Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anamunamizira Mlandu

Anamunamizira Mlandu

Zoti Achinyamata Achite

Anamunamizira Mlandu

YOSEFE​—GAWO 2

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a m’nkhaniyi akumvera mumtima mwawo.

Amene akutchulidwa kwambiri m’nkhaniyi: Yosefe, Potifara komanso mkazi wa Potifara

Chidule cha nkhaniyi: Yosefe anaikidwa m’ndende ngakhale kuti anali wosalakwa koma Yehova anali naye.

1 ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI GENESIS 39:7, 10-23.

Kodi mukuganiza kuti mkazi wa Potifara ankamva bwanji mumtima mwake pamene ankanamizira Yosefe, nanga mawu ake ankamveka bwanji?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti ndende imene anamuikamo Yosefe inkaoneka bwanji? Fotokozani.

․․․․․

Yosefe atangoikidwa kumene m’ndende, kodi anakumana ndi mavuto ati amene anafunika kuwapirira? (Zokuthandizani: Onani Salimo 105:17, 18.)

․․․․․

2 FUFUZANI MOZAMA.

Yosefe akanakhala ndi chikhulupiriro chofooka, kodi ndi maganizo olakwika ati amene akanakhala nawo pa nthawi imene anali m’ndende? (Zokuthandizani: Onani Yobu 30:20, 21.)

․․․․․

Kodi tikudziwa bwanji kuti Yosefe sanaimbe mlandu Mulungu chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo? (Zokuthandizani: Onani Genesis 40:8; 41:15, 16.)

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti Yosefe anali ndi makhalidwe ati amene anamuthandiza kupirira pamene anaikidwa m’ndende ngakhale kuti sanalakwe? (Zokuthandizani: Werengani ndipo ganizirani mozama malemba awa: Mika 7:7; Luka 14:11; Yakobo 1:4.)

․․․․․

Kodi ndi zinthu ziti zimene Yosefe anaphunzira pamene anali m’ndende? Kodi zimene anaphunzirazo zinamuthandiza bwanji pa moyo wake m’tsogolo? (Zokuthandizani: Onani Genesis 39:21-23; 41:38-43.)

․․․․․

3 GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA ZOKHUDZA . . .

Madalitso amene anthu opirira amapeza.

․․․․․

Zimene mungaphunzire pa nthawi imene mukukumana ndi mavuto.

․․․․․

Mmene Yehova amatithandizira tikakhala pa mavuto.

․․․․․

MMENE MUNGAGWIRITSIRE NTCHITO MFUNDOZI.

Kodi zinakuchitikiranipo nthawi ina kuti munavutika kwambiri ndipo munkaona kuti muli nokhanokha? Ngakhale kuti munali pa mavuto, kodi Yehova anakuthandizani bwanji pa nthawiyo? (Zokuthandizani: Werengani ndipo ganizirani mozama 1 Akorinto 10:13.)

․․․․․

4 M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ITI IMENE YAKUKHUDZANI MTIMA KWAMBIRI, NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․

Ngati Mulibe Baibulo, Uzani a Mboni za Yehova, Kapena Kawerengeni Baibulo pa Adiresi ya pa Intaneti iyi: www.pr418.com.