“Anthu Olimba Mtima Ofunika Kuwayamikira”
“Anthu Olimba Mtima Ofunika Kuwayamikira”
PA NTHAWI ya ulamuliro wake wankhanza, Adolf Hitler, yemwe anali mtsogoleri wa dziko la Germany, analandira makalata ambirimbiri. Mu 1945, boma la Russia litatenga dera lozungulira mzinda wa Berlin, ambiri mwa makalata amenewa anakawasunga ku Moscow. Katswiri wina wa mbiri yakale, dzina lake Henrik Eberle, anawerenga ambiri mwa makalata amene akusungidwa ku Moscow amenewa. Iye anachita zimenezi n’cholinga choti adziwe anthu amene analembera makalata Hitler komanso chifukwa chimene analembera makalatawo. Eberle analemba zimene anapeza m’buku lakuti, Makalata Opita Kwa Hitler (Briefe an Hitler).
Dr. Eberle analemba kuti: “Anthu ambiri analembera Hitler makalata, kuphatikizapo aphunzitsi ndi ana asukulu, masisitere ndi ansembe, anthu omwe sanali pa ntchito ndi akuluakulu amabizinezi komanso akuluakulu a asilikali ndi asilikali wamba. Anthu ena ankamupatsa ulemu kwambiri ndipo ankamuona ngati Mesiya wobadwanso mwatsopano, pamene ena ankamuona kuti ndi munthu woipa kwambiri amene ankayambitsa mavuto.” Kodi Hitler analandira makalata alionse ochokera kwa akuluakulu a chipembedzo omudzudzula chifukwa cha nkhanza zimene chipani cha Nazi chinkachita? Inde, koma panali makalata ochepa okha ochokera kwa anthu amenewa ndipo ankalembedwa patalipatali kwambiri.
Mosiyana ndi makalata ochokera kwa anthu amenewa, Eberle anapeza makalata ambirimbiri amene a Mboni za Yehova a m’madera osiyanasiyana ku Germany analembera Hitler. Makalatawa ankadzudzula khalidwe loipa la chipani cha Nazi. Ndipotu a Mboni ochokera m’mayiko pafupifupi 50 analemba makalata komanso matelegalamu pafupifupi 20,000 odzudzula nkhanza zimene a Mboni za Yehova ankachitiridwa. A Mboni masauzande ambiri anatsekeredwa m’ndende ndipo ena ambiri ananyongedwa kapena anafa chifukwa chochitiridwa nkhanza ndi chipani cha Nazi. Dr. Eberle anamaliza n’kunena kuti: “Tikaganizira kuchuluka kwa anthu amene anazunzidwa ndi chipani cha Nazi, chiwerengero chimenechi [cha a Mboni omwe anazunzidwa] chingaoneke chochepa. Komabe anthu amenewa anazunzidwa chifukwa chakuti anali ogwirizana ndipo molimba mtima anakanitsitsa kutsatira mfundo za chipani chimenechi ndipo tifunika kuwayamikira.”