Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

5 Mulungu Amavomereza Zipembedzo Zonse—Kodi Zimenezi ndi Zoona?

5 Mulungu Amavomereza Zipembedzo Zonse—Kodi Zimenezi ndi Zoona?

5 Mulungu Amavomereza Zipembedzo Zonse​—Kodi Zimenezi ndi Zoona?

Mwina munamvapo izi: “Pali njira zambiri zokafikira kwa Mulungu mofanana ndi mmene pamakhalira njira zambirimbiri zokafikira kumalo amodzi. Aliyense ayenera kusankha njira yake yokafikira kwa Mulungu.”

Zimene Baibulo limaphunzitsa: Tiyenera kulambira Mulungu mochokera pansi pa mtima ndipo tiyenera kupewa kulambira kwachinyengo kapena kongofuna kudzionetsera. Yesu anauza atsogoleri achipembedzo a m’nthawi yake chifukwa chimene Mulungu anawakanira. Iye anati: “Yesaya analosera moyenera za anthu onyenga inu, monga mmene Malemba amanenera kuti, ‘Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mitima yawo ili kutali ndi ine.’” (Maliko 7:6) Komabe, sikuti Mulungu amavomereza kulambira kulikonse kochokera pansi pa mtima.

Pofuna kumveketsa mfundo imeneyi, Yesu anafotokoza chinthu china chimene chinkachititsa kuti kulambira kwa atsogoleri amenewa komanso otsatira awo kukhale kopanda phindu. Iye anawauza kuti zimene ankachitazo zinali zofanana ndi zimene Mawu a Mulungu ananena, kuti: “[Anthu awa] amandipembedza pachabe, chifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu ngati ziphunzitso za Mulungu.” (Maliko 7:7) Anthu amenewa ankalambira “pachabe” kapena kuti kulambira kwawo kunali kopanda phindu chifukwa ankaika patsogolo miyambo ya chipembedzo chawo osati zimene Mulungu amafuna.

Baibulo siliphunzitsa kuti pali njira zambirimbiri zovomerezeka zolambirira Mulungu, koma limaphunzitsa kuti pali njira imodzi yokha. Lemba la Mateyu 7:13, 14 limati: “Lowani pachipata chopapatiza. Pakuti msewu waukulu ndi wotakasuka ukupita kuchiwonongeko, ndipo anthu ambiri akuyenda mmenemo. Koma chipata cholowera ku moyo n’chopapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi owerengeka.”

Kodi kudziwa zoona pa nkhaniyi kungakuthandizeni bwanji? Taganizirani mmene mungamvere mutakonzekera mpikisano wothamanga kwa miyezi yambiri ndipo pa tsiku la mpikisanowo mwakhala nambala wani koma n’kuuzidwa kuti simulandira mphoto chifukwa mwaphwanya lamulo lina la mpikisanowo mosadziwa. Mosakayikira mungaone kuti mwangowononga mphamvu zanu pachabe. Zofanana ndi zimenezi zingachitikenso pa nkhani ya kulambira Mulungu.

Mtumwi Paulo anayerekezera kulambira kwathu ndi mpikisano wothamanga. Iye analemba kuti: “Ngati munthu akuchita nawo mpikisano ngakhale pa masewera, savekedwa nkhata yaulemerero kumutu akapanda kupikisana nawo motsatira malamulo.” (2 Timoteyo 2:5) Kuti Mulungu avomereze kulambira kwathu, tiyenera kumulambira “motsatira malamulo,” kapena kuti m’njira imene iyeyo amavomereza. Anthufe sitingasankhe tokha njira yolambirira Mulungu ndipo zimenezi ndi zofanana ndi zimene zimachitika pa mpikisano wothamanga. Munthu sangasankhe yekha njira imene akufuna kudzera n’kumayembekezera kuti alandira mphoto.

Kuti Mulungu azisangalala ndi kulambira kwathu, sitiyenera kukhulupirira bodza lililonse limene anthu amanena lokhudza iyeyo. Yesu anati: “Olambira oona adzalambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi.” (Yohane 4:23) Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, ndi limene limatiphunzitsa njira yolondola yofikira kwa Mulungu.​—Yohane 17:17. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Kuti mudziwe zambiri zokhudza kulambira kumene Mulungu amavomereza, werengani mutu 15 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Kodi zipembedzo zonse zimaphunzitsa anthu kulambira Mulungu m’njira imene Mulunguyo amavomereza?