe kuona kuti mwatula chimtolo cholemetsa chimene munasenza.
Mavesi amene mungawerenge mu August:
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 Werengani mutu 26 wakuti “Mulungu ‘Wokhululukira’” m’buku lakuti Yandikirani kwa Yehova lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Mawu Otsindika patsamba 13]
“Ndayamba kuona kuti n’zothekadi kuyandikira Yehova, moti ndikumva kupepukidwa kwambiri ngati kuti ndatula chimtolo cholemetsa”