Baibulo Limasintha Anthu
Baibulo Limasintha Anthu
N’CHIYANI chinachititsa bambo wina amene ankakonda kwambiri kutchova juga ndiponso kuba pothyola nyumba za anthu kuti asiye khalidwe lakeli? Werengani nkhaniyi kuti mumve zimene iye ananena.
“Ndinkakonda kwambiri mpikisano wa mahatchi.”—RICHARD STEWART
CHAKA CHOBADWA: 1965
DZIKO: JAMAICA
POYAMBA: NDINKAKONDA KUTCHOVA JUGA KOMANSO KUBA POTHYOLA NYUMBA ZA ANTHU
KALE LANGA: Ndinakulira m’dera lina lomwe lili ndi anthu ambiri mumzinda wa Kingston, likulu la dziko la Jamaica. Anthu a m’derali anali osauka ndipo ambiri sanali pa ntchito. Pa nthawiyi, umbava unali wofala moti anthu ankakhala mwamantha chifukwa cha magulu achifwamba. Pafupifupi tsiku lililonse ndinkamva kulira kwa mfuti.
Amayi anga ankagwira ntchito mwakhama kwambiri kuti azisamalira ineyo, mng’ono wanga ndiponso mchemwali wanga. Ankayesetsa kuti tidzakhale anthu ophunzira. Ineyo sindinkakonda sukulu kwenikweni, koma mpikisano wa mahatchi. Masiku ena ndinkajomba kusukulu n’kupita kukaonera mpikisanowo ndipo nthawi zina ndinkapeza mwayi wokwera nawo mahatchi.
Pasanapite nthawi yaitali, ndinayamba kumabetcherana ndi anzanga za mahatchi amene angawine. Ndinayamba kusuta chamba komanso kuchita chiwerewere ndipo ndinkagona ndi akazi ambiri. Kuti ndizipeza ndalama zochitira zimenezi, ndinayamba kuba. Ndinali ndi mfuti zambiri, koma panopa ndimayamikira kuti palibe munthu amene anaphedwa pa maulendo onse amene ineyo ndinapita nawo kokaba.
Kenako, apolisi anandigwira n’kukanditsekera m’ndende chifukwa cha milandu imene ndinapalamula. Nditatuluka kundendeko ndinayambiranso khalidwe langa loipa lija ndipo zimene ndinkachita pa nthawiyi zinali zoipa kuposa poyamba. Ngakhale kuti pamaso ndinkaoneka ngati munthu wabwino, ndinali womva zake zokha, wosachedwa kukwiya komanso woipa mtima. Sindinkasamala za munthu, ndinkangopanga zoti zanga ziyende basi.
MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Pa nthawi imeneyi, mayi anga anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anakhala a Mboni za Yehova. Ndinachita chidwi kwambiri kuona mmene iwo anasinthira. Ndinaganiza zofufuza kuti ndidziwe zimene zachititsa kuti asinthe choncho. Motero, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.
Ndinazindikira kuti zimene a Mboni za Yehova amaphunzitsa ndi zosiyana ndi zimene zipembedzo zina zimaphunzitsa. Ndinazindikiranso kuti mfundo zonse zimene iwo amanena, amazitenga m’Baibulo. Komanso ndinaona kuti a Mboni za Yehova okha ndi amene ankalalikira kunyumba ndi nyumba ngati mmene ankachitira Akhristu oyambirira. (Mateyu 28:19; Machitidwe 20:20) Nditaona chikondi chenicheni chimene anthu amenewa amasonyezana, ndinatsimikiza kuti ndapeza chipembedzo choona.—Yohane 13:35.
Zimene ndinkaphunzira m’Baibulo zinandichititsa kuona kuti ndikufunika kusintha zinthu zambiri pa moyo wanga. Ndinazindikira kuti Yehova Mulungu amadana ndi dama ndipo kuti ndimusangalatse 2 Akorinto 7:1; Aheberi 13:4) Ndinadziwa kuti zochita zanga zingathe kukhumudwitsa Yehova kapena kumusangalatsa ndipo zimenezi zinandikhudza kwambiri. (Miyambo 27:11) Choncho ndinatsimikiza zosiya kusuta chamba komanso kusunga mfuti. Ndinatsimikizanso zoti ndisinthe makhalidwe anga oipa. Ena mwa makhalidwe amene anandivuta kwambiri kusintha ndi chiwerewere ndi kutchova juga.
ndiyenera kusiya makhalidwe onse amene amaipitsa thupi. (Poyamba sindinkafuna kuti anzanga adziwe zoti ndikuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Koma ndinasintha maganizo nditawerenga mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 10:33. Lembali limati: “Aliyense wondikana ine pamaso pa anthu, inenso ndidzamukana pamaso pa Atate wanga wakumwamba.” Mawu amenewa anandipangitsa kuti ndiuze anzanga zoti ndikuphunzira Baibulo ndi a Mboni. Iwo anadabwa kwambiri atamva zimenezi. Sanakhulupirire zoti munthu ngati ine angafune kukhala Mkhristu. Koma ndinawauza kuti ndikufuna kusiya zonse zomwe ndinkachita poyamba.
PHINDU LIMENE NDAPEZA: Mayi anga anasangalala kwambiri ataona kuti ndayamba kutsatira mfundo za m’Baibulo. Panopa sadandaulanso zoti mwina ndichita zinthu zoipa. Komanso tsopano ndife ogwirizana kwambiri chifukwa tonse timakonda Yehova. Nthawi zina ndimakumbukira zimene ndinkachita poyamba ndipo ndimaona kuti Mulungu anandithandiza kwambiri kuti ndisinthe. Panopa sindilakalakanso moyo wachiwerewere komanso wokondetsa chuma umene ndinali nawo poyamba.
Ndikanakhala kuti sindinayambe kutsatira mfundo za m’Baibulo, pano ndikanakhala nditafa kapena ndili kundende. Panopa ndili ndi banja labwino komanso losangalala. Ndikusangalala kwambiri kutumikira Yehova Mulungu limodzi ndi mkazi wanga, yemwe amandithandiza, komanso mwana wathu wamkazi. Ndikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa chondilola kukhala m’gulu la abale ndi alongo omwe amakondana kwambiri. Ndikuyamikira kwambiri kuti munthu wina anachita khama kundiphunzitsa choonadi cha m’Baibulo. Ndikuona kuti mwayi umene ndili nawo wophunzitsa ena Baibulo ndi wamtengo wapatali. Komanso ndikuthokoza kwambiri Yehova Mulungu chifukwa cha kukoma mtima kwake pondikokera kwa iye.
[Mawu Otsindika patsamba 11]
“Ndinadziwa kuti zochita zanga zingathe kukhumudwitsa Yehova kapena kumusangalatsa”
[Chithunzi patsamba 11]
Ndili ndi mkazi wanga ndi mwana wathu wamkazi
[Chithunzi patsamba 11]
Ndinaona kuti mayi anga anasintha kwambiri