Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Malamulo a Mulungu Amatithandiza Bwanji?

Kodi Malamulo a Mulungu Amatithandiza Bwanji?

Phunzirani Zimene Mawu A Mulungu Amanena

Kodi Malamulo a Mulungu Amatithandiza Bwanji?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kumvera Mulungu?

Tiyenera kumvera Mulungu chifukwa iyeyo ndi amene anatilenga. Ngakhalenso Yesu ankamvera Mulungu nthawi zonse. (Yohane 6:38; Chivumbulutso 4:11) Tikamatsatira malamulo a Mulungu pa moyo wathu, timasonyeza kuti timamukonda.​—Werengani 1 Yohane 5:3.

Malamulo onse a Yehova Mulungu ndi opindulitsa. Amatithandiza kukhala ndi moyo wabwino panopa komanso amatiphunzitsa zoyenera kuchita kuti tidzapeze madalitso osatha m’tsogolo.​—Werengani Salimo 19:7, 11; Yesaya 48:17, 18.

2. Kodi kutsatira Malamulo a Mulungu kumatithandiza bwanji kukhala ndi thanzi labwino?

Lamulo la Mulungu loletsa kuledzera limatiteteza kuti tisadwale matenda oopsa komanso limatithandiza kupewa ngozi. Munthu wokonda kumwa mowa mwauchidakwa amafika poti zimakhala zovuta kuti asiye khalidweli ndipo amachita zinthu zambiri zopanda nzeru. (Miyambo 23:20, 29, 30) Yehova amatilola kumwa mowa koma osati mpaka kuledzera.​—Werengani Salimo 104:15; 1 Akorinto 6:10.

Yehova amatichenjezanso za kuipa kochita nsanje, kukwiya kwambiri komanso makhalidwe ena oipa amene angatibweretsere mavuto. Tikamatsatira kwambiri malangizo ake pa nkhani zimenezi, m’pamenenso timakhala ndi thanzi labwino.​—Werengani Miyambo 14:30; 22:24, 25.

3. Kodi malamulo a Mulungu angatiteteze bwanji?

Mulungu amaletsa kugonana ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi wako. (Aheberi 13:4) Anthu okwatirana amene amatsatira lamulo limeneli amakhala otetezeka ndiponso banja lawo limakhala malo abwino olerera ana. Koma anthu amene amagonana ndi munthu woti si mkazi kapena mwamuna wawo, nthawi zambiri zotsatira zake zimakhala matenda, kutha kwa banja, chiwawa, kuvutika maganizo komanso ana amaleredwa ndi bambo kapena mayi wokha.​—Werengani Miyambo 5:1-9.

Tikamapewa kuchita zinthu kapena kukhala pamalo amene angachititse kuti tigonane ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wathu, timakhala tikutetezera ubwenzi wathu ndi Mulungu. Tikamachita zimenezi timapewanso kubweretsa mavuto kwa anthu ena.​—Werengani 1 Atesalonika 4:3-6.

4. Kodi timapindula bwanji chifukwa choona kuti moyo ndi wamtengo wapatali?

Anthu amene ankasuta fodya komanso kuchita makhalidwe ena owononga moyo, amakhala ndi thanzi labwino akasiya makhalidwe amenewa chifukwa choona kuti moyo ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu. (2 Akorinto 7:1) Mulungu amaonanso kuti moyo wa mwana wosabadwa ndi wamtengo wapatali. (Ekisodo 21:22, 23) Choncho sitiyenera kupha mwadala mwana wosabadwa. Anthu amene amaona moyo ngati mmene Mulungu amauonera, amapewa ngozi akakhala kuntchito, kunyumba ndiponso m’galimoto. (Deuteronomo 22:8) Kuwonjezera pamenepo, iwo sachita masewera oika moyo pachiswe chifukwa amadziwa kuti moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.​—Werengani Salimo 36:9.

5. Kodi kupatulika kwa magazi kumatipindulitsa bwanji?

Magazi ndi opatulika chifukwa Mulungu amanena kuti amaimira moyo wa chinthu. (Genesis 9:3, 4) Lamulo la Mulungu limene limasonyeza kuti magazi ndi ofanana ndi moyo limatipindulitsa. Tikutero chifukwa lamulo limeneli limachititsa kuti machimo athu azikhululukidwa.​—Werengani Levitiko 17:11-13; Aheberi 9:22.

Magazi a Yesu anali amtengo wapatali kwambiri chifukwa iye anali wangwiro. Yesu anapereka magazi ake kwa Mulungu ndipo magaziwo anaimira moyo wake. (Aheberi 9:12) Magazi amene iye anakhetsa amachititsa kuti zikhale zotheka kuti anthu adzakhale ndi moyo wosatha.​—Werengani Mateyu 26:28; Yohane 3:16.

Kuti mudziwe zambiri werengani mutu 12 ndi 13 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.