Kudziwa Zoona Kungasinthe Moyo Wanu
Kudziwa Zoona Kungasinthe Moyo Wanu
N’KUTHEKA kuti munamvapo kapena munaphunzitsidwapo imodzi mwa mfundo zabodza zokhudza Mulungu zimene zatchulidwa m’nkhani zino. Komabe mwina zingakuvuteni kusintha zimene mumakhulupirira makamaka ngati mwazikhulupirira kwa nthawi yaitali.
Zimenezi zingakhale zomveka. Matchalitchi ena amaletsa anthu awo kuyerekezera ziphunzitso za tchalitchi chawo ndi zimene Baibulo limanena. Ena amaikira kumbuyo ziphunzitso zawo zabodza ponena kuti Baibulo ndi nkhalango ndipo munthu wamba sangalimvetse. Komatu ambiri mwa ophunzira a Yesu anali anthu wamba, osaphunzira kwambiri, koma ankamvetsa mosavuta zimene Yesu ankaphunzitsa.—Machitidwe 4:13.
Mwinanso mungamalephere kufufuza bwinobwino zimene mumakhulupirira poopa kuti kuchita zimenezi kungasonyeze kuti chikhulupiriro chanu ndi chochepa. Baibulo lili ndi uthenga wa Mulungu wopita kwa anthu. Ndiye kodi zingakhale zomveka kuti Mulungu angakhumudwe ngati mukuphunzira Baibulo mwakhama n’cholinga choti mudziwe zimene iyeyo amafuna kuti muzichita? Mosiyana ndi maganizo amenewa, Mawu ake amatilimbikitsa kufufuza patokha zimene Malemba amanena. Baibulo limati: ‘Muyenera kuzindikira chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.’—Aroma 12:2.
Kuphunzira zoona zokhudza Mulungu si nkhani yongodziwa zinthu zambiri zokhudza Mulungu. M’malomwake kuphunzira kumeneku kungakuthandizeni kwambiri. (Yohane 8:32) Deanne, yemwe tamutchula m’nkhani yoyamba ija, panopa amakhulupirira kwambiri Mawu a Mulungu. Iye anati: “Nditayamba kuphunzira Baibulo, m’pamene ndinazindikira kuti Malemba ndi osavuta kuwamvetsa. Tsopano ndimaona kuti Yehova ndi Atate wanga wakumwamba ndipo amandikonda. Ndimaonanso kuti moyo wanga panopa ndi waphindu.”
Mwina munaphunzirapo Baibulo m’mbuyomu koma simunaone phindu lake. Ngati zili choncho, musataye mtima. Kuyesetsa kuti mumvetse Baibulo koma mutaphunzitsidwa zinthu zabodza zokhudza Mulungu, kungafanane ndi kuyesa kulumikiza makina atsopano koma mukutsatira buku lamalangizo lolakwika. Mukhoza kulumikiza zitsulo zina molondola koma kenako n’kugwa ulesi polephera kulumikiza zitsulo zotsala chifukwa choti sizikugwirizana ndi zimene alemba m’bukumo. Choncho, kuti mulumikize makinawo bwinobwino, muyenera kugwiritsa ntchito buku lamalangizo lolondola.
Kodi mukufuna kudziwa zolondola zokhudza Mulungu? Lankhulani ndi a Mboni za Yehova a m’dera lanu, kapena lembani kalata ku adiresi yoyenera patsamba 4 la magazini ino, kuti wina adzayambe kuphunzira nanu Baibulo kwaulere.
[Mawu Otsindika patsamba 9]
‘Muyenera kuzindikira chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.’—AROMA 12:2.