Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukwaniritsa Udindo Wathu kwa Mulungu

Kukwaniritsa Udindo Wathu kwa Mulungu

Yandikirani Mulungu

Kukwaniritsa Udindo Wathu kwa Mulungu

KODI munayamba mwadzifunsapo kuti cholinga cha moyo n’chiyani? Yehova anatipatsa nzeru zoti titha kufunsa funso limeneli komanso chikhumbo chofuna kudziwa yankho lake. Mulungu wathu wachikondi watipatsanso zonse zimene zingatithandize kupeza yankho la funsoli. Yankho la funso limeneli lili m’Mawu ake, Baibulo. Tiyeni tikambirane mawu a Mfumu Solomo opezeka palemba la Mlaliki 12:13.

Solomo anali woyenereradi kufotokoza zimene munthu angachite kuti akhale wosangalala pa moyo wake. Iye anadalitsidwa ndi nzeru, chuma chochuluka komanso ufumu ndipo izi zinathandiza kuti athe kufufuza bwino zimene anthu ambiri amafuna, kuphatikizapo chuma ndi kutchuka. (Mlaliki 2:4-9; 4:4) Ndiyeno mouziridwa ndi Mulungu, iye ananena zimene anapeza pa kufufuza kwakeko. Iye anati: “Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake chifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenera kuchita.” Mawu amenewa akufotokoza chinthu chofunika kwambiri chimene anthufe tiyenera kuchita.

“Opa Mulungu woona.” Poyamba, mfundo yakuti tiziopa Mulungu singaoneke yosangalatsa. Koma mantha amenewa ndi oyenera. Kuopa kwake si ngati kwa wantchito amene amakhala ndi mantha chifukwa cha bwana wake wovuta koma kwa mwana amene amaopa kukhumudwitsa bambo ake chifukwa chowakonda. Buku lina linanena kuti kuopa Mulungu kumatanthauza “ulemu waukulu umene anthu Ake amamusonyeza chifukwa chakuti amamukonda, komanso chifukwa chakuti amaona kuti Iye ngwamphamvu ndiponso wolemekezeka.” Mantha amenewa amatipangitsa kuti tizimvera Mulungu chifukwa chomukonda komanso chodziwa kuti iye amatikonda. Komabe sikuti munthu amangomva mumtima mwake kuti ali ndi mantha oyenera amenewa. Zochita zake ziyenera kusonyeza zimenezi. Kodi zochita zathu zingasonyeze bwanji kuti tili ndi mantha amenewa?

‘Tizisunga malamulo ake.’ Kuopa Mulungu kumatipangitsa kuti tizimumvera ndipo pali zifukwa zomveka zotipangitsa kumvera Yehova. Wopanga chinthu ndi amene amadziwa njira yoyenera yogwiritsira ntchito chinthucho. Mofanana ndi zimenezi, Mulungu, yemwe ndi Mlengi wathu, amadziwa zimene tiyenera kuchita kuti tikhale ndi moyo wabwino. Komanso Yehova amatifunira zabwino. Iye amafuna kuti tizikhala osangalala ndipo amatipatsa malamulo n’cholinga chakuti zinthu zitiyendere bwino. (Yesaya 48:17) Mtumwi Yohane anafotokoza mfundo imeneyi motere: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.” (1 Yohane 5:3) Choncho tikamamvera Mulungu timasonyeza kuti timamukonda ndipo malamulo ake amasonyeza kuti iyenso amatikonda.

“Zimenezi ndiye zimene munthu ayenera kuchita.” Mawu amenewa akusonyeza kuti ndi udindo wathu kumvera Mulungu komanso kumuopa. Popeza Yehova ndiye Mlengi wathu, popanda iyeyo sitikanakhala ndi moyo. (Salimo 36:9) Choncho tiyenera kumumvera. Tikamachita zimene iye amafuna, timakhala tikukwaniritsa udindo wathu.

Ndiyeno kodi cholinga cha moyo n’chiyani? Mwachidule tinganene kuti: Tili ndi moyo kuti tizichita chifuniro cha Mulungu. Palibe chinthu china chimene chingatipangitse kukhala osangalala pa moyo wathu kuposa kuchita chifuniro cha Mulungu. Tikukupemphani kuti muphunzire zambiri zokhudza cholinga cha Yehova komanso zimene mungachite kuti muzichita zinthu zogwirizana ndi cholinga chakecho. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukuthandizani kuchita zimenezi.

Mavesi amene mungawerenge mu November:

Miyambo 22-31; Mlaliki 1-12 mpaka Nyimbo ya Solomo 1-8