Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Pali Winawake Amene Amachititsa Zoipa Zonsezi?

Kodi Pali Winawake Amene Amachititsa Zoipa Zonsezi?

Kodi Pali Winawake Amene Amachititsa Zoipa Zonsezi?

“NDINAKUMANA ndi mdyerekezi.” Mawu amenewa ananena ndi mkulu wa asilikali a bungwe la United Nations ku Rwanda. Iye ananena zimenezi podandaula chifukwa choti bungwelo linalephera kuthetsa nkhondo imene inachitika m’dzikolo m’chaka cha 1994. Pofotokoza za kuphana mwachisawawa kumene kunkachitika pa nthawiyo, munthu wina anati: “Ngati pali wina amene akukayikirabe zoti kunja kuno kuli Satana, abwere ndikamuonetse mitembo yambirimbiri imene yaikidwa m’manda amodzi ku Rwanda.” Kodi n’zoonadi kuti Mdyerekezi ndiye amachititsa kuti zinthu zoipa kwambiri ngati zimenezi zizichitika?

Anthu ambiri sakhulupirira kuti pali cholengedwa chinachake chauzimu choipa kwambiri chimene chimachititsa kuti anthu azichita zinthu zoipa komanso zachiwawa. Ambiri amaganiza kuti zimenezi zimangochitika chifukwa cha chibadwa cha munthu chofuna kuchita zoipa. Palinso anthu ena amene amaganiza kuti pali gulu lina la anthu olemera komanso amphamvu omwe pofuna kuti azilamulira dziko lonse lapansi, mwakabisira amachititsa anthu padzikoli kuti azichita zinthu zoipa. Ndiyeno palinso anthu ena amene amaimba mlandu maboma ndiponso atsogoleri andale kuti ndi amene amachititsa zinthu zonse zopanda chilungamo komanso mavuto amene timakumana nawowa.

Kodi inuyo mumakhulupirira chiyani pa nkhani imeneyi? N’chifukwa chiyani nkhanza, kuphana, ndiponso zoipa zina zafala kwambiri padziko lonse ngakhale kuti anthu akuyesetsa kuti zinthu zoterezi zithe? Nanga n’chifukwa chiyani anthu padzikoli akunyalanyaza malangizo n’kumapitirizabe kuchita zinthu zimene zimabweretsa mavuto? Kodi pali winawake amene akuchititsa zonsezi? Kodi amene akulamulira anthu padzikoli ndi ndani kwenikweni? Yankho lake likhoza kukudabwitsani kwambiri.