Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Inu Yehova, . . . Mukundidziwa”

“Inu Yehova, . . . Mukundidziwa”

Yandikirani Mulungu

“Inu Yehova, . . . Mukundidziwa”

“KUDZIWA kuti palibe munthu aliyense amene amakukonda kapena amene amamvetsa mavuto amene ukukumana nawo ndi chinthu chopweteka kwambiri.” * Kodi inunso mumamva choncho? Kodi nthawi zina mumaona kuti palibe aliyense amene amakukondani kapena kumvetsa mmene mukumvera pa mavuto amene mukukumana nawo? Ngati ndi choncho, mfundo iyi ingakulimbikitseni: Yehova amakonda kwambiri atumiki ake moti amadziwa zonse zimene zimawachitikira pa moyo wawo. Mawu a Davide opezeka mu Salimo 139 amatitsimikizira mfundo imeneyi.

Davide anali ndi chikhulupiriro chonse kuti Mulungu amamukonda. Iye anati: “Inu Yehova, mwandifufuza ndipo mukundidziwa.” (Vesi 1) Pamenepatu Davide anagwiritsa ntchito mawu okuluwika. Mawu achiheberi amene palembali anawamasulira kuti ‘kufufuza’ angagwiritsidwenso ntchito ponena za kukumba miyala yamtengo wapatali (Yobu 28:3), kuzonda dziko (Oweruza 18:2), kapena kufufuza mfundo zokhudza mlandu winawake (Deuteronomo 13:14). Yehova amatidziwa bwino anthufe moti tingati amafufuza ndi kudziwa chilichonse chimene tikuchita pa moyo wathu. Pamenepa Davide akutiphunzitsa mfundo yakuti Mulungu amafufuza mtumiki wake aliyense payekha ndipo amadziwa zimene zikumuchitikira.

Davide anawonjezera mawu osonyeza kuti Mulungu amatifufuza kwambiri. Iye anati: “Inu mumadziwa ndikakhala pansi kapena ndikaimirira. Mumadziwa maganizo anga muli kutali.” (Vesi 2) Mwanjira ina, tingati Yehova amakhala “kutali,” kumwamba. Koma ngakhale zili choncho, iye amadziwa tikakhala pansi, mwina pambuyo pogwira ntchito tsiku lonse komanso pamene tadzuka m’mawa kuti tiyambe ntchito zathu zatsikulo. Iye amadziwanso maganizo athu, zolakalaka zathu komanso zolinga zathu. Koma kodi Davide anachita mantha chifukwa chofufuzidwa mwanjira imeneyi? Ayi, m’malomwake iye anachita kupempha kuti Mulungu amufufuze. (Vesi 23, 24) Kodi n’chifukwa chiyani Davide anapempha Mulungu kuti amufufuze?

Davide ankadziwa kuti Yehova amafufuza atumiki Ake ndi zolinga zabwino. Iye anatchula za zolinga zimenezi pamene analemba kuti: “Mumandidziwa bwino pamene ndikuyenda komanso pamene ndikugona, ndipo njira zanga zonse mukuzidziwa bwino.” (Vesi 3) Tsiku lililonse Yehova amadziwa ‘njira zathu zonse,’ kaya zolakwa zathu kapena zinthu zimene timachita bwino. Kodi iye amaganizira kwambiri zolakwa zathu kapena amaganizira kwambiri zimene timachita bwino? Mawu achiheberi amene anamasuliridwa kuti ‘kudziwa bwino,’ amene ali kumayambiriro kwa vesili, angatanthauzenso “kupeta” kapena “kuulutsa,” ngati mmene mlimi amachitira pochotsa mankhusu opanda ntchito kuti atsale ndi mbewu zabwino zokhazokha. Ndipo mawu akuti ‘kuzidziwa bwino’ amene ali kumapeto kwa lembali, achokera ku mawu achiheberi amene angatanthauzenso “kukumbukira” chinthu chifukwa choona kuti ndi cha mtengo wapatali. Choncho Yehova akamafufuza zimene atumiki ake amanena kapena kuchita tsiku lililonse, kwenikweni amakumbukira zinthu zabwino zimene anthuwo akuchita. Amachita zimenezi chifukwa amasangalala ndi khama lawo lofuna kuchita zinthu zimene iyeyo amasangalala nazo.

Salimo 139 limatiphunzitsa kuti Yehova amakonda kwambiri atumiki ake. Iye amawafufuza ndiponso amawayang’anira pa zonse zimene akuchita pa moyo wawo. Choncho Yehova amadziwa mavuto amene atumiki ake akukumana nawo komanso amamvetsa mmene iwo akumvera mu mtima mwawo chifukwa cha mavutowo. Kodi mukulakalaka kutumikira Mulungu wachikondi ameneyu? Ngati ndi choncho, musakayikire ngakhale pang’ono kuti Yehova ‘sadzaiwala ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.’​—Aheberi 6:10.

Mavesi amene mungawerenge mu September:

Masalimo 119 mpaka 150

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Mawu amenewa ananena ndi wolemba mabuku wina dzina lake Arthur H. Stainback.